Deuteronomo 34:1-12

  • Yehova anaonetsa Mose dziko (1-4)

  • Imfa ya Mose (5-12)

34  Kenako Mose anachoka mʼchipululu cha Mowabu kupita mʼphiri la Nebo,+ pamwamba pa Pisiga,+ moyangʼanizana ndi Yeriko.+ Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse, kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.+  Anamuonetsanso dziko lonse la Nafitali, dziko la Efuraimu, dziko la Manase komanso dziko lonse la Yuda mpaka kunyanja yakumadzulo.*+  Anamuonetsa Negebu+ ndi Chigawo+ cha Yorodano kuphatikizapo chigwa cha Yeriko, mzinda wa mitengo ya kanjedza, mpaka ku Zowari.+  Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Ili ndi dziko limene ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzalipereka kwa mbadwa* zanu.’+ Ndakulola kuti ulione ndi maso ako, koma suwoloka kukalowa mʼdzikolo.”+  Kenako Mose mtumiki wa Yehova anafera pamenepo mʼdziko la Mowabu, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.+  Mulungu anamuika mʼmanda mʼchigwa, mʼdziko la Mowabu moyangʼanizana ndi Beti-peori, ndipo palibe amene akudziwa pamene pali manda ake mpaka lero.+  Mose anamwalira ali ndi zaka 120.+ Pa nthawiyo maso ake ankaonabe bwinobwino ndipo anali adakali ndi mphamvu.  Aisiraeli analira maliro a Mose kwa masiku 30 mʼchipululu cha Mowabu.+ Kenako masiku onse olira maliro a Mose anatha.  Yoswa mwana wa Nuni anali atadzazidwa ndi mzimu wa nzeru, chifukwa Mose anaika manja ake pa iye.+ Aisiraeli anayamba kumumvera ndipo anachita mogwirizana ndi zomwe Yehova analamula Mose.+ 10  Koma mu Isiraeli simunakhalenso mneneri aliyense wofanana ndi Mose,+ amene Yehova ankamudziwa bwino kwambiri.*+ 11  Iye anachita zizindikiro ndi zodabwitsa zonse zimene Yehova anamutuma kukachita mʼdziko la Iguputo kwa Farao, atumiki ake onse ndi mʼdziko lake lonse.+ 12  Mose anachita zimenezi ndi dzanja lamphamvu komanso mphamvu zazikulu pamaso pa Aisiraeli onse.+

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene Yehova ankamudziwa pamasomʼpamaso.”