Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 6:1-17

  • Mwanawankhosa anamatula zidindo 6 zoyambirira (1-17)

    • Wogonjetsa adani anakwera pahatchi yoyera (1, 2)

    • Amene anakwera pahatchi yofiira ngati moto analoledwa kuchotsa mtendere (3, 4)

    • Amene anakwera pahatchi yakuda anabweretsa njala (5, 6)

    • Amene anakwera pahatchi yotuwa dzina lake ndi Imfa (7, 8)

    • Pansi pa guwa lansembe panali anthu amene anaphedwa (9-11)

    • Chivomerezi chachikulu (12-17)

6  Ndinaona Mwanawankhosa+ akumatula chidindo chimodzi mwa zidindo 7 zija,+ ndipo ndinamva mngelo mmodzi mwa angelo 4 aja+ akulankhula ndi mawu omveka ngati kugunda kwa bingu kuti: “Bwera!”  Nditayangʼana, ndinaona hatchi yoyera+ ndipo amene anakwera pahatchiyi ananyamula uta. Iye anapatsidwa chisoti chachifumu+ nʼkupita kukagonjetsa adani ake ndipo anapambana pankhondo yolimbana nawo.+  Atamatula chidindo chachiwiri, ndinamva mngelo wachiwiri+ akunena kuti: “Bwera!”  Panatuluka hatchi ina yofiira ngati moto. Amene anakwera pahatchi imeneyi analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi, kuti anthu aphane ndipo anapatsidwa lupanga lalikulu.+  Atamatula chidindo chachitatu,+ ndinamva mngelo wachitatu+ akunena kuti: “Bwera!” Ndipo nditayangʼana, ndinaona hatchi yakuda. Amene anakwera pahatchiyo anali ndi sikelo mʼdzanja lake.  Kenako ndinamva ngati wina akulankhula kuchokera pakati pa angelo 4 aja kuti: “Kilogalamu imodzi* ya tirigu, mtengo wake ukhala dinari* imodzi,+ ndipo makilogalamu atatu a balere, mtengo wake ukhala dinari imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.”+  Atamatula chidindo cha 4, ndinamva mawu a mngelo wa 4+ akunena kuti: “Bwera!”  Nditayangʼana, ndinaona hatchi yotuwa. Amene anakwera pahatchiyi dzina lake anali Imfa. Ndipo Manda* ankamutsatira pafupi kwambiri. Iwo anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo 4 adziko lapansi, kuti aphe anthu ndi lupanga lalitali, njala,+ mliri woopsa komanso zilombo zapadziko lapansi.+  Atamatula chidindo cha 5, ndinaona pansi pa guwa lansembe+ pali miyoyo*+ ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu ndiponso chifukwa cha ntchito yochitira umboni.+ 10  Iwo anafuula ndi mawu okweza akuti: “Mudzalekerera mpaka liti, inu Ambuye Wamkulu Koposa, Mulungu woyera ndi woona,+ osaweruza ndi kubwezera okhala padziko lapansi chifukwa cha magazi athu?”+ 11  Aliyense wa iwo anapatsidwa mkanjo woyera+ ndipo anauzidwa kuti apumulebe kanthawi pangʼono, mpaka chiwerengero cha akapolo anzawo chitakwanira, inde chiwerengero cha abale awo amene anali atatsala pangʼono kuphedwa ngati mmenenso iwowo anaphedwera.+ 12  Atamatula chidindo cha 6, ndinaona kuti kunachitika chivomerezi chachikulu. Dzuwa linada ngati chiguduli choluka ndi ubweya* ndipo mwezi wonse unafiira ngati magazi.+ 13  Nyenyezi zakumwamba zinagwera padziko lapansi ngati mmene mtengo wa mkuyu umene ukugwedezeka ndi mphepo yamphamvu umagwetsera nkhuyu zake zosapsa. 14  Ndipo kumwamba kunachoka ngati mpukutu umene akuupinda,+ ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa pamalo ake.+ 15  Kenako mafumu apadziko lapansi, nduna, akuluakulu a asilikali, olemera, amphamvu, kapolo aliyense ndi munthu aliyense amene ndi mfulu, anabisala mʼmapanga ndi mʼmatanthwe amʼmapiri.+ 16  Iwo ankauza mapiri ndi matanthwe kuti: “Tigwereni,+ tibiseni kuti tisaonekere kwa Mulungu amene wakhala pampando wachifumu+ ndiponso kuti mkwiyo wa Mwanawankhosa usatigwere,+ 17  chifukwa tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika,+ ndipo ndi ndani amene angaimirire pamaso pawo?”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kwati imodzi.” Onani Zakumapeto B14.
Imeneyi ndi ndalama ya siliva ya Aroma ndipo inali malipiro antchito imene munthu wagwira tsiku limodzi. Onani Zakumapeto B14.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Nʼkutheka kuti apa akunena za magazi amene anathiridwa paguwa lansembe. Magazi amenewa akuimira moyo.
Nʼkutheka kuti akunena ubweya wa mbuzi.