Deuteronomo 10:1-22

  • Anapanganso miyala yosema iwiri (1-11)

  • Zimene Yehova amafuna (12-22)

    • Muziopa komanso kukonda Yehova (12)

10  “Pa nthawi imeneyo Yehova anandiuza kuti, ‘Useme miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija+ komanso upange likasa lamatabwa. Ukatero ukwere mʼphiri muno kwa ine.  Pamiyalayo ndidzalembapo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija, imene unaiswa, ndipo udzaiike mʼlikasalo.’  Choncho ndinapanga likasa la mtengo wa mthethe nʼkusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija. Kenako ndinakwera mʼphiri, miyala iwiriyo ili mʼmanja mwanga.+  Ndiyeno analemba pamiyalayo mawu amene analemba poyamba aja,+ Malamulo Khumi,*+ amene Yehova anakuuzani paphiri kuchokera mʼmoto,+ pa tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Atatero, Yehova anandipatsa miyalayo.  Kenako ndinatembenuka nʼkutsika mʼphirimo+ ndipo ndinaika miyala iwiriyo mʼlikasa limene ndinapanga. Mpaka pano miyalayo idakali momwemo, mogwirizana ndi zimene Yehova anandilamula.  Zitatero Aisiraeli anachoka ku Beeroti Bene-yaakana kupita ku Mosera. Kumeneku nʼkumene Aroni anafera ndipo anamuikanso komweko.+ Mwana wake Eleazara anayamba kutumikira monga wansembe mʼmalo mwa Aroniyo.+  Ndiyeno ananyamuka pamalo amenewo kupita ku Gudigoda. Anachokanso ku Gudigoda kupita ku Yotibata,+ dziko lokhala ndi mitsinje ya madzi.*  Pa nthawi imeneyo, Yehova anapatula fuko la Levi+ kuti lizinyamula likasa la pangano la Yehova,+ liziima pamaso pa Yehova nʼkumamutumikira komanso kuti lizidalitsa anthu mʼdzina lake+ ngati mmene akuchitira mpaka lero.  Nʼchifukwa chake fuko la Levi silinapatsidwe gawo kapena cholowa ngati abale awo. Cholowa chawo ndi Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anawauza.+ 10  Ine ndinakhala mʼphirimo kwa masiku 40, masana ndi usiku,+ ngati mmene ndinachitira poyamba paja. Pa nthawi imeneyinso Yehova anandimvetsera.+ Yehova sankafuna kukuwonongani. 11  Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Tsogolera anthuwa ndipo mukonzekere ulendo, kuti akalowe nʼkutenga dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndidzawapatsa.’+ 12  Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani?+ Akufuna kuti muzichita izi: muziopa Yehova Mulungu wanu,+ muziyenda mʼnjira zake zonse,+ muzikonda ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse,+ 13  ndiponso kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, kuti zinthu zikuyendereni bwino.+ 14  Taonani, kumwamba ndi kwa Yehova Mulungu wanu, ngakhale kumwamba kwa kumwambako* komanso dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo zonsezo ndi zake.+ 15  Koma Yehova anayandikira kwa makolo anu okha nʼkuwasonyeza chikondi chake, ndipo wasankha inuyo mbadwa zawo+ pakati pa anthu onse, ngati mmene mulili lero. 16  Tsopano muyeretse* mitima yanu+ ndipo musakhalenso ankhutukumve.*+ 17  Chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye. Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera munthu aliyense+ ndipo salandira chiphuphu. 18  Iye amachitira chilungamo ana amasiye ndi akazi amasiye,+ ndipo amakonda mlendo+ moti amamupatsa chakudya ndi zovala. 19  Inunso muzikonda mlendo, chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+ 20  Yehova Mulungu wanu muzimuopa, muzimutumikira,+ muzikhala naye pafupi kwambiri komanso muzilumbira pa dzina lake. 21  Iye ndi amene muyenera kumutamanda.+ Iyeyo ndi Mulungu wanu amene wakuchitirani zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha zonsezi, zimene mwaziona ndi maso anu.+ 22  Makolo anu anapita ku Iguputo ndi anthu 70,+ koma pano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mawu Khumi.”
Kapena kuti, “makhwawa a madzi.”
Kapena kuti, “kumwambamwamba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “muchite mdulidwe wa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo musaumitsenso khosi lanu.”