Deuteronomo 1:1-46
1 Awa ndi mawu amene Mose analankhula ndi Aisiraeli onse mʼchipululu, mʼchigawo cha Yorodano, mʼchigwa chimene chinali moyangʼanizana ndi Sufu, pakati pa Parana, Tofeli, Labani, Hazeroti ndi Dizahabi.
2 Kuchokera ku Horebe kupita ku Kadesi-barinea+ kudzera njira yakuphiri la Seiri pali mtunda woyenda masiku 11.
3 Mʼchaka cha 40,+ mʼmwezi wa 11, pa tsiku loyamba la mweziwo, Mose anauza Aisiraeli* zonse zimene Yehova anamuuza kuti awauze.
4 Apa nʼkuti atagonjetsa Sihoni+ mfumu ya Aamori imene inkakhala ku Hesiboni komanso Ogi+ mfumu ya Basana imene inkakhala ku Asitaroti. Mfumu imeneyi anaigonjetsera ku Edirei.+
5 Mose anayamba kufotokoza Chilamulo+ ichi mʼchigawo cha Yorodano mʼdziko la Mowabu kuti:
6 “Yehova Mulungu wathu anatiuza tili ku Horebe kuti, ‘Mwakhalitsa mʼdera lamapiri lino.+
7 Tembenukani mulowere kudera lamapiri la Aamori+ komanso kwa anthu onse oyandikana nawo okhala ku Araba,+ kudera lamapiri, ku Sefela, ku Negebu, mʼmbali mwa nyanja,+ mʼdziko la Akanani ndi ku Lebanoni*+ mpaka kumtsinje waukulu wa Firate.+
8 Taonani, ndikukupatsani dzikolo. Mukalowe mʼdzikolo nʼkulitenga kuti likhale lanu, dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki+ ndi Yakobo,+ kuti adzalipereka kwa iwo ndi kwa mbadwa* zawo.’+
9 Pa nthawi imeneyo ndinakuuzani kuti, ‘Sindikwanitsa ndekha kugwira ntchito yokutsogolerani.+
10 Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ndipo onani, lero mwachulukadi ngati nyenyezi zakuthambo.+
11 Yehova Mulungu wa makolo anu achulukitse chiwerengero chanu+ kuwirikiza maulendo 1,000, ndipo akudalitseni mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.+
12 Inuyo ndinu mtolo ndi katundu wolemera. Ndingathe bwanji kukusenzani ndekha, ndi mtima wanu wokonda mikanganowo?+
13 Sankhani amuna anzeru, aluso ndi ozindikira mʼmafuko anu, kuti ndiwaike kukhala atsogoleri anu.’+
14 Ndiye inu munandiuza kuti, ‘Zimene mwatiuza kuti tichitezi ndi zabwino.’
15 Choncho ndinatenga atsogoleri a mafuko anu, amuna anzeru ndi ozindikira nʼkuwaika kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50, atsogoleri a magulu a anthu 10 ndi akapitawo a mʼmafuko anu.+
16 Pa nthawi imeneyo ndinauza oweruza anu kuti, ‘Mukamaweruza mlandu pakati pa abale anu, muziweruza mwachilungamo+ pakati pa munthu ndi mʼbale wake kapena ndi mlendo.+
17 Musamakondere poweruza mlandu.+ Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka, onse muziwamvetsera chimodzimodzi.+ Musamaope anthu+ chifukwa mukuweruzira Mulungu+ ndipo ngati mlandu wakuvutani muzibwera nawo kwa ine kuti ndiumve.’+
18 Pa nthawi imeneyo ndinakuuzani zonse zimene muyenera kuchita.
19 Kenako tinachoka ku Horebe nʼkudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha+ chonse chija chimene munachiona popita kudera lamapiri la Aamori,+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wathu anatilamula, ndipo pamapeto pake tinafika ku Kadesi-barinea.+
20 Ndiyeno ndinakuuzani kuti, ‘Mwafika mʼdera lamapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akufuna kutipatsa.
21 Onani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani, kalitengeni kuti likhale lanu, mogwirizana ndi zimene Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuuzani.+ Musaope kapena kuchita mantha.’
22 Koma nonse munabwera kwa ine nʼkundiuza kuti, ‘Tiyeni titumize amuna kuti akatifufuzire zokhudza dzikolo ndipo adzatiuze njira imene tikuyenera kudzera ndiponso mizinda imene tikaipeze kumeneko.’+
23 Ine ndinaona kuti amenewo anali maganizo abwino, moti ndinasankha amuna 12 pakati panu, mmodzi pa fuko lililonse.+
24 Choncho iwo ananyamuka nʼkupita kudera lamapiri+ mpaka anakafika kuchigwa cha Esikolo,* ndipo anazonda dzikolo.
25 Iwo anatengako zina mwa zipatso zamʼdzikolo nʼkutibweretsera, ndipo anatiuza kuti, ‘Dziko limene Yehova Mulungu wathu akufuna kutipatsa ndi labwino.’+
26 Koma inu munakana kupita kukalowa mʼdzikolo, ndipo munapandukira lamulo la Yehova Mulungu wanu.+
27 Choncho munapitiriza kungʼungʼudza mʼmatenti anu kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Iguputo chifukwa choti ankadana nafe, ndipo akufuna kutipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge.
28 Kodi tikupita kuti? Abale athu achititsa mantha mitima yathu*+ potiuza kuti, “Kumeneko kuli anthu amphamvu zawo ndiponso ataliatali kuposa ifeyo ndipo mizinda yawo ndi ikuluikulu komanso ili ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.*+ Tinaonakonso ana a Anaki+ kumeneko.”’
29 Ndiye ine ndinakuuzani kuti, ‘Musachite mantha kapena kuwaopa.+
30 Yehova Mulungu wanu adzakutsogolerani ndipo adzakumenyerani nkhondo,+ ngati mmene anachitira ku Iguputo inu mukuona.+
31 Komanso munaona mʼchipululu mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani ngati mmene bambo amanyamulira mwana wake. Ankakunyamulani kulikonse kumene munkapita mpaka kudzafika pamalo ano.’
32 Ngakhale kuti anakuchitirani zonsezi, simunakhulupirire Yehova Mulungu wanu,+
33 amene ankayenda patsogolo panu kuti akufufuzireni malo oti mumangepo msasa. Usiku ankakutsogolerani ndi moto ndipo masana ankakutsogolerani ndi mtambo kuti akusonyezeni njira yoti muyendemo.+
34 Nthawi yonseyi Yehova ankamva zimene munkanena ndipo anakwiya kwambiri, moti analumbira kuti,+
35 ‘Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mʼbadwo woipa uwu amene adzaone dziko labwino limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu,+
36 kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune. Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzapereka dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+
37 (Ngakhale inenso Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu, ndipo anati, “Iwenso sukalowa mʼdziko limeneli.+
38 Yoswa mwana wa Nuni, amene akukutumikira+ ndi amene akalowe mʼdzikomo.+ Umulimbitse,*+ chifukwa ndi amene adzatsogolere Aisiraeli pokatenga dzikolo kukhala lawo.”)
39 Komanso ana anu amene munanena kuti adzagwidwa ndi adani,+ ana anu amene lero sakudziwa chabwino kapena choipa, amenewa ndi amene adzalowe mʼdzikolo ndipo ndidzawapatsa dzikolo kuti likhale lawo.+
40 Koma inu mubwerere, mupite kuchipululu kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.’+
41 Zitatero munandiuza kuti, ‘Tachimwira Yehova. Tsopano tipita kukamenya nkhondo mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wathu watilamula!’ Choncho aliyense wa inu anamanga mʼchiuno zida zake zankhondo, ndipo munkaganiza kuti zikhala zosavuta kukwera phirilo.+
42 Koma Yehova anandiuza kuti, ‘Auze kuti: “Musapite kukamenya nkhondo, chifukwa ine sindikhala nanu.+ Mukapita, adani anu akakugonjetsani.”’
43 Choncho ine ndinalankhula nanu, koma inu simunamvere. Mʼmalomwake, munapandukira lamulo la Yehova nʼkuchita zinthu modzikuza, moti munanyamuka kupita mʼphirimo.
44 Kenako Aamori amene ankakhala mʼphirimo anatuluka kudzakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati mmene njuchi zimachitira, moti anakubalalitsani ku Seiri mpaka kukafika ku Horima.
45 Zitatero munabwerera nʼkuyamba kulira pamaso pa Yehova, koma Yehova sanakumvereni kapena kukulabadirani.
46 Nʼchifukwa chake munakhala ku Kadesi masiku ambiri.”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
^ Zikuoneka kuti kumeneku kunali kumapiri a ku Lebanoni.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Kapena kuti, “kukhwawa la Esikolo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “achititsa kuti mitima yathu isungunuke.”
^ Kutanthauza kuti mizindayo inali ndi mipanda italiitali.
^ Mabaibulo ena amati, “Mulungu wamulimbitsa.”