Deuteronomo 13:1-18

  • Zoyenera kuchita ndi ampatuko (1-18)

13  “Pakati panu pakapezeka mneneri kapena wolosera za mʼtsogolo pogwiritsa ntchito maloto nʼkukupatsani chizindikiro kapena kulosera china chake,  ndipo chizindikiro kapena zimene analoserazo zachitikadi, kenako iye nʼkunena kuti, ‘Tiyeni titsatire milungu ina,’ milungu imene simukuidziwa, ‘ndipo tiitumikire,’  musamvere mawu a mneneriyo kapena woloserayo,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu akukuyesani+ kuti adziwe ngati mumakonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse.+  Muzitsatira Yehova Mulungu wanu, muzimuopa, muzisunga malamulo ake, muzimvera mawu ake ndipo iye ndi amene muyenera kumutumikira komanso kumumamatira.+  Koma mneneri kapena woloserayo muzimupha,+ chifukwa akulimbikitsa anthu kuti azipandukira Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo komanso kukuwombolani mʼnyumba yaukapolo. Munthu ameneyo akufuna akupatutseni panjira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muziyendamo. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+  Mchimwene wanu, amene ndi mwana wamwamuna wa mayi anu, kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mkazi wanu wokondedwa kapena mnzanu wapamtima, akayesa kukukopani mwachinsinsi pokuuzani kuti, ‘Tiyeni tikatumikire milungu ina,’+ milungu imene inuyo kapena makolo anu sankaidziwa,  kaya ndi milungu ya anthu amene akuzungulirani, amene akukhala pafupi ndi inu kapena amene akukhala kutali ndi inu, kuchokera kumalekezero ena a dziko kukafika kumalekezero ena,  musavomere kuchita zimene akufunazo kapena kumumvera.+ Musamumvere chisoni kapena kumuchitira chifundo kapenanso kumuteteza.  Koma muzimupha ndithu.+ Dzanja lanu lizikhala loyamba kumʼponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo.+ 10  Muzimuponya miyala kuti afe,+ chifukwa amafuna akuchotseni kwa Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo. 11  Zikadzatero Aisiraeli onse adzamva nʼkuchita mantha, ndipo sadzachitanso chinthu choipa chilichonse ngati chimenechi pakati panu.+ 12  Mukadzamva mu umodzi mwa mizinda yanu, imene Yehova Mulungu wanu wakupatsani kuti muzikhalamo kuti, 13  ‘Pakati panu papezeka anthu opanda pake amene akufuna kusocheretsa anthu mumzinda wawo, ponena kuti: “Tiyeni tikatumikire milungu ina,” milungu imene inu simukuidziwa,’ 14  muzifufuza mosamala kwambiri komanso muzifunsa ena za nkhaniyo.+ Ndiye zikatsimikizirika kuti ndi zoonadi kuti chinthu chonyansachi chachitika pakati panu, 15  muzipha ndithu anthu amumzindawo ndi lupanga.+ Muziwononga ndi lupanga mzindawo komanso chilichonse chimene chili mmenemo, kuphatikizapo ziweto zake.+ 16  Kenako muzisonkhanitsa zinthu zonse zimene mwapeza mumzindawo, pakati pa bwalo lake nʼkuwotcha mzindawo ndi moto. Ndipo zinthu zimene munapeza mumzindawo zidzakhala nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova Mulungu wanu. Mzindawo udzakhale bwinja mpaka kalekale ndipo usadzamangidwenso. 17  Dzanja lanu lisatenge chinthu chilichonse choyenera kuwonongedwa,+ kuti mkwiyo woyaka moto wa Yehova usiye kukuyakirani ndiponso kuti akuchitireni chifundo, kukumverani chisoni ndi kukuchulukitsani, mogwirizana ndi zimene analumbira kwa makolo anu.+ 18  Choncho muzimvera* Yehova Mulungu wanu, posunga malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero, mukatero mudzachita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “muzimvera mawu a.”