Deuteronomo 20:1-20

  • Malamulo okhudza nkhondo (1-20)

    • Anthu amene samayenera kupita kunkhondo (5-9)

20  “Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, nʼkuona kuti ali ndi mahatchi, magaleta ankhondo komanso asilikali ochuluka kuposa inu, musachite nawo mantha chifukwa Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo ali ndi inu.+  Mukatsala pangʼono kuyamba nkhondo, wansembe azifika pafupi nʼkulankhula ndi anthu.+  Iye aziwauza kuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu. Mwatsala pangʼono kumenyana ndi adani anu. Mitima yanu isachite mantha. Musaope, kuchita mantha kapena kunjenjemera chifukwa cha iwo,  chifukwa Yehova Mulungu wanu akuyenda nanu limodzi kuti akumenyereni nkhondo nʼkukupulumutsani kwa adani anu.’+  Atsogoleri nawonso aziuza anthuwo kuti, ‘Kodi pali amene wamanga nyumba yatsopano koma sanaitsegulire? Achoke nʼkubwerera kunyumba yakeyo, kuopera kuti angafe pankhondo, ndipo munthu wina angatsegulire nyumbayo.  Kodi pali amene walima munda wa mpesa koma sanayambe kukolola zipatso zake? Achoke nʼkubwerera kunyumba yake, kuopera kuti angafe pankhondo ndipo munthu wina angakolole zipatsozo.  Kodi pali amene analonjeza mkazi kuti adzamukwatira koma sanamukwatire? Achoke nʼkubwerera kunyumba yake,+ kuopera kuti angafe pankhondo ndipo mwamuna wina angakwatire mkaziyo.’  Atsogoleriwo afunsenso anthuwo kuti, ‘Kodi pali wamantha komanso wosalimba mtima?+ Abwerere kunyumba yake, kuti asachititse mantha mitima ya abale ake ngati mmene iye wachitira.’*+  Atsogoleriwo akamaliza kulankhula ndi anthu, azisankha akulu a magulu ankhondo oti azitsogolera anthuwo. 10  Mukayandikira mzinda kuti mumenyane nawo, muzilengeza kwa anthu amumzindawo mfundo za mtendere.+ 11  Ngati anthu amumzindawo akuyankhani mwamtendere nʼkukutsegulirani mageti ake, anthu onse opezeka mmenemo azikhala anu kuti azikugwirirani ntchito yaukapolo ndipo azikutumikirani.+ 12  Koma ngati anthuwo akana kuchita nanu mtendere, ndipo akuchita nanu nkhondo, inuyo muzizungulira mzindawo, 13  Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu mʼmanja mwanu, ndipo zikatero muzipha mwamuna aliyense ndi lupanga. 14  Koma muzitenga akazi, ana aangʼono, ziweto ndi chilichonse chopezeka mumzindawo kuti zikhale zanu,+ ndipo muzidya zimene mwatenga kwa adani anu amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 15  Muzichita zimenezi ndi mizinda yonse imene ili kutali kwambiri ndi inu, yomwe sili pakati pa mizinda ya mitundu iyi imene yayandikana nanu. 16  Koma mʼmizinda ya anthu awa, imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, musalole kuti mutsale chamoyo chilichonse.+ 17  Mʼmalomwake, mudzawononge anthu onse. Mudzawononge Ahiti, Aamori, Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani. 18  Mukawawononge kuti asakakuphunzitseni kuchita zinthu zonse zonyansa zimene achitira milungu yawo nʼkukuchititsani kuti muchimwire Yehova Mulungu wanu.+ 19  Mukazungulira mzinda nʼcholinga choti muulande ndipo mwakhala mukumenyana nawo kwa masiku ambiri, musawononge mitengo yake poidula ndi nkhwangwa. Mukhoza kudya zipatso za mitengoyo, koma simukuyenera kuidula.+ Kodi mtengo wamʼmunda ndi munthu kuti muwuukire? 20  Mungathe kuwononga mtengo wokhawo umene mukuudziwa kuti subereka zipatso zakudya. Mtengo woterowo mungaudule nʼkumangira mpanda wozungulira mzinda wa adani amene akuchita nanu nkhondo, mpaka mzindawo utagwa.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kuchititsa mtima wa abale ake kuti usungunuke ngati wake.”