Deuteronomo 7:1-26

  • Mitundu 7 yoyenera kuwonongedwa (1-6)

  • Chifukwa chimene anasankhira Aisiraeli (7-11)

  • Kumvera kumabweretsa madalitso (12-26)

7  “Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene mwatsala pangʼono kulitenga kuti likhale lanu,+ adzakuchotseraninso mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotserani Ahiti, Agirigasi, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu komanso yamphamvu kuposa inu.+  Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu ndipo mudzawagonjetsa.+ Mudzawawononge+ ndithu ndipo musadzachite nawo pangano lililonse kapena kuwakomera mtima.+  Musadzachite nawo mgwirizano uliwonse wa ukwati.* Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna ndipo musadzatenge ana awo aakazi nʼkuwapereka kwa ana anu aamuna.+  Chifukwa adzachititsa kuti ana anu aamuna asiye kunditsatira ndipo adzatumikira milungu ina.+ Ndiyeno mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani mofulumira.+  Koma inu mudzawachitire zotsatirazi: Mudzagwetse maguwa awo ansembe komanso kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mudzadule mizati yawo yopatulika+ ndi kuwotcha zifaniziro zawo zogoba.+  Chifukwa ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera, pa anthu onse okhala padziko lapansi.+  Sikuti Yehova anakusonyezani chikondi ndi kukusankhani+ chifukwa chakuti munali ochuluka kuposa mitundu yonse, chifukwatu mtundu wanu unali waungʼono mwa mitundu yonse.+  Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu kuti akulanditseni mʼnyumba yaukapolo,+ mʼmanja mwa Farao* mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani, komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.+  Inu mukudziwa bwino kuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu woona, Mulungu wokhulupirika, amene amasunga pangano lake ndiponso amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amamukonda ndi kusunga malamulo ake ku mibadwo 1,000.+ 10  Koma anthu amene amadana naye adzawabwezera powawononga.+ Iye sadzazengereza kupereka chilango kwa anthu amene amadana naye koma adzawabwezera powawononga. 11  Choncho muzionetsetsa kuti mukusunga malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene ndikukupatsani lero, pozitsatira. 12  Ngati mutapitiriza kumvera zigamulo zimenezi ndi kuzitsatira, Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano ndi kukusonyezani chikondi chokhulupirika, zimene analumbira kwa makolo anu. 13  Iye adzakukondani, kukudalitsani komanso kukuchulukitsani. Adzakudalitsani ndithu pokupatsani ana ambiri,*+ adzadalitsa zokolola za nthaka yanu, mbewu zanu, vinyo wanu watsopano, mafuta anu,+ ana a ngʼombe zanu ndi ana a nkhosa zanu, mʼdziko limene analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani.+ 14  Inu mudzakhala odalitsika kwambiri mwa anthu onse.+ Pakati panu sipadzapezeka mwamuna, mkazi kapena chiweto chosabereka.+ 15  Yehova adzakuchotserani matenda onse ndipo sadzakugwetserani matenda alionse oopsa amene munawaona ku Iguputo.+ Koma adzawagwetsera pa anthu onse amene amadana nanu. 16  Muwononge anthu a mitundu yonse amene Yehova Mulungu wanu akuwapereka kwa inu.+ Musawamvere chisoni+ ndipo musatumikire milungu yawo+ chifukwa kuchita zimenezo kudzakutcherani msampha.+ 17  Mukaganiza mumtima mwanu kuti, ‘Anthu a mitundu iyi ndi ambiri kuposa ife. Tingathe bwanji kuwathamangitsa?’+ 18  musawaope.+ Nthawi zonse muzikumbukira zimene Yehova Mulungu wanu anachitira Farao ndi Iguputo yense.+ 19  Muzikumbukira ziweruzo zamphamvu zimene* maso anu anaona, zizindikiro, zodabwitsa,+ dzanja lamphamvu ndiponso mkono wotambasula umene Yehova Mulungu wanu anagwiritsa ntchito pokutulutsani mʼdzikolo.+ Izi ndi zimene Yehova Mulungu wanu adzachite ndi anthu a mitundu yonse amene mukuwaopa.+ 20  Yehova Mulungu wanu adzachititsa mantha mitima yawo mpaka onse amene anatsala+ ndiponso amene anabisala pamaso panu atawonongedwa. 21  Musachite nawo mantha chifukwa Yehova Mulungu wanu, Mulungu wamphamvu komanso wochititsa mantha,+ ali pakati panu.+ 22  Yehova Mulungu wanu adzathamangitsira mitundu imeneyi kutali ndi inu, kuichotsa pamaso panu pangʼonopangʼono.+ Sadzakulolani kuti muiwononge mofulumira, kuopera kuti zilombo zakutchire zingachuluke nʼkukuwonongani. 23  Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu ndipo mudzawagonjetsa mobwerezabwereza mpaka onse atatha.+ 24  Adzapereka mafumu awo mʼmanja mwanu,+ ndipo inu mudzafafanize mayina awo padziko lapansi.+ Palibe munthu amene adzalimbane ndi inu+ mpaka mutawawononga.+ 25  Mudzawotche pamoto zifaniziro zogoba za milungu yawo.+ Musadzalakelake siliva ndi golide wawo kapena kutenga zinthu zimenezi kuti zikhale zanu,+ kuopera kuti zingakutchereni msampha, chifukwa zinthu zimenezi ndi zonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.+ 26  Musabweretse mʼnyumba mwanu zinthu zonyansa kuti nanunso musakhale oyenera kuwonongedwa mofanana ndi zinthuzo. Muzinyansidwa nazo kwambiri komanso kuipidwa nazo chifukwa zinthu zimenezi ndi zoyenera kuwonongedwa.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Musamakwatirane ndi anthu a mtundu wina.”
Kapena kuti, “ku mphamvu za Farao.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzadalitsa chipatso cha mimba yanu.”
Kapena kuti, “mayesero amphamvu amene.”