Deuteronomo 30:1-20
30 “Mawu onsewa akadzakwaniritsidwa pa inu, madalitso ndi matemberero amene ndaika pamaso panu,+ ndipo mukadzawakumbukira*+ muli ku mitundu yonse kumene Yehova Mulungu wanu adzakubalalitsireni,+
2 inu nʼkubwerera kwa Yehova Mulungu wanu+ komanso kumvera mawu ake ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, mogwirizana ndi zonse zimene ndikukulamulani lero, inuyo ndi ana anu,+
3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+
4 Ngakhale anthu a mtundu wanu amene anabalalitsidwawo atadzakhala kumalekezero kwa thambo, Yehova Mulungu wanu adzakusonkhanitsani nʼkukubweretsani kuchokera kumeneko.+
5 Yehova Mulungu wanu adzakubweretsani mʼdziko limene makolo anu analitenga kuti likhale lawo, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino ndipo adzakuchulukitsani kwambiri kuposa makolo anu.+
6 Yehova Mulungu wanu adzayeretsa* mitima yanu ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse ndipo mudzakhala ndi moyo.+
7 Ndiyeno Yehova Mulungu wanu adzabweretsa matemberero onsewa pa adani anu, amene ankadana nanu komanso kukuzunzani.+
8 Kenako inu mudzabwerera nʼkumvera mawu a Yehova komanso kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero.
9 Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino kwambiri pa ntchito iliyonse ya manja anu.+ Adzachulukitsa ana anu, ziweto zanu ndi zokolola zanu, chifukwa Yehova adzasangalalanso kuchititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino, ngati mmene anachitira ndi makolo anu.+
10 Chifukwa pa nthawiyo mudzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo komanso malangizo ake amene analembedwa mʼbuku ili la Chilamulo, ndipo mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse.+
11 Lamulo limene ndikukupatsani leroli si lovuta kwa inu kulitsatira, ndipo silili poti simungathe kulipeza.*+
12 Silili kumwamba kuti munene kuti, ‘Ndani adzapite kumwamba kuti akatitengere lamulolo kuti ife tidzalimve nʼkulitsatira?’+
13 Ndiponso silili tsidya lina la nyanja kuti munene kuti, ‘Ndani adzawoloke kupita tsidya lina la nyanja kuti akatitengere lamulolo kuti ife tidzalimve nʼkulitsatira?’
14 Chifukwa mawu a chilamulowo ali pafupi kwambiri ndi inu, ali mʼkamwa mwanu ndi mumtima mwanu+ kuti muwatsatire.+
15 Taonani, ine ndikuika pamaso panu lero moyo ndi zinthu zabwino, imfa ndi zinthu zoipa.+
16 Mukadzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero, pokonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda mʼnjira zake ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake ndi zigamulo zake, mudzakhala ndi moyo,+ mudzachulukana ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+
17 Koma mtima wanu ukatembenukira kwina+ ndipo simukumvera, moti mwakopeka nʼkugwadira milungu ina ndi kuitumikira,+
18 ndikukuuzani lero kuti mudzatheratu.+ Simudzakhala nthawi yaitali mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu mutawoloka Yorodano.
19 Lero ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu. Choncho inuyo ndi mbadwa zanu+ musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.+
20 Musankhe moyo pokonda Yehova Mulungu wanu,+ kumvera mawu ake ndi kukhala okhulupirika kwa iye,+ chifukwa iye ndi amene amapereka moyo ndipo angakuthandizeni kuti mukhale ndi moyo kwa nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzalipereka kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.”+