Ekisodo 13:1-22

  • Mwana wamwamuna woyamba kubadwa aliyense ndi wa Yehova (1, 2)

  • Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa (3-10)

  • Mwana wamwamuna woyamba kubadwa aliyense ankaperekedwa kwa Mulungu (11-16)

  • Aisiraeli anatsogoleredwa kupita ku Nyanja Yofiira (17-20)

  • Chipilala cha mtambo komanso cha moto (21, 22)

13  Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2  “Ndipatulireni* mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa,* wa munthu ndi wa chiweto, pakati pa Aisiraeli. Ameneyu ndi wanga.”+ 3  Kenako Mose anauza anthuwo kuti: “Muzikumbukira tsiku lalero limene mwatuluka mu Iguputo,+ mʼnyumba ya ukapolo, chifukwa Yehova wakutulutsani mʼdzikoli ndi dzanja lake lamphamvu.+ Choncho musadye chilichonse chokhala ndi zofufumitsa. 4  Mukutuluka mu Iguputo lero, mʼmwezi wa Abibu.*+ 5  Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ limene analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani,+ muzidzachita mwambo umenewu mʼmwezi uno. 6  Muzidzadya mikate yopanda zofufumitsa kwa masiku 7,+ ndipo pa tsiku la 7 muzidzachita chikondwerero kwa Yehova. 7  Muzidzadya mikate yopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+ Musamadzapezeke ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa.+ Ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa usamadzapezeke pena paliponse mʼdziko lanu. 8  Ndiyeno pa tsiku limenelo mudzauze ana anu kuti, ‘Tikuchita izi chifukwa cha zimene Yehova anatichitira potuluka mu Iguputo.’+ 9  Mwambowu ukhale ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu ndi pamphumi panu.*+ Uzikukumbutsani kuti muzilankhula za chilamulo cha Yehova. Uzikukumbutsaninso kuti Yehova ndi amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo ndi dzanja lake lamphamvu. 10  Muzitsatira lamulo limeneli pa nthawi yake yoikidwiratu chaka ndi chaka.+ 11  Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanani, limene analumbira kuti adzalipereka kwa inu ndi makolo anu,+ 12  muzidzapereka kwa Yehova mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa,* wa munthu komanso wa chiweto. Chachimuna chilichonse ndi cha Yehova.+ 13  Mwana aliyense woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa, koma ngati simungamuwombole, muzimuthyola khosi. Ndipo mwana wanu aliyense wamwamuna woyamba kubadwa muzimuwombola.+ 14  Ndiyeno mʼtsogolo ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ mudzawayankhe kuti, ‘Yehova anatitulutsa ndi dzanja lake lamphamvu mu Iguputo, mʼnyumba ya ukapolo.+ 15  Farao atakana mouma mtima kuti tichoke,+ Yehova anapha mwana woyamba kubadwa aliyense mʼdziko la Iguputo, kuyambira mwana woyamba kubadwa wa munthu mpaka mwana woyamba kubadwa wa nyama.+ Nʼchifukwa chake tikupereka nsembe kwa Yehova ana onse a nyama oyamba kubadwa* ndiponso tikuwombola mwana wathu wamwamuna aliyense woyamba kubadwa.’ 16  Mwambowu ukhale ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu komanso pamphumi panu,*+ chifukwa Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi dzanja lake lamphamvu.” 17  Farao atalola kuti Aisiraeli apite, Mulungu sanawadutsitse mʼdziko la Afilisiti ngakhale kuti inali njira yaifupi, chifukwa Mulungu anati: “Anthu angasinthe maganizo akakumana ndi nkhondo ndipo angabwerere ku Iguputo.” 18  Choncho Mulungu anachititsa kuti Aisiraeli adutse njira yaitali yodzera mʼchipululu chapafupi ndi Nyanja Yofiira.+ Koma potuluka mʼdziko la Iguputo, Aisiraeli anayenda mwadongosolo ngati magulu a asilikali. 19  Mose anatenganso mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeli kuti: “Ndithudi, Mulungu adzakukumbukirani, ndipo pochoka kuno mudzatenge mafupa anga.”+ 20  Iwo ananyamuka ku Sukoti nʼkukamanga msasa ku Etamu mʼmalire a chipululu. 21  Pofuna kuwatsogolera, Yehova ankayenda patsogolo pawo. Masana ankawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha mtambo+ ndipo usiku ankawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha moto kuti chiziwaunikira. Choncho ankatha kuyenda masana komanso usiku.+ 22  Chipilala cha mtambo sichinkachoka patsogolo pa anthuwo masana, komanso chipilala cha moto sichinkachoka patsogolo pawo usiku.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Muyeretse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana aliyense woyamba kubadwa, wotsegula mimba ya mayi aliyense.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa maso anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wotsegula mimba ya mayi ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “iliyonse yotsegula mimba ya mayi ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa maso anu.”