Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 2:1-29

  • Mauthenga opita ku Efeso (1-7), ku Simuna (8-11), ku Pegamo (12-17), ku Tiyatira (18-29)

2  “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Efeso+ lemba kuti: Izi ndi zimene akunena wonyamula nyenyezi 7 mʼdzanja lake lamanja, amene akuyenda pakati pa zoikapo nyale 7 zagolide:+  ‘Ndikudziwa ntchito zako, khama lako ndi kupirira kwako ndiponso kuti sungalekelere anthu oipa. Ndikudziwanso kuti unayesa anthu amene ankati ndi atumwi+ pamene sanali atumwi, ndipo unapeza kuti ndi abodza.  Ukuonetsanso kupirira ndipo walimbana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha dzina langa,+ koma sunafooke.+  Komabe, ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya kusonyeza chikondi ngati mmene unkachitira poyamba.  Choncho, kumbukira malo amene unali usanagwe ndipo ulape+ ndi kuchita ntchito zimene unkachita poyamba. Ngati suchita zimenezi, ndibwera kwa iwe ndipo ndidzachotsa choikapo nyale chako+ pamalo ake ngati sulapa.+  Komabe, pali chinthu chimodzi chimene ukuchita bwino: Umadana ndi zochita za mpatuko wa Nikolao,+ zimenenso ine ndimadana nazo.  Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti:+ Amene wapambana pankhondo,+ ndidzamulola kudya zipatso zamumtengo wa moyo+ umene uli mʼparadaiso wa Mulungu.’  Kwa mngelo wa mpingo wa ku Simuna lemba kuti: Izi ndi zimene akunena ‘Woyamba ndi Womaliza,’+ amene anafa nʼkukhalanso ndi moyo:+  ‘Ndikudziwa masautso ako ndi umphawi wako, koma ndiwe wolemera.+ Ndikudziwanso kuti pali anthu amene amanena kuti ndi Ayuda ndipo amakunyoza. Koma sikuti iwo ndi Ayuda, mʼmalomwake iwo ndi sunagoge wa Satana.+ 10  Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo.+ Taona! Mdyerekezi apitiriza kuponya mʼndende ena a inu kuti muyesedwe mpaka pamapeto, ndipo mudzakhala mʼmasautso kwa masiku 10. Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa ndipo ndidzakupatsa mphoto* ya moyo.+ 11  Amene ali ndi makutu amve+ zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti: Amene wapambana pankhondo+ sadzakhudzidwa ndi imfa yachiwiri.’+ 12  Kwa mngelo wa mpingo wa ku Pegamo lemba kuti: Izi ndi zimene akunena amene ali ndi lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse:+ 13  ‘Ndikudziwa kumene ukukhala. Ukukhala kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Koma ukugwirabe mwamphamvu dzina langa+ ndipo sunakane kuti umandikhulupirira.+ Sunakane ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika,+ amene anaphedwa+ mumzinda wanu, kumene Satana akukhala. 14  Ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo. Iwe kumeneko uli ndi anthu amene akupitiriza kutsatira chiphunzitso cha Balamu,+ amene anaphunzitsa Balaki+ kuti aikire ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita chiwerewere.*+ 15  Kuwonjezera pamenepo, ulinso ndi anthu amene akupitiriza kutsatira chiphunzitso cha mpatuko wa Nikolao.+ 16  Choncho ulape. Ngati sulapa, ndibwera kwa iwe mwamsanga, ndipo ndidzamenyana nawo ndi lupanga lalitali lamʼkamwa mwanga.+ 17  Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti:+ Amene wapambana pankhondo+ ndidzamupatsa ena mwa mana obisika+ komanso ndidzamupatsa mwala woyera. Pamwala woyerawo panalembedwa dzina latsopano limene wina aliyense sakulidziwa kupatulapo wolandira yekhayo.’ 18  Kwa mngelo wa mpingo wa ku Tiyatira+ lemba kuti: Izi ndi zimene Mwana wa Mulungu akunena, iye amene maso ake ali ngati lawi la moto+ ndipo mapazi ake ali ngati kopa* woyengedwa bwino:+ 19  ‘Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako komanso kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zapanopa nʼzambiri kuposa zimene unkachita poyamba. 20  Komabe, ndakupeza ndi mlandu wakuti ukulekerera mayi uja Yezebeli,+ amene amadziona ngati mneneri. Iye akuphunzitsa ndi kusocheretsa akapolo anga kuti azichita chiwerewere*+ komanso kuti azidya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano. 21  Ndamupatsa nthawi kuti alape, koma sakufuna kulapa chiwerewere* chakecho. 22  Taona! Ndatsala pangʼono kumudwalitsa kwambiri, ndipo amene akuchita naye chigololo ndiwabweretsera masautso aakulu, kupatulapo ngati atalapa ntchito zawo zofanana ndi za mayiyo. 23  Ana ake ndidzawapha ndi mliri woopsa, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ine ndi amene ndimafufuza maganizo* komanso mitima, ndipo aliyense payekha ndidzamubwezera mogwirizana ndi ntchito zake.+ 24  Komabe, ena nonse amene muli ku Tiyatira, nonsenu amene simutsatira chiphunzitso chimenechi, amene simukudziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene amati ndi “zinthu zozama za Satana,”+ ndikukuuzani kuti: Sindikusenzetsani katundu aliyense wolemera. 25  Mʼmalomwake gwirani mwamphamvu zinthu zabwino zimene muli nazo mpaka nditabwera.+ 26  Ndipo amene wapambana pankhondo nʼkumatsatira ntchito zanga mpaka mapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu.+ 27  Ulamuliro wake udzakhala wofanana ndi umene ine ndalandira kuchokera kwa Atate wanga. Iye adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo+ moti anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi. 28  Ndipo ndidzamupatsa nthanda.*+ 29  Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “ndimafufuza mmene munthu akumvera mumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso.”
“Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pangʼono kutuluka.