Deuteronomo 31:1-30
31 Kenako Mose anapita kukauza Aisiraeli onse mawu awa,
2 kuti: “Tsopano ndili ndi zaka 120.+ Sindingathenso kukutsogolerani* chifukwa Yehova wandiuza kuti, ‘Suwoloka Yorodano uyu.’+
3 Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu kuti akutsogolereni. Iye adzawononga mitundu imeneyi pamaso panu ndipo inu mudzaithamangitsa.+ Yoswa ndi amene akutsogolereni nʼkukuwolotsani,+ mogwirizana ndi zimene Yehova wanena.
4 Yehova adzachitira mitundu imeneyi zimene anachitira Sihoni+ ndi Ogi,+ mafumu a Aamori, ndiponso zimene anachitira dziko lawo pamene anawawononga.+
5 Yehova adzakugonjetserani mitundu imeneyi, ndipo mudzaichitire mogwirizana ndi malamulo onse amene ndakupatsani.+
6 Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pangʼono.”+
7 Kenako Mose anaitana Yoswa nʼkumuuza pamaso pa Aisiraeli onse kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iwe ndi amene udzalowetse anthu awa mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo awo kuti adzawapatsa. Ndipo iwe ndi amene udzawagawire dzikolo kuti likhale cholowa chawo.+
8 Yehova ndi amene akuyenda patsogolo panu ndipo apitiriza kuyenda nanu.+ Sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pangʼono. Choncho musaope kapena kuchita mantha.”+
9 Kenako Mose analemba Chilamulo+ chimenechi nʼkuchipereka kwa ansembe, omwe ndi Alevi, amene amanyamula likasa la pangano la Yehova, komanso kwa akulu onse a Isiraeli.
10 Ndiyeno Mose anawalamula kuti: “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse, pa nthawi imene inaikidwiratu mʼchaka choti anthu angongole amasuke,+ Pachikondwerero cha Misasa,+
11 Aisiraeli onse akabwera pamaso pa Yehova+ Mulungu wanu pamalo amene iye adzasankhe, muzidzawerenga Chilamulo ichi pamaso pa Aisiraeli onse kuti achimve.+
12 Sonkhanitsani anthu,+ amuna, akazi, ana ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu,* kuti amvetsere komanso kuti aphunzire zokhudza Yehova Mulungu wanu, kuti azimuopa ndiponso kuti azitsatira mosamala mawu onse a mʼChilamulo ichi.
13 Akatero ana awo amene sakudziwa Chilamulo ichi adzamvetsera+ ndipo adzaphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse amene mudzakhale mʼdziko limene mukuwoloka Yorodano kukalitenga kuti likhale lanu.”+
14 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Taona, nthawi yoti ufe yayandikira.+ Itana Yoswa, ndipo mukaime pachihema chokumanako kuti ndikamuike kukhala mtsogoleri.”+ Choncho Mose ndi Yoswa anapita nʼkukaima pachihema chokumanako.
15 Ndiyeno Yehova anaonekera kuchihemako mʼchipilala cha mtambo chimene chinaima pafupi ndi khomo la chihema.+
16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa,* ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+
17 Pa nthawi imeneyo mkwiyo wanga udzawayakira+ ndipo ndidzawasiya+ nʼkuwabisira nkhope yanga+ mpaka atawonongedwa.+ Ndiyeno akadzakumana ndi masoka komanso mavuto ambiri adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+
18 Koma ine ndidzapitiriza kuwabisira nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoipa zonse zimene achita, potembenukira kwa milungu ina.+
19 Tsopano mulembe nyimbo iyi+ nʼkuphunzitsa Aisiraeli.+ Muwaphunzitse* nyimbo imeneyi kuti ikhale mboni yanga pamaso pa Aisiraeliwo.+
20 Ndikadzawalowetsa mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo awo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ ndipo akadzadya nʼkukhuta, zinthu nʼkuyamba kuwayendera bwino,*+ adzatembenukira kwa milungu ina nʼkuyamba kuitumikira. Iwo adzandichitira mwano komanso kuphwanya pangano langa.+
21 Ndiyeno akadzakumana ndi masoka komanso mavuto ambiri,+ nyimboyi idzawakumbutsa zimene ndinawachenjeza, (chifukwa mbadwa zawo sizikuyenera kuiwala nyimboyi), chifukwa ndikudziwa kale mtima umene ayamba kukhala nawo+ ndisanawalowetse nʼkomwe mʼdziko limene ndinawalumbirira.”
22 Choncho Mose analemba nyimboyi pa tsiku limenelo nʼkuphunzitsa Aisiraeli.
23 Ndiyeno Mulungu anaika Yoswa+ mwana wa Nuni kuti akhale mtsogoleri, ndipo anamuuza kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iwe ndi amene udzalowetse Aisiraeli mʼdziko limene ndawalumbirira,+ ndipo ine ndidzapitiriza kukhala ndi iwe.”
24 Mose atangomaliza kulemba mawu onse a Chilamulo ichi mʼbuku,+
25 Mose analamula Alevi amene amanyamula likasa la pangano la Yehova kuti:
26 “Tengani buku ili la Chilamulo+ ndipo muliike pambali pa likasa+ la pangano la Yehova Mulungu wanu, ndipo lidzakhala mboni ya Mulungu yokutsutsani.
27 Ineyo ndikudziwa bwino khalidwe lanu lopanduka+ ndi kuuma mtima* kwanu.+ Ngati mwakhala mukupandukira Yehova pamene ndili moyo, ndiye kuli bwanji pambuyo pa imfa yanga!
28 Sonkhanitsani akulu onse a mafuko anu ndi atsogoleri anu, kuti amve mawu awa amene ndikufuna kulankhula nawo, ndipo nditenge kumwamba ndi dziko lapansi kuti zikhale mboni zanga pamaso pawo.+
29 Chifukwa ndikudziwa bwino kuti pambuyo pa imfa yanga, mosakayikira mudzachita zinthu zoipa+ nʼkupatuka kusiya njira imene ndakulamulani. Ndiyeno pamapeto pake tsoka lidzakugwerani,+ chifukwa mudzachita zoipa pamaso pa Yehova ndipo mudzamukhumudwitsa ndi ntchito za manja anu.”
30 Choncho mpingo wonse wa Isiraeli ukumva, Mose anayamba kulankhula mawu a nyimbo iyi, kuchokera poyambirira mpaka kumapeto kuti:+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kutuluka ndi kulowa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kugona pamodzi ndi makolo ako.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Muiike mʼkamwa mwawo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkunenepa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kuuma khosi.”