Deuteronomo 33:1-29

  • Mose anadalitsa mafuko (1-29)

    • Manja a Yehova “omwe adzakhalapo mpaka kalekale” (27)

33  Tsopano awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu woona, ananena asanafe kuti Aisiraeli adzalandira.+  Iye anati: “Yehova anabwera kuchokera ku Sinai,+Anawala pa iwo kuchokera ku Seiri. Anawala mwa ulemerero kuchokera kudera lamapiri la Parana,+Ndipo anali ndi angelo ake ambirimbiri,*+Kudzanja lake lamanja kunali asilikali ake.+   Iye ankakonda anthu ake,+Anthu oyera onsewa ali mʼmanja mwanu.+ Iwowa anakhala pamapazi anu.+Anayamba kumvetsera mawu anu.+   (Mose anatipatsa chilamulo,+Chimene ndi chuma cha mpingo wa Yakobo.)+   Mulungu anakhala mfumu mu Yesuruni,*+Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana pamodzi,+Limodzi ndi mafuko onse a Isiraeli.+   Rubeni akhale ndi moyo ndipo asafe,+Ndipo anthu ake asakhale ochepa.”+   Iye ananena kuti Yuda adzalandira madalitso otsatirawa:+ “Inu Yehova, imvani mawu a Yuda,+Ndipo mumubwezere kwa anthu ake. Iye wateteza* zinthu zake ndi manja ake,Mumuthandize kulimbana ndi adani ake.”+   Ponena za Levi anati:+ “Tumimu ndi Urimu wanu*+ ndi za munthu wokhulupirika kwa inu,+Amene munamuyesa pa Masa.+ Munayamba kulimbana naye pafupi ndi madzi a ku Meriba.+   Munthu amene anauza bambo ndi mayi ake kuti, ‘Sindinasonyeze kuti ndikuwalabadira.’ Ngakhale abale ake sanawasamale,+Ndipo ana ake anakhala ngati sakuwadziwa. Chifukwa anatsatira mawu anu,Ndipo anasunga pangano lanu.+ 10  Amenewa azilangiza Yakobo pa zigamulo zanu+Ndi Isiraeli mʼChilamulo chanu.+ Azipereka nsembe zofukiza kuti zikhale kafungo kosangalatsa kwa inu,*+Ndi nsembe yathunthu paguwa lanu lansembe.+ 11  Inu Yehova dalitsani mphamvu zake,Ndipo mukondwere ndi ntchito ya manja ake. Muphwanye miyendo ya* amene akumuukira,Kuti amene amadana naye asathenso kuimirira.” 12  Ponena za Benjamini anati:+ “Wokondedwa wa Yehova azikhala wotetezedwa ndi iye,Pamene akumuteteza tsiku lonse,Iye adzakhala pakati pa mapewa ake.” 13  Ponena za Yosefe anati:+ “Dziko lake lidalitsidwe ndi Yehova.+Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri zakumwamba,Ndi mame komanso madzi ochokera mu akasupe a pansi pa nthaka.+ 14  Lidalitsidwenso ndi zinthu zabwino kwambiri, zochokera ku dzuwa,Ndi zokolola zabwino kwambiri mwezi uliwonse,+ 15  Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino koposa zamʼmapiri akale,*+Ndi zinthu zabwino kwambiri zamʼmapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale. 16  Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri za padziko lapansi, ndi chuma chake chonse,+Komanso movomerezedwa ndi Iye amene anaonekera mʼchitsamba chaminga.+ Madalitso amenewa akhale pamutu pa Yosefe,Paliwombo pa munthu amene anasankhidwa pakati pa abale ake.+ 17  Ulemerero wake ndi wofanana ndi wa mwana wa ngʼombe wamphongo woyamba kubadwa,Ndipo nyanga zake ndi nyanga za ngʼombe yamphongo yamʼtchire. Nyanga zimenezo adzakankha* nazo anthu.Adzakankha nazo anthu onse pamodzi mpaka kukafika kumalekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezo ndi anthu masauzande makumimakumi a fuko la Efuraimu,+Ndiponso anthu masauzande a fuko la Manase.” 18  Ponena za Zebuloni anati:+ “Kondwera Zebuloni iwe, pa maulendo ako,Ndiponso iwe Isakara, mʼmatenti ako.+ 19  Adzaitanira mitundu ya anthu kuphiri. Kumeneko adzapereka nsembe zachilungamo. Chifukwa adzatenga chuma* kuchokera pa chuma chochuluka cha mʼnyanja,Ndi chuma chobisika chamumchenga.” 20  Ponena za Gadi anati:+ “Wofutukula malire a dera la Gadi ndi wodala.+ Iye adzagona kumeneko ngati mkango,Wokonzeka kukhadzula dzanja, komanso kungʼamba mutu paliwombo. 21  Iye adzasankha gawo labwino kwambiri kuti likhale lake,+Chifukwa gawo loperekedwa ndi wopereka malamulo linasungidwa kumeneko.+ Atsogoleri a anthu adzasonkhana pamodzi. Iye adzachita chilungamo cha Yehova,Ndi zigamulo zake zokhudza Isiraeli.” 22  Ponena za Dani anati:+ “Dani ndi mwana wa mkango.+ Adzadumpha kuchokera ku Basana.”+ 23  Ponena za Nafitali anati:+ “Nafitali wakhutira chifukwa chovomerezedwa,Ndipo madalitso a Yehova amuchulukira. Tenga chigawo chakumadzulo ndi kumʼmwera.” 24  Ponena za Aseri anati:+ “Aseri anamudalitsa ndi ana aamuna. Abale ake amukomere mtima,Ndipo apondetse* mapazi ake mʼmafuta. 25  Chitsulo komanso kopa* ndi zokhomera geti lako,+Ndipo udzakhala wotetezeka masiku onse a moyo wako.* 26  Palibe amene angafanane ndi Mulungu woona+ wa Yesuruni,+Amene amayenda mumlengalenga kuti akuthandize,Amene amayenda pamitambo mu ulemerero wake.+ 27  Mulungu ndi malo ako othawirapo kuyambira kalekale,+Iye wakunyamula mʼmanja ake omwe adzakhalapo mpaka kalekale.+ Adzathamangitsa mdani pamaso pako,+Ndipo adzanena kuti, ‘Awonongeni!’+ 28  Isiraeli adzakhala motetezeka,Kasupe wa Yakobo adzakhala motetezeka,Mʼdziko lokhala ndi chakudya komanso vinyo watsopano,+Limene kumwamba kwake kudzagwetsa mame.+ 29  Ndiwe wosangalala iwe Isiraeli!+ Ndani angafanane ndi iwe,+Anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova,+Chishango chako chokuteteza,+Komanso lupanga lako lamphamvu? Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+Ndipo iwe udzaponda pamisana yawo.”*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anali ndi oyera ake masauzande masauzande.”
Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.
Kapena kuti, “wamenyera nkhondo.”
Mawu akuti “wanu” ndi “inu” akuimira Mulungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmphuno mwanu.”
Kapena kuti, “ziuno za.”
Mabaibulo ena amati, “mʼmapiri a kumʼmawa.”
Kapena kuti, “adzagunda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzayamwa chuma chochuluka.”
Kapena kuti, “asambitse.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mphamvu zako zidzafanana ndi masiku a moyo wako.”
Mabaibulo ena amati, “pamalo awo okwezeka.”