Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 7:1-17

  • Angelo 4 anagwira mphepo kuti zisawononge (1-3)

  • Anthu okwana 144,000 anaikidwa chidindo (4-8)

  • Khamu lalikulu limene lavala mikanjo yoyera (9-17)

7  Zimenezi zitatha, ndinaona angelo 4 ataimirira mʼmakona 4 a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo 4 za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi, panyanja kapena pamtengo uliwonse.  Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa,* ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuula mokweza mawu kwa angelo 4, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja aja,  kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, mpaka titadinda chidindo+ pazipumi za akapolo a Mulungu wathu.”+  Ndiyeno ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000,+ ochokera mʼfuko lililonse la ana a Isiraeli, anadindidwa chidindo:+  Mu fuko la Yuda, anadindamo anthu 12,000.Mu fuko la Rubeni, 12,000.Mu fuko la Gadi, 12,000.  Mu fuko la Aseri, 12,000.Mu fuko la Nafitali, 12,000.Mu fuko la Manase,+ 12,000.  Mu fuko la Simiyoni, 12,000.Mu fuko la Levi, 12,000.Mu fuko la Isakara, 12,000.  Mu fuko la Zebuloni, 12,000.Mu fuko la Yosefe, 12,000.Ndipo mu fuko la Benjamini, anadindamo anthu 12,000.  Zimenezi zitatha, nditayangʼana ndinaona khamu lalikulu la anthu, amene palibe munthu aliyense amene anatha kuwawerenga, ochokera mʼdziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chilankhulo chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.+ 10  Iwo anapitiriza kufuula ndi mawu okweza akuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu,+ ndi kwa Mwanawankhosa.”+ 11  Angelo onse anali ataima kuzungulira mpando wachifumu, akulu+ komanso angelo 4 aja. Ndipo onse anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi, pamaso pa mpando wachifumuwo ndi kulambira Mulungu. 12  Iwo ankanena kuti: “Ame! Mulungu wathu ndi amene ali ndi nzeru, mphamvu komanso nyonga ndipo ndi amene akuyenera kutamandidwa, kupatsidwa ulemerero ndi ulemu komanso kuyamikiridwa mpaka kalekale.+ Ame.” 13  Ndiyeno mmodzi wa akulu aja anandifunsa kuti: “Kodi amene avala mikanjo yoyerawa+ ndi ndani ndipo achokera kuti?” 14  Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: “Mbuyanga, mukudziwa ndinu.” Ndipo iye anandiuza kuti: “Amenewa ndi amene atuluka mʼchisautso chachikulu+ ndipo achapa mikanjo yawo nʼkuiyeretsa mʼmagazi a Mwanawankhosa.+ 15  Nʼchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika usana ndi usiku mʼkachisi wake, ndipo Amene wakhala pampando wachifumuyo+ adzawaphimba ndi tenti yake kuti awateteze.+ 16  Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha,+ 17  chifukwa Mwanawankhosa,+ amene ali pambali* pa mpando wachifumu, adzawaweta+ nʼkuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.+ Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kuchokera kumʼmawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ali pakati.”