Ekisodo 10:1-29

  • Mliri wa 8: dzombe (1-20)

  • Mliri wa 9: mdima (21-29)

10  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao chifukwa ndalola kuti iye ndi atumiki ake aumitse mitima yawo,+ kuti ndichite zizindikiro zanga pamaso pake.+ 2  Ndachita zimenezi kuti mufotokozere ana anu ndi zidzukulu zanu mmene ndakhaulitsira Iguputo komanso zizindikiro zimene ndachitira Aiguputo.+ Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.” 3  Choncho Mose ndi Aroni anapita kwa Farao nʼkukamuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti, ‘Kodi upitiriza kukana kundigonjera mpaka liti?+ Lola anthu anga kuti apite kukanditumikira. 4  Ukapitiriza kukana kuti anthu anga apite, mawa ndikutumizira dzombe mʼdziko lako. 5  Dzombelo lidzakuta nthaka yonse ndipo simudzatha kuona dothi. Lidzadya chilichonse chotsalira komanso chilichonse chimene matalala sanawononge. Ndipo lidzadya mitengo yanu yonse imene yayamba kumera.+ 6  Dzombelo lidzadzaza mʼnyumba zanu, mʼnyumba zonse za atumiki anu ndi mʼnyumba za mu Iguputo monse. Lidzadzaza mʼnyumbazi mpaka kufika poti makolo anu ndi makolo a makolo anu sanaonepo chibadwire chawo.’”+ Atatero, Mose anachoka pamaso pa Farao. 7  Kenako atumiki a Farao anamuuza kuti: “Kodi munthu uyu apitiriza kutizunza* mpaka liti? Lolani anthuwa apite kuti akatumikire Yehova Mulungu wawo. Kodi simunazindikirebe kuti Iguputo wawonongeka?” 8  Choncho Farao anaitanitsa Mose ndi Aroni nʼkuwauza kuti: “Pitani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma ndi ndani kwenikweni amene apite?” 9  Ndiyeno Mose anati: “Tipita ndi achinyamata athu, achikulire athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe zathu,+ chifukwa tikukachitira Yehova chikondwerero.”+ 10  Farao anawauza kuti: “Ngati ndingalole kuti inu pamodzi ndi ana anu mupite, ndiye kuti Yehova alidi ndi inu.+ Ndikudziwa kuti mukufuna kuchita chinachake choipa. 11  Sizitheka! Amuna okha ndi amene apite kukatumikira Yehova, chifukwa ndi zimene munapempha.” Atanena zimenezi, anawachotsa pamaso pa Farao. 12  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako nʼkuloza dziko la Iguputo kuti dzombe ligwe mʼdziko lonselo nʼkudya zomera zonse zamʼdzikomo, chilichonse chimene matalala sanawononge.” 13  Zitatero Mose analoza dziko lonse la Iguputo ndi ndodo yake, ndipo Yehova anachititsa mphepo yochokera kumʼmawa kuwomba padziko lonselo, masana onse ndi usiku onse. Mʼmawa kutacha mphepoyo inabweretsa dzombe. 14  Dzombelo linafika mʼdziko lonse la Iguputo nʼkufalikira mʼmadera onse adzikolo+ ndipo linawononga kwambiri.+ Dzombe lambiri ngati limeneli linali lisanagwepo nʼkale lonse ndipo silidzagwanso lambiri ngati limeneli. 15  Dzombelo linakuta nthaka yonse yamʼdzikolo ndipo dziko linachita mdima. Dzombelo linadya zomera zonse zamʼdzikolo ndi zipatso zonse zamʼmitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala, moti sipanatsale chobiriwira chilichonse mʼmitengo kapena mʼminda mʼdziko lonse la Iguputo. 16  Ndiyeno Farao anaitanitsa Mose ndi Aroni mwamsanga nʼkuwauza kuti: “Ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso ndachimwira inu. 17  Chonde ndikhululukireni tchimo langa ulendo uno wokha, ndipo chondererani Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wakuphawu.” 18  Choncho iwo anachoka pamaso pa Farao ndipo anapita kukachonderera Yehova.+ 19  Atatero Yehova anachititsa kuti mphepo yamphamvuyo iziwomba kuchokera kumadzulo ndipo inatenga dzombelo nʼkukaliponya mʼNyanja Yofiira. Mʼdera lonse la Iguputo simunatsale dzombe ngakhale limodzi. 20  Komabe Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake+ moti sanalole kuti Aisiraeli achoke. 21  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza kumwamba kuti mʼdziko lonse la Iguputo mugwe mdima wandiweyani.” 22  Nthawi yomweyo, Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza kumwamba ndipo mʼdziko lonse la Iguputo munali mdima wandiweyani kwa masiku atatu.+ 23  Anthu sankatha kuonana ndipo palibe amene anachoka pamalo amene anali kwa masiku atatu. Koma kumene Aisiraeli ankakhala kunkawala.+ 24  Zitatero Farao anaitana Mose nʼkumuuza kuti: “Pitani, katumikireni Yehova.+ Koma nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu simupita nazo. Ana anunso mungathe kupita nawo.” 25  Koma Mose anati: “Inuyo mutipatse* nyama zokapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kuti tikazipereke kwa Yehova Mulungu wathu.+ 26  Ziweto zathu tipitanso nazo. Sitidzasiya chiweto* ngakhale chimodzi, chifukwa tikagwiritsa ntchito zina mwa ziweto zimenezi polambira Yehova Mulungu wathu. Koma panopa sitikudziwa kuti tikapereka chiyani polambira Yehova mpaka titakafika kumeneko.” 27  Choncho Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti Aisiraeli achoke.+ 28  Ndiyeno Farao anauza Mose kuti: “Choka pamaso panga! Uonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga, chifukwa tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.” 29  Ndipo Mose anayankha kuti: “Monga mwanenera, sindidzaonekeranso pamaso panu.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “apitiriza kukhala msampha kwa ife.”
Kapena kuti, “mutilole kutenga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chiboda.”