Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 18:1-24

  • Kugwa kwa “Babulo Wamkulu” (1-8)

    • “Tulukani mwa iye anthu anga” (4)

  • Kulirira Babulo amene wagwa (9-19)

  • Kumwamba kudzakhala chisangalalo chifukwa cha kugwa kwa Babulo (20)

  • Babulo adzaponyedwa mʼnyanja ngati mwala (21-24)

18  Zimenezi zitatha, ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba ali ndi ulamuliro waukulu ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero wake.  Iye anafuula ndi mawu amphamvu akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo amene ziwanda zimakhala. Wakhalanso malo amene mzimu uliwonse wonyansa* komanso mbalame iliyonse yonyansa ndi imene imadedwa zimabisala.+  Iye wamwetsa mitundu yonse ya anthu vinyo wa chilakolako chake cha* chiwerewere.*+ Ndipo mafumu a dziko lapansi anachita naye chiwerewere.+ Amalonda* apadziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zambiri zamtengo wapatali zimene mkazi ameneyu anadziunjikira mopanda manyazi.”  Ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti: “Tulukani mwa iye anthu anga,+ ngati simukufuna kugawana naye machimo ake ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.+  Chifukwa machimo ake aunjikana mpaka kumwamba,+ ndipo Mulungu wakumbukira zochita zake zopanda chilungamo.*+  Mubwezereni zofanana ndi zimene iye anachitira ena.+ Mubwezereni kuwirikiza kawiri zinthu zimene iyeyo anachita.+ Mʼkapu+ imene anaikamo chakumwa chosakaniza, ikanimo chakumwa chakecho kuwirikiza kawiri.+  Pa muyezo umene anadzipezera ulemerero ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, pa muyezo womwewo mumuzunze ndi kumuliritsa. Chifukwa mumtima mwake akumanena kuti: ‘Ine ndine mfumukazi. Si ine mkazi wamasiye ndipo sindidzalira.’+  Nʼchifukwa chake mʼtsiku limodzi, miliri yake idzafika. Miliri yake ndi imfa, kulira komanso njala ndipo adzapserera ndi moto+ chifukwa Yehova* Mulungu, amene anamuweruza ndi wamphamvu.+  Mafumu a dziko lapansi amene anachita naye chiwerewere* nʼkumasangalala ndi chuma mopanda manyazi, adzalira ndi kudziguguda pachifuwa pomumvera chisoni, akadzaona utsi ukufuka chifukwa cha kupsa kwake. 10  Iwo adzaima patali chifukwa cha mantha poona mmene akuzunzikira ndipo adzanena kuti: ‘Zomvetsa chisoni! Zomvetsa chisoni! Iwe mzinda waukulu,+ iwe Babulo mzinda wamphamvu! Chifukwa mu ola limodzi lokha, chiweruzo chako chafika!’ 11  Komanso amalonda apadziko lapansi adzamulirira ndi kumva chisoni, chifukwa palibenso wina amene angawagule katundu wawo yense. 12  Katundu wawoyo ndi golide, siliva, miyala yamtengo wapatali, ngale, nsalu zabwino kwambiri, nsalu zapepo, nsalu zasilika ndi nsalu zofiira kwambiri. Palibe amene akuwagula chilichonse chopangidwa kuchokera ku mtengo wa fungo labwino, zinthu zosiyanasiyana zopangidwa ndi minyanga, mtengo wapamwamba, kopa, chitsulo ndi mwala wa mabo. 13  Komanso palibe amene akuwagula sinamoni, zonunkhiritsa zochokera ku Indiya, zofukiza, mafuta onunkhira, lubani, vinyo, mafuta a maolivi, ufa wabwino kwambiri, tirigu, ngʼombe, nkhosa, mahatchi, ngolo, akapolo ndiponso anthu ena.* 14  Zoonadi, chipatso chabwino chimene unkachilakalaka chija chakuchokera, ndipo zinthu zako zonse zabwino komanso zokongola zawonongeka ndipo anthu sadzazipezanso. 15  Amalonda amene ankagulitsa zinthu zimenezi, amene analemera chifukwa cha iye, adzaima patali chifukwa cha mantha poona mmene akuzunzikira ndipo adzamulirira ndi kumva chisoni. 16  Iwo azidzati: ‘Zomvetsa chisoni! Zomvetsa chisoni! Iwe mzinda waukulu, umene unkavala zovala zapamwamba, zapepo ndi zofiira kwambiri. Iwe mzinda umene unakongoletsedwa mochititsa chidwi ndi zodzikongoletsera zagolide, mwala wamtengo wapatali ndi ngale.+ 17  Zachisoni, chifukwa mu ola limodzi, chuma chochulukachi chawonongedwa!’ Woyendetsa ngalawa aliyense, munthu aliyense woyenda panyanja, ogwira ntchito mʼngalawa ndi anthu onse amene amayenda panyanja nʼkumachita malonda, anaima patali. 18  Ndipo ataona utsi umene unkafuka chifukwa cha kupsa kwake, anafuula kuti: ‘Ndi mzinda uti umene ungafanane ndi mzinda waukulu umenewu?’ 19  Iwo anathira fumbi pamitu pawo akufuula, kulira ndi kumva chisoni, ndipo anati: ‘Nʼzomvetsa chisoni kuti zimenezi zachitikira mzinda waukuluwu. Anthu onse amene anali ndi ngalawa panyanja analemera chifukwa cha chuma chake. Zatheka bwanji kuti mzindawu uwonongedwe mu ola limodzi.’+ 20  Sangalalani kumwambako chifukwa cha zimene zamuchitikira.+ Inunso oyera,+ atumwi ndi aneneri, sangalalani chifukwa Mulungu wamupatsa chilango chifukwa cha zomwe anakuchitirani.”+ 21  Ndiyeno mngelo wamphamvu ananyamula mwala wooneka ngati mphero yaikulu nʼkuuponya mʼnyanja, ndipo anati: “Mzinda waukulu wa Babulo udzaponyedwa pansi mofulumira ndi mwamphamvu chonchi, ndipo sudzapezekanso.+ 22  Kuimba kwa oimba pogwiritsa ntchito zeze, kwa oimba zitoliro, kwa oimba malipenga ndi kwa oimba ena sikudzamvekanso mwa iwe. Mwa iwe simudzapezekanso mmisiri wa ntchito iliyonse, komanso phokoso la mphero silidzamvekanso mwa iwe. 23  Kuwala kwa nyale sikudzaunikanso mwa iwe. Mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso mwa iwe, chifukwa amalonda ako anali anthu apamwamba padziko lapansi, ndiponso mitundu yonse ya anthu inasocheretsedwa ndi zochita zako zamizimu.+ 24  Mwa iye munapezeka magazi a aneneri, a oyera,+ ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “mpweya; mawu ouziridwa.”
Kapena kuti, “mkwiyo wake wa.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “Amalonda oyendayenda.”
Kapena kuti, “milandu yake.”
Kapena kuti, “miyoyo ya anthu.”