Deuteronomo 12:1-32

  • Muzilambira pamalo amene Mulungu anasankha (1-14)

  • Analoledwa kudya nyama koma osati magazi (15-28)

  • Musagwidwe mʼmisampha ya milungu ina (29-32)

12  “Awa ndi malangizo ndi zigamulo zimene muyenera kutsatira mosamala, masiku onse amene mudzakhale mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu adzakupatseni kuti likhale lanu.  Mukawonongeretu malo onse amene mitundu imene mukukailanda dziko lawo imatumikirirapo milungu yawo,+ kaya ndi pamapiri ataliatali, pazitunda ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.  Mukagwetse maguwa awo ansembe nʼkuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mukawotche mizati yawo yopatulika* nʼkudula zifaniziro zogoba za milungu yawo,+ ndipo mukachotseretu mayina awo pamalo amenewo.+  Musamalambire Yehova Mulungu wanu mwa njira imeneyi.+  Mʼmalomwake, mudzafunefune Yehova Mulungu wanu pamalo alionse amene adzasankhe kuti aikepo dzina lake komanso malo amene azidzakhala pakati pa mafuko anu onse, ndipo muzidzapita kumeneko.+  Nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu,+ nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo, nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzapita nazo kumalo amenewo.+  Inuyo ndi mabanja anu muzidzadya zimenezi kumalo amenewo pamaso pa Yehova Mulungu wanu,+ ndipo muzidzasangalala ndi zochita zanu zonse+ chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.  Musamakachite zimene tikuchita kuno lero, aliyense kumangochita zimene akuona kuti nʼzabwino,*  chifukwa simunafike kumalo anu a mpumulo+ nʼkulandira cholowa chimene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 10  Mukawoloka Yorodano+ nʼkukakhala mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu, adzakutetezani kwa adani anu onse okuzungulirani, ndipo mudzakhala otetezeka.+ 11  Muzidzabweretsa zinthu zonse zimene ndikukulamulani kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuti kukhale dzina lake.+ Muzidzabweretsa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu ndi nsembe zonse zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo limene munachita kwa Yehova. 12  Mudzasangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu,+ inuyo ndi ana anu aamuna, ana anu aakazi, akapolo anu aamuna, akapolo anu aakazi ndi Mlevi amene akukhala mumzinda wanu,* chifukwa iye sanapatsidwe gawo kapena cholowa mofanana ndi inu.+ 13  Samalani kuti musamadzapereke nsembe zanu zopsereza pamalo ena alionse amene mungaone.+ 14  Muzidzapereka nsembe zanu zopsereza pamalo amene Yehova adzasankhe mʼdera limodzi mwa madera a mafuko anu, ndipo pamalo amenewo muzidzachita chilichonse chimene ndakulamulani.+ 15  Ngati mukufuna kudya nyama, mungathe kupha chiweto chanu nʼkudya nyama yake nthawi iliyonse,+ mogwirizana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani mʼmizinda yanu yonse.* Munthu wodetsedwa komanso munthu wosadetsedwa angathe kudya nyamayo, ngati mmene mungadyere insa ndi mbawala. 16  Koma musamadye magazi ake.+ Muziwathira pansi ngati madzi.+ 17  Simudzaloledwa kudyera mʼmizinda yanu* chakhumi cha mbewu zanu, vinyo wanu watsopano, mafuta anu, ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu ndi a nkhosa zanu,+ iliyonse mwa nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo limene mwachita, nsembe zanu zaufulu kapena chopereka chochokera mʼmanja mwanu. 18  Koma muzidzadya zinthu zimenezi pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+ Muzidzadya zinthuzi inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi ndi Mlevi amene akukhala mumzinda wanu.* Ndipo muzidzasangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi zochita zanu zonse. 19  Samalani kuti musakanyalanyaze Mlevi+ kwa nthawi yonse imene mukakhale mʼdzikolo. 20  Yehova Mulungu wanu akadzawonjezera dziko lanu+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani,+ ndipo inu nʼkunena kuti, ‘Ndikufuna kudya nyama,’ chifukwa mukulakalaka kudya nyama, nthawi iliyonse imene mwalakalaka kudya nyama muzidzadya.+ 21  Ngati malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake+ adzakhale kutali kwambiri ndi inu, muzidzapha zina mwa ngʼombe zanu kapena nkhosa zanu zimene Yehova wakupatsani, mogwirizana ndi zimene ndakulamulani, ndipo nyamazo muzidzadyera mumzinda wanu* nthawi iliyonse imene mukufuna. 22  Mungathe kuidya ngati mmene mungadyere insa ndi mbawala.+ Munthu wodetsedwa komanso munthu wosadetsedwa angathe kudya nyamayo. 23  Koma mungokhala otsimikiza mtima kuti musadye magazi,+ chifukwa magazi ndi moyo,+ ndipo musamadye nyama limodzi ndi moyo wake. 24  Musamadye magazi. Muziwathira pansi ngati madzi.+ 25  Musamadye magazi, kuti zinthu zikuyendereni bwino inuyo ndi ana anu obwera mʼmbuyo mwanu, chifukwa choti mukuchita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova. 26  Popita kumalo amene Yehova adzasankhe, muzidzatenga zinthu zanu zokha zopatulika komanso zinthu zoti mukapereke nsembe pokwaniritsa lonjezo limene munachita. 27  Kumeneko muzikapereka nsembe zanu zopsereza, nyama ndi magazi,+ paguwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. Magazi a nsembe zanu azidzathiridwa pansi pafupi ndi guwa lansembe+ la Yehova Mulungu wanu, koma nyamayo mungathe kuidya. 28  Muzionetsetsa kuti mukumvera mawu onsewa amene ndikukuuzani, kuti nthawi zonse zinthu zizikuyenderani bwino, inuyo ndi ana anu obwera mʼmbuyo mwanu, chifukwa choti mukuchita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29  Yehova Mulungu wanu akadzawononga mitundu imene mukupita kukailanda dziko,+ inuyo nʼkuyamba kukhala mʼdziko lawolo, 30  mukasamale kuti musakagwidwe mumsampha wawo, pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso panu. Musakafunse zokhudza milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inkatumikira bwanji milungu yawo? Inenso ndichita zomwezo.’+ 31  Musamalambire Yehova Mulungu wanu mwa njira imeneyi, chifukwa iwo amachitira milungu yawo zinthu zonse zonyansa zimene Yehova amadana nazo. Iwo amafika ngakhale powotcha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto kuti ikhale nsembe kwa milungu yawo.+ 32  Muzionetsetsa kuti mukutsatira mawu onse amene ndikukuuzani.+ Musawonjezerepo kapena kuchotsapo kalikonse.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “gawo limodzi mwa magawo 10.”
Kapena kuti, “zimene akuganiza kuti nʼzabwino.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkati mwa mageti anu onse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkati mwa mageti anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”