Deuteronomo 21:1-23

  • Ngati wopha munthu sakudziwika (1-9)

  • Kukwatira akazi ogwidwa kunkhondo (10-14)

  • Ufulu wa mwana woyamba kubadwa (15-17)

  • Mwana wosamvera (18-21)

  • Munthu wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa (22, 23)

21  “Ngati mwapeza munthu wakufa pathengo, mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala lanu, ndipo amene wapha munthuyo sakudziwika,  akulu ndi oweruza anu+ azipita kukayeza mtunda kuchokera pamene pali munthu wakufayo kukafika kumizinda yonse yozungulira malo amene munthuyo wapezeka.  Ndiyeno akulu amumzinda umene uli pafupi ndi pamene papezeka munthu wakufayo, azitenga ngʼombe yaingʼono yaikazi imene sanaigwiritsepo ntchito, imene sinasenzepo goli nʼkukoka chilichonse.  Akulu a mumzindawo azitenga ngʼombeyo nʼkupita nayo kuchigwa chimene chili* ndi madzi oyenda. Chigwa chimenechi chikhale choti sichinalimidwepo kapena kudzalidwa mbewu. Akafika kumeneko azipha ngʼombe yaingʼonoyo poithyola khosi.+  Ansembe, omwe ndi Alevi, azifika pafupi chifukwa ndi amene Yehova Mulungu wanu wawasankha kuti azimutumikira+ komanso azidalitsa mʼdzina la Yehova.+ Iwo ndi amene akuyenera kunena njira yothetsera mkangano uliwonse wokhudza zinthu zankhanza zimene zachitika.+  Ndiyeno akulu onse amumzinda umene uli pafupi ndi munthu wakufayo azisamba mʼmanja+ pamwamba pa ngʼombe imene yathyoledwa khosi mʼchigwa ija.  Ndipo iwo azinena kuti, ‘Manja athu sanakhetse magazi awa, ndiponso maso athu sanaone magaziwa akukhetsedwa.  Inu Yehova, musaimbe mlanduwu anthu anu Aisiraeli amene munawawombola,+ ndipo musalole kuti mlandu wa magazi a munthu wosalakwa ukhale pa anthu anu Aisiraeli.’+ Akatero iwo sadzaimbidwa mlandu wa magaziwo.  Mukadzachita zimenezi mudzachotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa pakati panu, chifukwa mudzakhala mutachita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova. 10  Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu wakugonjetserani adaniwo, inu nʼkuwatenga kuti akhale akapolo,+ 11  ndipo pakati pa anthu ogwidwawo mwaonapo mkazi wokongola ndipo mwakopeka naye moti mukufuna kumutenga kuti akhale mkazi wanu, 12  mungathe kumutenga nʼkulowa naye mʼnyumba yanu. Kenako azimeta tsitsi lake nʼkusamalira zikhadabo zake. 13  Azisintha zovala zimene anavala pa nthawi imene ankagwidwa ukapolo ndipo azikhala mʼnyumba mwanu. Azilira maliro a bambo ake ndi a mayi ake kwa mwezi wathunthu,+ kenako mungathe kugona naye. Inu mudzakhala mwamuna wake ndipo iye adzakhala mkazi wanu. 14  Koma ngati simukusangalala naye muzimulola kuti achoke+ nʼkupita kulikonse kumene akufuna. Koma simukuyenera kumugulitsa kapena kumuchitira nkhanza, chifukwa mwamuchititsa manyazi. 15  Ngati mwamuna ali ndi akazi awiri, koma amakonda mmodzi kuposa winayo,* ndipo akazi onsewo anamuberekera ana aamuna, koma mwana woyamba kubadwa ndi wa mkazi wosakondedwayo,+ 16  pa tsiku limene adzagawe cholowa kwa ana ake aamuna, sadzaloledwa kutenga mwana wamwamuna wa mkazi wokondedwa uja ngati mwana wake woyamba kubadwa mʼmalo mwa mwana wamwamuna wa mkazi wosakondedwayo, amene ndi woyamba kubadwa. 17  Azivomereza kuti mwana wamwamuna wa mkazi wake wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa, pomupatsa magawo awiri pa chilichonse chimene ali nacho chifukwa iye ndi chiyambi cha mphamvu zake zobereka. Mwana ameneyo ndi amene ali woyenera kulandira udindo wa mwana woyamba kubadwa.+ 18  Ngati munthu ali ndi mwana wamwamuna wosamvera komanso wopanduka, amene samvera bambo ake kapena mayi ake,+ ndipo ayesetsa kumulangiza koma amakana kuwamvera,+ 19  bambo ake ndi mayi ake azimugwira nʼkupita naye kwa akulu kugeti la mzinda wawo, 20  ndipo aziuza akulu amzindawo kuti, ‘Mwana wathuyu ndi wosamva komanso ndi wopanduka ndipo amakana kutimvera. Ndi wosusuka+ komanso ndi chidakwa.’+ 21  Kenako amuna onse a mumzinda wawo azimuponya miyala nʼkumupha. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu, ndipo Aisiraeli onse adzamva nʼkuchita mantha.+ 22  Ngati munthu wachita tchimo loyenera chiweruzo choti aphedwe,+ ndiyeno munthuyo waphedwa, ndipo mwamupachika pamtengo,+ 23  mtembo wake usamakhale pamtengopo usiku wonse.+ Mʼmalomwake, muzionetsetsa kuti mwamuika mʼmanda tsiku lomwelo, chifukwa munthu aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.+ Musamaipitse dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kukhwawa limene lili.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ali ndi akazi awiri, mmodzi amamukonda ndipo winayo amadana naye.”