Deuteronomo 16:1-22

  • Pasika; Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa (1-8)

  • Chikondwerero cha Masabata (9-12)

  • Chikondwerero cha Misasa (13-17)

  • Kusankha oweruza (18-20)

  • Zinthu zosayenera kuzilambira (21, 22)

16  “Muzikumbukira kuti mwezi wa Abibu* ndi wofunika ndipo muzichita chikondwerero cha Pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa mʼmwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+  Ndipo muzipereka nsembe ya Pasika kwa Yehova Mulungu wanu.+ Muzipereka nkhosa ndi ngʼombe+ pamalo amene Yehova adzasankhe kuikapo dzina lake.+  Musamadye nsembeyo limodzi ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa.+ Kwa masiku 7 muzidya mkate wopanda zofufumitsa, umene ndi mkate wamasautso, chifukwa munatuluka mofulumira mʼdziko la Iguputo.+ Muzichita zimenezi kuti muzikumbukira tsiku limene munatuluka mʼdziko la Iguputo, masiku onse a moyo wanu.+  Musamapezeke ndi mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa mʼdziko lanu lonse kwa masiku 7.+ Nyama iliyonse imene mwapereka nsembe madzulo, pa tsiku loyamba, isamagone mpaka mʼmawa.+  Simudzaloledwa kupereka nsembe ya Pasika mumzinda wanu uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.  Koma muzidzapereka nsembe ya Pasikayo pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake. Muzidzapereka nsembeyo madzulo, dzuwa likangolowa,+ pa nthawi yofanana ndi imene munatuluka mu Iguputo.  Muzidzaiwotcha nʼkuidya+ pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe,+ ndipo mʼmawa mwake muzidzabwerera kumatenti anu.  Muzidya mkate wopanda zofufumitsa kwa masiku 6, ndipo pa tsiku la 7 muzichitira Yehova Mulungu wanu msonkhano wapadera. Pa tsikuli musamagwire ntchito.+  Muziwerenga masabata 7. Muziyamba kuwerenga masabata 7 amenewo kuchokera pa nthawi imene mwayamba kumweta tirigu.+ 10  Ndiyeno muzichitira Yehova Mulungu wanu Chikondwerero cha Masabata,+ popereka nsembe zaufulu zimene mungathe, mogwirizana ndi mmene Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.+ 11  Ndipo muzidzasangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, Mlevi amene akukhala mumzinda wanu,* mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali pakati panu. Muzidzasangalala pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake.+ 12  Muzikumbukira kuti munali akapolo ku Iguputo,+ ndipo muzisunga komanso kutsatira malamulo amenewa. 13  Muzichita Chikondwerero cha Misasa+ kwa masiku 7, mukamatuta zokolola kuchokera pamalo opunthira mbewu, pamalo oyengera mafuta ndi pamalo opondera mphesa. 14  Muzisangalala pa chikondwerero chimenecho,+ inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, Mlevi, mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali mumzinda wanu. 15  Muzichitira Yehova Mulungu wanu chikondwerero chimenecho kwa masiku 7+ pamalo amene Yehova adzasankhe. Muzichita chikondwererochi chifukwa Yehova Mulungu wanu adzadalitsa zokolola zanu zonse ndi chilichonse chimene dzanja lanu likuchita,+ ndipo inu mudzakhala osangalala kwambiri.+ 16  Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe. Azikaonekera pa Chikondwerero cha Mkate Wopanda Zofufumitsa,+ Chikondwerero cha Masabata+ ndi pa Chikondwerero cha Misasa.+ Palibe aliyense wa iwo amene akuyenera kukaonekera kwa Yehova chimanjamanja. 17  Mphatso imene aliyense ayenera kubweretsa izikhala yogwirizana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 18  Musankhe oweruza+ ndi atsogoleri a fuko lililonse mʼmizinda yonse imene* Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndipo aziweruza anthu mwachilungamo. 19  Musamakhotetse chilungamo,+ musamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ komanso kupotoza mawu a anthu olungama. 20  Muzichita zinthu mwachilungamo+ kuti mukhale ndi moyo nʼkukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 21  Musadzadzale mtengo uliwonse kuti ukhale mzati wopatulika*+ pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu limene mudzapange. 22  Ndipo musadzaimike chipilala chopatulika,+ chinthu chimene Yehova Mulungu wanu amadana nacho.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu onse amene.”