Deuteronomo 19:1-21

  • Mlandu wa magazi komanso mizinda yothawirako (1-13)

  • Zizindikiro za malire sizinkafunika kusunthidwa (14)

  • Anthu operekera umboni mukhoti (15-21)

    • Pankafunika mboni ziwiri kapena zitatu (15)

19  “Yehova Mulungu wanu akadzawononga mitundu yamʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, inu nʼkuwalandadi dzikolo ndi kukhala mʼmizinda yawo komanso mʼnyumba zawo,+  mudzapatule mizinda itatu pakati pa dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu.+  Mudzagawe mʼzigawo zitatu dziko limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani kuti likhale lanu, ndipo mudzalambule misewu yopita kumizindayo kuti aliyense wopha munthu azithawira kumizinda imeneyo.  Ndiye zimene zizichitika ndi munthu amene wapha mnzake nʼkuthawira kumeneko kuti akhale ndi moyo ndi izi: Ngati wapha mnzake mwangozi ndipo sankadana naye,+  mwachitsanzo, munthu akapita ndi mnzake kuthengo kukafuna nkhuni, ndipo wakweza dzanja lake kuti adule mtengo ndi nkhwangwa koma nkhwangwayo yaguluka mumpini wake nʼkumenya mnzakeyo mpaka kumupha, amene wapha mnzakeyo azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+  Akapanda kutero, chifukwa chakuti wobwezera magazi+ ndi wokwiya kwambiri,* angathamangitse wopha munthuyo nʼkumupeza kenako nʼkumumpha chifukwa chakuti mtunda wopita kumzindawo unali wautali. Koma wopha mnzake mwangoziyo samayenera kufa chifukwa sankadana ndi mnzakeyo.+  Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti, ‘Mupatule mizinda itatu.’  Yehova Mulungu wanu akadzawonjezera dziko lanu mogwirizana ndi zimene analumbira kwa makolo anu,+ nʼkukupatsani dziko lonse limene analonjeza makolo anu kuti adzawapatsa,+  (ngati mutatsatira mokhulupirika malamulo onsewa amene ndikukupatsani lero, akuti muzikonda Yehova Mulungu wanu komanso kuyenda mʼnjira zake nthawi zonse+) mudzawonjezere mizinda inanso itatu pa mizinda imeneyi.+ 10  Mukamachita zimenezi simudzakhetsa magazi a munthu wosalakwa+ mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa ndipo simudzakhala ndi mlandu wa magazi.+ 11  Koma ngati munthu amadana ndi mnzake+ ndipo wamubisalira panjira nʼkumuvulaza kwambiri mpaka mnzakeyo kufa, iye nʼkuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, 12  akulu amumzinda wakwawo azimuitanitsa kuchokera kumeneko nʼkumupereka mʼmanja mwa wobwezera magazi ndipo azimupha.+ 13  Musamamumvere* chisoni ndipo muzichotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa mu Isiraeli+ kuti zinthu zikuyendereni bwino. 14  Mukadzalandira cholowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu musamadzasunthe zizindikiro za malire a mnzanu,+ pamalo amene makolo anu anaika kale malire. 15  Mboni imodzi si yokwanira kutsimikizira kuti munthu wachitadi cholakwa kapena tchimo lililonse.+ Muzitsimikizira nkhaniyo mutamva umboni wochokera kwa* mboni ziwiri kapena zitatu.+ 16  Ngati munthu wakonzera mnzake chiwembu nʼkupereka umboni wonama wakuti waphwanya lamulo,+ 17  anthu awiri amene akukanganawo aziima pamaso pa Yehova, kapena kuti pamaso pa ansembe ndi oweruza amene akuweruza masiku amenewo.+ 18  Oweruzawo azifufuza nkhaniyo mosamala+ ndipo ngati munthu amene anapereka umboniyo wapezeka kuti amanama ndipo waneneza mʼbale wake mlandu wabodza, 19  muzimuchitira zimene amafuna kuti zichitikire mʼbale wakezo,+ ndipo muzichotsa woipayo pakati panu.+ 20  Ena onse adzamva nʼkuchita mantha, ndipo sadzachitanso choipa chilichonse ngati chimenechi pakati panu.+ 21  Musamamve* chisoni.+ Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wake ndi wodzaza ndi ukali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “diso lanu lisamamumvere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Diso lanu lisamamve.”