Deuteronomo 3:1-29

  • Anagonjetsa Mfumu Ogi ya ku Basana (1-7)

  • Malire a dziko kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano (8-20)

  • Yoswa anauzidwa kuti asachite mantha (21, 22)

  • Mose sadzalowa mʼdziko (23-29)

3  “Ndiyeno tinatembenuka nʼkulowera Njira ya ku Basana. Ndipo Ogi mfumu ya ku Basana anabwera limodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nafe ku Edirei.+  Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Usamuope ameneyu, chifukwa ndipereka iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse komanso dziko lake mʼmanja mwako. Umuchite zimene unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala ku Hesiboni.’  Choncho Yehova Mulungu wathu anaperekanso Ogi mfumu ya Basana ndi anthu ake onse mʼmanja mwathu, ndipo tinawapha moti panalibe munthu ngakhale mmodzi mwa anthu ake, yemwe anapulumuka.  Kenako tinalanda mizinda yake yonse. Panalibe mzinda umene sitinaulande. Tinalanda mizinda 60 mʼchigawo chonse cha Arigobi, mʼdera lonse la ufumu wa Ogi ku Basana.+  Mizinda yonseyi inali yamipanda yolimba yomwe inali ndi makoma aatali, zitseko ndiponso mipiringidzo. Tinalandanso matauni ambirimbiri akumidzi.  Koma mizinda yonseyo tinaiwononga+ ngati mmene tinachitira ndi Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni, tinawononga mzinda uliwonse kuphatikizapo amuna, akazi ndi ana.+  Ndipo tinatenga ziweto ndi zinthu zonse zamʼmizindayo.  Pa nthawi imeneyo tinalanda dziko la mafumu awiri a Aamori+ amene ankakhala mʼdera la Yorodano, kuyambira mʼchigwa cha Arinoni* mpaka kuphiri la Herimoni.+  (Phiri limeneli Asidoni ankalitchula kuti Sirioni, pamene Aamori ankalitchula kuti Seniri.) 10  Tinalanda mizinda yonse yakudera lokwererapo, mʼGiliyadi monse, mʼBasana monse, mpaka ku Saleka ndi ku Edirei,+ mizinda imene inali mu ufumu wa Ogi ku Basana. 11  Ogi mfumu ya ku Basana ndi amene anali womaliza pa Arefai amene anatsala. Chithatha chimene* anaikapo mtembo wake chinali chachitsulo ndipo mpaka pano chidakali ku Raba wa Aamoni. Mulitali mwake nʼchokwana masentimita 401,* ndipo mulifupi mwake masentimita 178,* potengera muyezo umene unakhazikitsidwa. 12  Pa nthawi imeneyo tinatenga dzikoli kukhala lathu kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli mʼchigwa cha Arinoni* ndi hafu ya dera lamapiri la Giliyadi. Ndipo ndinapereka mizinda yake kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi.+ 13  Mbali yotsala ya dera la Giliyadi ndi Basana yense amene anali mu ufumu wa Ogi ndinaipereka kwa hafu ya fuko la Manase.+ Dera lonse la Arigobi, limene ndi mbali ya Basana linkadziwika kuti ndi dziko la Arefai. 14  Yairi+ mwana wamwamuna wa Manase anatenga dera lonse la Arigobi+ mpaka kumalire a Agesuri ndi a Amaakati.+ Midzi ya ku Basana imeneyo anaipatsa dzina lofanana ndi lake lakuti, Havoti-yairi*+ ndipo imadziwika ndi dzina limeneli mpaka pano. 15  Makiri ndinamupatsa dera la Giliyadi.+ 16  Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi kukafika kuchigwa cha Arinoni,* ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a Aamoni. 17  Ndinawapatsanso Araba, mtsinje wa Yorodano ndi malo amʼmbali mwa mtsinjewo, kuchokera ku Kinereti* mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere* imene ili mʼmunsi mwa zitunda za Pisiga, chakumʼmawa.+ 18  Pa nthawi imeneyo ndinakulamulani kuti: ‘Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli kuti mulitenge kukhala lanu. Amuna onse olimba mtima atenge zida ndipo awoloke patsogolo pa abale anu, Aisiraeli.+ 19  Akazi anu okha ndi ana anu ndi amene atsale mʼmizinda imene ndakupatsani. Ziweto zanunso zitsale (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri), 20  mpaka Yehova atapereka mpumulo kwa abale anu, ngati mmene wachitira ndi inu ndiponso mpaka iwo atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa tsidya linalo la Yorodano. Mukatero mudzabwerera, aliyense kumalo ake amene ndakupatsani.’+ 21  Pa nthawi imeneyo ndinalamula Yoswa+ kuti: ‘Iwe waona ndi maso ako zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachitira mafumu awiriwa. Yehova adzachitanso chimodzimodzi ndi maufumu onse amene ali kumene mukuwolokera kukamenyana nawo.+ 22  Musawaope amenewo, chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akukumenyerani nkhondo.’+ 23  Pa nthawi imeneyo ndinachonderera Yehova kuti, 24  ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mwayamba kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu.+ Ndi mulungu winanso uti, kumwamba kapena padziko lapansi, amene amachita ntchito zamphamvu ngati inu?+ 25  Ndiloleni chonde ndiwoloke, kuti ndione dziko labwino limene lili kutsidya kwa Yorodano, dera lamapiri labwinoli komanso Lebanoni.’+ 26  Koma Yehova anapitiriza kundikwiyira chifukwa cha inu,+ ndipo sanandimvere. Mʼmalomwake Yehova anandiuza kuti, ‘Basi khala chete! Usadzandiuzenso nkhani imeneyi. 27  Kwera pamwamba pa Pisiga+ ndipo ukayangʼane kumadzulo, kumpoto, kumʼmwera ndi kumʼmawa kuti ukaone dzikolo ndi maso ako, chifukwa suwoloka Yorodano uyu.+ 28  Uike Yoswa+ kuti akhale mtsogoleri ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa mtima chifukwa ndi amene adzawolotse+ anthuwa ndi kuwachititsa kulandira dziko limene ulionelo kukhala cholowa chawo.’ 29  Zonsezi zinachitika tili mʼchigwa moyangʼanizana ndi Beti-peori.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “khwawa la Arinoni.”
Kapena kuti, “bokosi limene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 4.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 9.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa la Arinoni.”
Kutanthauza, “Midzi ya Matenti ya Yairi.”
Kapena kuti, “kukhwawa la Arinoni.”
“Kinereti” linali dzina loyambirira la Nyanja ya Galileya.
Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.