Deuteronomo 14:1-29

  • Zinthu zosayenera kuchita polira maliro (1, 2)

  • Zakudya zodetsedwa komanso zosadetsedwa (3-21)

  • Chakhumi choperekedwa kwa Yehova (22-29)

14  “Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu. Musamadzichekecheke+ kapena kumeta nsidze zanu* chifukwa cha anthu akufa.+  Chifukwa ndinu anthu oyera+ kwa Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova wakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera, pa anthu onse okhala padziko lapansi.+  Musamadye chinthu chilichonse chonyansa.+  Nyama zimene mungathe kudya+ ndi izi: ngʼombe, nkhosa, mbuzi,  mbawala, insa, ngondo, mbuzi yakuthengo, mphalapala, nkhosa yakuthengo ndi nkhosa yamʼmapiri.  Mungathe kudya nyama iliyonse ya ziboda zogawanika, zokhala ndi mpata pakati, imenenso imabzikula.  Koma musamadye nyama izi zokha zimene zimabzikula kapena zimene zili ndi ziboda zogawanika: ngamila, kalulu ndi mbira, chifukwa zimabzikula koma si zogawanika ziboda. Nyama zimenezi nʼzodetsedwa kwa inu.+  Musamadyenso nkhumba chifukwa ndi ya ziboda zogawanika koma sibzikula. Imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu. Musamadye nyama yake kapena kuikhudza ikafa.  Pa zinthu zonse zokhala mʼmadzi, zimene mungadye ndi izi: Chilichonse chimene chili ndi zipsepse ndi mamba mungadye.+ 10  Koma musamadye chilichonse chimene chilibe zipsepse ndi mamba. Chimenecho nʼchodetsedwa kwa inu. 11  Mungathe kudya mbalame iliyonse yosadetsedwa. 12  Koma mbalame izi ndi zimene simuyenera kudya: chiwombankhanga, nkhwazi, muimba wakuda,+ 13  mphamba wofiira, mphamba wakuda ndi mtundu uliwonse wa kamtema. 14  Simuyeneranso kudya mtundu uliwonse wa khwangwala, 15  nthiwatiwa, kadzidzi, kakowa ndi mtundu uliwonse wa kabawi, 16  nkhwezule, mantchichi, tsekwe, 17  vuwo, muimba, chiswankhono, 18  dokowe, sadzu, mleme ndi mtundu uliwonse wa chimeza. 19  Tizilombo tonse ta mapiko timene timapezeka tambiri nʼtodetsedwanso kwa inu. Timeneti simuyenera kudya. 20  Cholengedwa chilichonse chouluka chosadetsedwa mungadye. 21  Musamadye nyama iliyonse imene mwaipeza yakufa.+ Mungapatse mlendo amene akukhala mumzinda wanu* kuti adye, kapena mungathe kuigulitsa kwa mlendo chifukwa inu ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu. Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.+ 22  Musamalephere kupereka chakhumi cha zokolola zonse za mʼmunda mwanu chaka ndi chaka.+ 23  Muzidzadya chakhumi cha mbewu zanu, kumwa vinyo wanu watsopano, kudya mafuta anu, ana oyamba a ngʼombe ndi a nkhosa zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene iye adzasankhe kuikapo dzina lake.+ Muzidzachita zimenezi kuti mudzaphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse.+ 24  Koma ngati ulendowo ndi wautali kwa inu ndipo simungathe kunyamula chakhumicho kupita nacho kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake,+ chifukwa malowo ali kutali ndi inu (chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani), 25  muzidzagulitsa chakhumicho ndipo muzidzatenga ndalamazo mʼmanja mwanu nʼkupita kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. 26  Ndalamazo muzidzagulira chilichonse chimene mtima wanu wafuna, kaya ndi ngʼombe, nkhosa, mbuzi, vinyo, chakumwa choledzeretsa ndi chilichonse chimene mtima wanu wafuna. Ndipo muzidzadya zinthuzi pamaso pa Yehova Mulungu wanu nʼkusangalala, inuyo ndi banja lanu.+ 27  Ndipo musaiwale Mlevi amene akukhala mumzinda wanu,+ chifukwa sanapatsidwe gawo kapena cholowa ngati inuyo.+ 28  Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzidzabweretsa chakhumi cha zokolola zanu zonse mʼchaka chachitatucho, ndipo muzidzachisiya mkati mwa mzinda wanu.+ 29  Ndiyeno Mlevi, amene sanapatsidwe gawo kapena cholowa ngati inuyo, komanso mlendo, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye amene akukhala mumzinda wanu, azibwera kudzadya ndi kukhuta+ kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kumeta mpala pachipumi panu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”