Deuteronomo 28:1-68

  • Madalitso chifukwa chomvera (1-14)

  • Matemberero chifukwa chosamvera (15-68)

28  “Mukamveradi mawu a Yehova Mulungu wanu poonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani ndithu pamwamba pa mitundu yonse ya padziko lapansi.+  Mudzalandira madalitso onsewa ndipo zinthu zabwino zonsezi zidzakhala zanu,+ mukapitiriza kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu:  Mudzakhala odalitsika mumzinda, komanso mudzakhala odalitsika mʼmunda.+  Ana anu+ adzakhala odalitsika* komanso chipatso cha mʼdziko lanu, ana a ziweto zanu, ana a ngʼombe zanu ndi ana a nkhosa zanu adzakhala odalitsika.+  Dengu+ lanu komanso chiwiya chanu chokandiramo ufa, zidzakhala zodalitsika.+  Mudzakhala odalitsika pa zochita zanu zonse.  Yehova adzachititsa adani anu amene adzakuukireni kugonja pamaso panu.+ Pobwera kudzakuukirani adzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso panu, adzadutsa njira zosiyanasiyana 7.+  Yehova adzadalitsa nyumba zanu zosungiramo zinthu+ komanso chilichonse chimene mukuchita ndipo adzakudalitsani mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.  Yehova adzakupangani kukhala anthu ake oyera,+ mogwirizana ndi zimene analumbira kwa inu,+ chifukwa mukupitiriza kusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu ndipo mukuyenda mʼnjira zake. 10  Anthu onse padziko lapansi adzaona kuti mukutchedwa ndi dzina la Yehova,+ ndipo adzachita nanu mantha.+ 11  Yehova adzakupatsani ana ambiri komanso ziweto zochuluka ndipo nthaka+ yamʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani, idzabereka zipatso zambiri.+ 12  Yehova adzakutsegulirani kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatseni mvula pa nyengo yake+ mʼdziko lanu ndi kudalitsa chilichonse chimene mukuchita. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inuyo simudzafunika kukongola kanthu kwa iwo.+ 13  Yehova adzakuchititsani kuti mukhale mutu osati mchira ndipo mudzakhala pamwamba+ osati mʼmunsi, mukapitiriza kumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero kuti muziwasunga ndi kuwatsatira. 14  Musapatuke nʼkusiya kutsatira mawu onse amene ndikukulamulani lero, kupita kudzanja lamanja kapena lamanzere+ kuti mutsatire milungu ina nʼkuitumikira.+ 15  Koma mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu poonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mudzatembereredwa ndipo zinthu zoipa zotsatirazi zidzakuchitikirani:+ 16  Mudzakhala otembereredwa mumzinda komanso mudzakhala otembereredwa mʼmunda.+ 17  Dengu+ lanu komanso chiwiya chanu chokandiramo ufa zidzakhala zotembereredwa.+ 18  Ana anu adzakhala otembereredwa*+ komanso chipatso cha nthaka yanu, ana a ngʼombe zanu ndi ana a nkhosa zanu adzakhala otembereredwa.+ 19  Mudzakhala otembereredwa pa zochita zanu zonse. 20  Yehova adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndi chilango pa chilichonse chimene mukuchita mpaka mutawonongedwa nʼkutha mofulumira, chifukwa cha zinthu zoipa zimene mukuchita komanso chifukwa choti mwandisiya.+ 21  Yehova adzachititsa kuti matenda akukakamireni mpaka atakufafanizani mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+ 22  Yehova adzakulangani ndi chifuwa chachikulu, kutentha kwa thupi koopsa,+ kutupa, nyengo yotentha,* lupanga,+ mphepo yotentha yowononga mbewu ndi matenda a mbewu.+ Zimenezi zidzakuvutitsani mpaka mutatheratu. 23  Thambo limene lili pamwamba pa mutu wanu lidzakhala ngati kopa,* ndipo nthaka yanu idzakhala ngati chitsulo.+ 24  Yehova adzakugwetserani mchenga ndi fumbi ngati mvula mʼdziko lanu. Adzakugwetserani zimenezi kuchokera kumwamba mpaka mutawonongedwa. 25  Yehova adzachititsa kuti adani anu akugonjetseni.+ Popita kukawaukira mudzadutsa njira imodzi, koma pothawa mudzadutsa njira zosiyanasiyana 7. Mafumu onse a dziko lapansi adzachita mantha akadzaona zinthu zoipa zimene zakuchitikirani.+ 26  Mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse zouluka mumlengalenga ndi zilombo zoyenda panthaka, ndipo sipadzapezeka woziopseza.+ 27  Yehova adzakulangani ndi zithupsa za ku Iguputo, matenda a mudzi,* ziwengo ndi zotupa, ndipo simudzachira matenda amenewa. 28  Yehova adzakulangani ndi misala, khungu+ ndipo adzakuchititsani kuti musokonezeke. 29  Mudzapapasapapasa masana ngati mmene munthu wavuto losaona amapapasira mumdima,+ ndipo chilichonse chimene mudzachite sichidzakuyenderani bwino. Nthawi zonse anthu azidzakuberani mwachinyengo komanso kukulandani zinthu zanu popanda wokupulumutsani.+ 30  Mudzalonjeza kukwatira mkazi koma mwamuna wina adzamugwiririra. Mudzamanga nyumba koma simudzakhalamo.+ Mudzadzala mitengo ya mpesa koma simudzadya zipatso zake.+ 31  Ngʼombe yanu idzaphedwa inu mukuona, koma simudzadya nyama yake. Bulu wanu adzabedwa inu mukuona ndipo simudzamuonanso. Nkhosa yanu idzaperekedwa kwa adani anu ndipo sipadzakhala wokupulumutsani. 32  Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzaperekedwa kwa anthu ena+ inu mukuona ndipo nthawi zonse mudzalakalaka mutawaona, koma manja anu adzakhala opanda mphamvu. 33  Anthu amene simukuwadziwa adzadya zipatso zamʼdziko lanu ndi mbewu zanu zonse+ ndipo nthawi zonse muzidzaberedwa mwachinyengo komanso kuponderezedwa. 34  Mudzasokonezeka mutu chifukwa cha zimene maso anu adzaone. 35  Yehova adzakulangani ndi zithupsa zopweteka komanso zosachiritsika mʼmawondo ndi miyendo yanu. Matendawa adzayambira kumapazi mpaka paliwombo. 36  Yehova adzakuthamangitsani limodzi ndi mfumu yanu imene mudzaike kuti izikulamulirani, kukupititsani ku mtundu umene inuyo kapena makolo anu sanaudziwe.+ Kumeneko mudzatumikira milungu ina, milungu yamtengo ndi yamwala.+ 37  Anthu adzachita mantha akadzaona zimene zakuchitikirani ndipo mudzatonzedwa ndi kunyozedwa pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene Yehova akukuthamangitsirani.+ 38  Mudzadzala mbewu zambiri mʼmunda, koma mudzakolola zochepa+ chifukwa dzombe lidzadya mbewuzo. 39  Mudzalima nʼkudzala mitengo ya mpesa, koma simudzakolola mphesa zake nʼkumwa vinyo,+ chifukwa mbozi zidzadya mpesawo. 40  Mudzakhala ndi mitengo ya maolivi mʼdera lanu lonse, koma simudzadzola mafuta chifukwa maolivi anu adzayoyoka. 41  Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi, koma sadzakhala anu chifukwa adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 42  Tizilombo timene timakhala tambirimbiri tidzawononga mitengo yanu yonse ndi zipatso za mʼdziko lanu. 43  Mlendo amene akukhala pakati panu adzapitiriza kukhala wamphamvu, koma inuyo mphamvu zanu zidzapitiriza kucheperachepera. 44  Iye adzakukongozani zinthu koma inuyo simudzatha kumukongoza.+ Iye adzakhala mutu koma inuyo mudzakhala mchira.+ 45  Matemberero onsewa+ adzakugwerani ndipo zinthu zoipa zonsezi zidzakuchitikirani mpaka mutawonongedwa,+ chifukwa simunamvere mawu a Yehova Mulungu wanu posunga malamulo ndi malangizo amene anakupatsani.+ 46  Matembererowa adzapitiriza kugwera inu ndi ana anu ngati chizindikiro komanso chenjezo kwa inu mpaka kalekale,+ 47  chifukwa chakuti simunatumikire Yehova Mulungu wanu mokondwera komanso ndi mtima wosangalala, pamene munali ndi chilichonse komanso zinthu zochuluka.+ 48  Yehova adzakutumizirani adani anu kuti akuukireni ndipo mudzawatumikira+ muli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso mukusowa chilichonse. Iye adzakuvekani goli lachitsulo mʼkhosi lanu mpaka atakuwonongani. 49  Yehova adzatumiza mtundu wakutali+ kuchokera kumalekezero adziko lapansi kuti udzakuukireni. Mtunduwo udzakuukirani mofulumira kwambiri ngati mmene chiwombankhanga chimagwirira nyama.+ Mtundu umenewo chilankhulo chake simudzachimva,+ 50  mtundu wooneka moopsa umene sudzamvera chisoni munthu wachikulire kapena kuchitira chifundo mnyamata.+ 51  Iwo adzadya ana a ziweto zanu ndi zipatso za nthaka yanu mpaka mutawonongedwa. Sadzakusiyirani mbewu iliyonse, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ngʼombe kapena mwana wa nkhosa mpaka atakuwonongani.+ 52  Adzakuzungulirani nʼkukutsekerani mʼmizinda yanu* mʼdziko lanu lonse, mpaka mipanda yanu yaitali ndi yolimba kwambiri imene mukuidalira itagwa. Adzakuzungulirani ndithu mʼmizinda yanu yonse mʼdziko lanu limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 53  Zikadzatero mudzadya ana anu omwe,* mnofu wa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi+ amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzakuzungulirani. 54  Ngakhale mwamuna amene ndi wachifundo komanso wofatsa pakati panu, sadzachitira chisoni mchimwene wake, mkazi wake wokondedwa ndi ana ake aamuna amene atsala, 55  ndipo sadzagawana nawo mnofu uliwonse wa ana ake aamuna amene adzawadye, popeza adzakhala alibiretu china chilichonse chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzazungulira mizinda yanu.+ 56  Ndipo mkazi amene anakulira moyo wofewa komanso wachisasati pakati panu, amene sanayambe waganizapo zopondetsa phazi lake pansi chifukwa chokulira moyo wofewa, sadzamvera chisoni mwamuna wake wokondedwa,+ mwana wake wamwamuna komanso mwana wake wamkazi. 57  Iye sadzafuna kugawana nawo zotuluka mʼmimba mwake pambuyo pobereka komanso mnofu wa ana ake aamuna amene wabereka, popeza adzawadya mobisa chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzazungulira mizinda yanu. 58  Ngati simudzatsatira mosamala mawu onse a Chilamulo ichi amene alembedwa mʼbuku ili,+ ndipo ngati simudzaopa dzina laulemerero ndi lochititsa manthali,+ dzina la Yehova+ Mulungu wanu, 59  Yehova adzabweretsa miliri yoopsa pa inu ndi ana anu. Miliri imeneyo idzakhala yaikulu kwambiri ndi yokhalitsa,+ ndipo mudzagwidwa ndi matenda oopsa komanso okhalitsa. 60  Adzakubweretserani matenda onse a ku Iguputo amene munkachita nawo mantha, ndipo simudzachira. 61  Kuwonjezera pamenepo, Yehova adzakubweretserani matenda aliwonse ndi mliri uliwonse umene sunalembedwe mʼbuku la Chilamulo ili, mpaka mutawonongedwa. 62  Ngakhale kuti mwachuluka ngati nyenyezi zakumwamba,+ mudzatsala ochepa+ chifukwa chakuti simunamvere mawu a Yehova Mulungu wanu. 63  Mofanana ndi mmene Yehova anasangalalira kuchititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuchititsa kuti muchuluke, Yehova adzasangalalanso kuti akuwonongeni nʼkukufafanizani, ndipo mudzatheratu mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu. 64  Yehova adzakubalalitsirani pakati pa mitundu yonse, kuchokera kumalekezero a dziko mpaka kumalekezero ena a dziko.+ Kumeneko mudzatumikira milungu yamtengo komanso milungu yamwala, imene inuyo kapena makolo anu sanaidziwe.+ 65  Mudzasowa mtendere pakati pa mitundu imeneyo,+ ndipo simudzapeza malo oti phazi lanu liponde kuti lipume. Mʼmalomwake, Yehova adzakupatsani mtima wankhawa,+ adzachititsa kuti maso anu aziona movutikira ndipo adzakuchititsani kuti mutaye mtima.+ 66  Moyo wanu udzakhala pangozi yaikulu koopsa, ndipo mudzakhala mwamantha usiku ndi masana, moti simudzakhala wotsimikiza ngati mudzakhalebe ndi moyo. 67  Mʼmawa mudzanena kuti, ‘Zikanakhala bwino akanakhala madzulo!’ ndipo madzulo mudzanena kuti, ‘Zikanakhala bwino ukanakhala mʼmawa!’ chifukwa cha mantha amene adzagwire mtima wanu, ndiponso chifukwa cha zimene maso anu adzaone. 68  Yehova adzakubwezerani ku Iguputo pasitima kudzera njira imene ndinakuuzani kuti, ‘Simudzaionanso.’ Kumeneko mudzalakalaka kudzigulitsa kwa adani anu kuti mukhale akapolo aamuna ndi aakazi, koma sipadzakhala wokugulani.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chipatso cha mimba yanu chidzakhala chodalitsika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Chipatso cha mimba yanu chidzakhala chotembereredwa.”
Mawu a Chiheberi angatanthauzenso kutentha kwa thupi.
Kapena kuti, “mkuwa.”
Matendawa amachititsa kuti munthu atupe kotulukira chimbudzi ndipo nthawi zina amatha kutuluka thumbo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chipatso cha mimba yanu.”