Deuteronomo 17:1-20

  • Nsembe zizikhala zopanda chilema (1)

  • Zoyenera kuchita ndi ampatuko (2-7)

  • Milandu yovuta kuweruza (8-13)

  • Malangizo oti mafumu azidzatsatira (14-20)

    • Mfumu izikopera buku la Chilamulo (18)

17  “Musamapereke kwa Yehova Mulungu wanu nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena vuto lililonse, chifukwa idzakhala yonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.+  Ngati pakati panu papezeka mwamuna kapena mkazi amene akuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, mu umodzi mwa mizinda yanu imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndipo akuphwanya pangano la Mulungu,+  moti wasochera ndipo amalambira milungu ina nʼkumaigwadira, kapena kugwadira dzuwa, mwezi kapena gulu lonse la zinthu zakuthambo,+ zomwe ine sindinakulamuleni,+  ndiye munthu wina akakuuzani zimenezi kapena mwamva zimene zachitika, muzifufuza nkhaniyo mosamala. Mukatsimikizira kuti ndi zoonadi+ kuti chinthu choipachi chachitika mu Isiraeli,  muzitenga mwamuna kapena mkazi amene wachita chinthu choipayo nʼkupita naye kunja kwa mzinda, ndipo muzikamuponya miyala kuti afe.+  Munthuyo aziphedwa ngati pali umboni wa* anthu awiri kapena atatu.+ Asaphedwe ngati munthu mmodzi yekha ndi amene wapereka umboni.+  Dzanja la mbonizo lizikhala loyamba kumuponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+  Ngati mu umodzi mwa mizinda yanu muli mlandu wovuta kwambiri kuweruza kaya ndi mlandu wokhudza kukhetsa magazi,+ mlandu umene munthu wakasuma, mlandu wokhudza zachiwawa kapena mkangano, muzinyamuka nʼkupita kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+  Muzipita kwa Alevi omwe ndi ansembe ndi kwa woweruza+ amene akutumikira mʼmasiku amenewo. Muziwafotokozera nkhaniyo ndipo iwo azikuuzani chigamulo.+ 10  Kenako muzichita mogwirizana ndi chigamulo chimene akuuzani kumalo amene Yehova adzasankhe. Muzionetsetsa kuti mukuchita zonse zimene akulangizani. 11  Muzichita mogwirizana ndi lamulo limene akusonyezani komanso chigamulo chimene akuuzani.+ Musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere pa chigamulo chimene akupatsani.+ 12  Munthu amene adzachite zinthu modzikuza posamvera wansembe amene akutumikira Yehova Mulungu wanu kapena woweruza, ayenera kufa.+ Muzichotsa woipayo mu Isiraeli.+ 13  Anthu onse adzamva zimenezo nʼkuchita mantha ndipo sadzachitanso zinthu modzikuza.+ 14  Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani nʼkulitenga kukhala lanu ndipo mukukhalamo, ndiye inu nʼkunena kuti, ‘Tisankhe mfumu ngati mitundu ina yonse imene yatizungulira,’+ 15  mudzasankhe mfumu imene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+ Mudzasankhe mfumuyo kuchokera pakati pa abale anu. Simukuloledwa kusankha mlendo amene si mʼbale wanu. 16  Koma iye asakhale ndi mahatchi ambiri+ kapena kuchititsa anthu kuti abwerere ku Iguputo kuti akatenge mahatchi ochuluka+ chifukwa Yehova anakuuzani kuti, ‘Musabwererenso kudzera njira iyi.’ 17  Asakhalenso ndi akazi ambiri kuti mtima wake usapatuke+ komanso asakhale ndi siliva ndi golide wambiri.+ 18  Akakhala pampando wachifumu, ayenera kukopera buku lakelake la Chilamulo ichi, kuchokera mʼbuku limene* Alevi omwe ndi ansembe amasunga.+ 19  Buku limeneli azikhala nalo nthawi zonse ndipo aziliwerenga masiku onse a moyo wake,+ kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake ndi kusunga mawu onse a Chilamulo ichi, komanso kutsatira malangizo ake.+ 20  Akachita zimenezi sadzadzikweza pamaso pa abale ake, komanso sadzachoka pachilamulo nʼkupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere, kuti iyeyo ndi ana ake apitirize kukhala mafumu mu Isiraeli kwa nthawi yaitali.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “aziphedwa pakamwa pa.”
Kapena kuti, “mpukutu umene.”