Deuteronomo 15:1-23

  • Ankakhululukira angongole chaka cha 7 chilichonse (1-6)

  • Kuthandiza osauka (7-11)

  • Akapolo ankamasulidwa chaka cha 7 chilichonse (12-18)

    • Kuboola khutu la kapolo (16, 17)

  • Nyama zoyamba kubadwa zinali zopatulika (19-23)

15  “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse muzimasula anthu amene anakongola zinthu zanu.+  Muzichita izi pomasula anthu angongolewo: Munthu aliyense azimasula mnzake amene ali ndi ngongole yake. Asamakakamize mnzake kapena mʼbale wake kuti abweze ngongoleyo, chifukwa chilengezo choti anthu angongole amasuke chaperekedwa potsatira lamulo la Yehova.+  Mlendo mungathe kumukakamiza kuti abweze ngongole,+ koma ngati mʼbale wanu wakongola chinthu chanu chilichonse, musamukakamize kuti achibweze.  Pakati panu pasapezeke munthu wosauka, chifukwa Yehova adzakudalitsani ndithu+ mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu.  Adzakudalitsani pokhapokha ngati mutamvera mosamala mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mokhulupirika malamulo onsewa amene ndikukupatsani lero.+  Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mogwirizana ndi zimene anakulonjezani ndipo mitundu yambiri idzakongola zinthu zanu,* koma inu simudzafunika kukongola kanthu.+ Mudzalamulira mitundu yambiri koma mitunduyo sidzakulamulirani.+  Ngati mmodzi mwa abale anu wasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musamamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lanu.+  Koma muzithandiza mʼbale wanuyo mowolowa manja,+ ndipo mulimonse mmene zingakhalire, muzimukongoza* chilichonse chimene akufuna kapena chimene akusowa.  Samalani kuti musakhale ndi maganizo oipa awa mumtima mwanu akuti, ‘Chaka cha 7 choti anthu angongole amasuke chayandikira,’+ nʼkulephera kuthandiza mʼbale wanu wosaukayo mowolowa manja, osamupatsa chilichonse. Ngati atafuulira Yehova chifukwa cha zimene inuyo mwamuchitira, mudzakhala kuti mwachimwa.+ 10  Muzimupatsa mowolowa manja zimene akufunazo,+ ndipo musamamupatse* zinthuzo monyinyirika. Mukamachita zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita ndi ntchito zanu zonse.+ 11  Mʼdziko lanu mudzapitirizabe kupezeka anthu osauka.+ Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti, ‘Muzikhala owolowa manja kwa mʼbale wanu wovutika komanso wosauka mʼdziko lanu.’+ 12  Ngati mʼbale wanu anagulitsidwa kwa inu, kaya ndi mwamuna kapena mkazi wa Chiheberi, ndipo wakutumikirani zaka 6, mʼchaka cha 7 muzimumasula nʼkumulola kuti achoke.+ 13  Ndipo mukamʼmasula, musamulole kuti achoke chimanjamanja. 14  Muzimupatsa mowolowa manja zina mwa nkhosa zanu, mbewu zochokera pamalo anu opunthira, mafuta ochokera pamalo oyengera ndi vinyo wochokera moponderamo mphesa. Muzimupatsa mogwirizana ndi mmene Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani. 15  Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwombolani. Nʼchifukwa chake lero ndikukulamulani kuti muzichita zinthu zimenezi. 16  Koma kapoloyo akakuuzani kuti, ‘Ine sindikusiyani!’ chifukwa chakuti amakukondani komanso amakonda banja lanu, ndipo pamene amakhala ndi inu amasangalala,+ 17  muzitenga choboolera nʼkuboola khutu lake ali pakhomo, mpaka chobooleracho chigunde chitseko ndipo azikhala kapolo wanu moyo wake wonse. Muzichitanso zimenezi ndi kapolo wanu wamkazi. 18  Musamaone kuti sipanachitike chilungamo ngati kapolo wanu mwamumasula iye nʼkuchoka, chifukwa ntchito imene wakugwirirani kwa zaka 6 ndi yochuluka kuwirikiza kawiri kuposa ya munthu waganyu, ndipo Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa chilichonse. 19  Mwana aliyense wamphongo woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena wa nkhosa muzimupatula nʼkumupereka kwa Yehova Mulungu wanu.+ Musamagwiritse ntchito iliyonse mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe,* kapena kumeta ubweya wa mwana woyamba kubadwa wa nkhosa. 20  Chaka chilichonse inuyo ndi banja lanu muzidzadya mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena wa nkhosa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Yehova adzasankhe.+ 21  Koma ngati nyamayo ili ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, musamaipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.+ 22  Muziidyera mumzinda wanu* ngati mmene mumadyera insa ndi mbawala.+ Munthu wodetsedwa komanso munthu woyera nayenso azidya nawo. 23  Koma musamadye magazi ake.+ Muziwathira pansi ngati madzi.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “idzakongola zinthu zanu itakupatsani chikole.”
Kapena kuti, “muzimukongoza atakupatsani chikole.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wanu usamamupatse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngʼombe yamphongo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”