Deuteronomo 27:1-26

  • Akalembe Chilamulo pamiyala (1-10)

  • Paphiri la Ebala ndi paphiri la Gerizimu (11-14)

  • Anatchulanso matemberero (15-26)

27  Ndiyeno Mose pamodzi ndi akulu a Isiraeli analamula anthuwo kuti: “Muzisunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero.  Ndipo tsiku limene muwoloke Yorodano nʼkulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, mukaimike miyala ikuluikulu nʼkuipanga pulasitala.*+  Kenako mukakawoloka, mukalembe pamiyalapo mawu onse a mʼChilamulo ichi, kuti mulowe mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, mogwirizana ndi zimene Yehova, Mulungu wa makolo anu anakulonjezani.+  Mukawoloka Yorodano, mukaimike miyala imeneyi paphiri la Ebala,+ ndipo mukaipange pulasitala,* mogwirizana ndi zimene ndikukulamulani lero.  Komanso mukamangire Yehova Mulungu wanu guwa lansembe kumeneko, guwa lansembe lamiyala. Musakaseme miyalayo ndi chipangizo chilichonse chachitsulo.+  Mukagwiritse ntchito miyala yathunthu pomangira Yehova Mulungu wanu guwa lansembe, ndipo mukapereke nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu paguwalo.  Mukapereke nsembe zamgwirizano+ nʼkuzidyera pamenepo,+ ndipo mukasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+  Ndipo mukalembe moonekera bwino pamiyalayo mawu onse a mʼChilamulo chimenechi.”+  Kenako Mose komanso ansembe omwe ndi Alevi analankhula ndi Aisiraeli onse kuti: “Aisiraeli inu, khalani chete ndi kumvetsera. Lero mwakhala anthu a Yehova Mulungu wanu.+ 10  Muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo+ ndi malangizo ake, amene ndikukupatsani lero.” 11  Tsiku limenelo Mose analamula anthuwo kuti: 12  “Mukawoloka Yorodano, mafuko otsatirawa ndi amene adzaimirire paphiri la Gerizimu+ nʼkudalitsa anthu: Fuko la Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13  Ndipo mafuko otsatirawa ndi amene adzaimirire paphiri la Ebala+ kuti azidzavomereza matemberero akamadzatchulidwa: Fuko la Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafitali. 14  Ndipo Alevi azidzalankhula mokweza kwa anthu onse a mu Isiraeli kuti:+ 15  ‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wopanga chifaniziro chosema+ kapena chifaniziro chachitsulo+ nʼkuchibisa.* Chifanizirocho, chomwe ndi ntchito ya manja a mmisiri waluso,* ndi chonyansa kwa Yehova.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’*) 16  ‘Wotembereredwa ndi munthu wonyoza bambo ake kapena mayi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 17  ‘Wotembereredwa ndi munthu wosuntha chizindikiro cha malire a mnzake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 18  ‘Wotembereredwa ndi munthu wosocheretsa munthu amene ali ndi vuto losaona.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 19  ‘Wotembereredwa ndi munthu wopotoza chiweruzo cha mlendo+ amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 20  ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mkazi wa bambo ake, chifukwa wachititsa manyazi bambo akewo.’*+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 21  ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi nyama iliyonse.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 22  ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mchemwali wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 23  ‘Wotembereredwa ndi mwamuna wogona ndi apongozi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 24  ‘Wotembereredwa ndi munthu wobisalira mnzake nʼkumupha.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 25  ‘Wotembereredwa ndi munthu wolandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 26  ‘Wotembereredwa ndi munthu amene sadzatsatira mawu a mʼChilamulo ichi ndipo sadzawagwiritsa ntchito.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’”)

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nʼkuipaka laimu woyera.”
Kapena kuti, “mukaipake laimu woyera.”
Kapena kuti, “Ame!” mʼChiheberi.
Kapena kuti, “waluso pa ntchito za matabwa ndi zitsulo.”
Kapena kuti, “fano lachitsulo chosungunula nʼkulibisa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wavula bambo ake.”