Ekisodo 15:1-27
15 Pa nthawiyo Mose ndi Aisiraeli anaimbira Yehova nyimbo iyi:+
“Ndiimbira Yehova, chifukwa walemekezeka kwambiri.+
Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.+
2 Mphamvu ndi nyonga zanga ndi Ya,* chifukwa wandipulumutsa.+
Ameneyu ndi Mulungu wanga ndipo ndidzamʼtamanda.+ Ndi Mulungu wa bambo anga,+ ndipo ndidzamulemekeza.+
3 Yehova ndi msilikali wamphamvu.+ Dzina lake ndi Yehova.+
4 Magaleta a Farao ndi gulu lake lankhondo wawaponyera mʼnyanja.+Asilikali odalirika a Farao amira mʼNyanja Yofiira.+
5 Mafunde amphamvu awakwirira. Amira pansi pa nyanja ngati mwala.+
6 Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, ndi lamphamvu zochuluka.+Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, limaphwanya mdani.
7 Ndi mphamvu zanu zazikulu mumagwetsa otsutsana nanu.+Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.
8 Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu, madzi anaunjikana pamodzi.Madzi oyenda anaima ngati khoma.Mafunde amphamvu anaundana pakatikati pa nyanja.
9 Mdaniyo anati: ‘Ndiwathamangira nʼkuwapeza!
Ndigawa chuma chawo mpaka nditakhutira!
Ndisolola lupanga langa! Dzanja langa liwawononga!’+
10 Mwapemerera mpweya wanu, ndipo nyanja yawamiza.+Amira mʼmadzi akuya ngati chitsulo cholemera.
11 Ndi mulungu uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+
Mumasonyeza kuti ndinu woyera koposa,+ ndani angafanane ndi inu?
Ndinu woyenera kuopedwa ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda. Inu mumachita zodabwitsa.+
12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko lapansi lawameza.+
13 Munasonyeza chikondi chanu chokhulupirika potsogolera anthu amene munawawombola.+Ndi mphamvu zanu, mudzawatsogolera kudziko lanu lopatulika kumene mudzakhala.
14 Anthu adzamva+ ndipo adzanjenjemera.Anthu okhala ku Filisitiya adzamva ululu.*
15 Pa nthawi imeneyo mafumu a ku Edomu adzachita mantha.Ndipo olamulira amphamvu a ku Mowabu adzanjenjemera.+
Anthu onse okhala mu Kanani adzataya mtima.+
16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+
Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala ngati mwala, osachita kanthu.Mpaka anthu anu atadutsa, inu Yehova,Mpaka anthu anu amene munawapanga+ atadutsa.+
17 Mudzawabweretsa nʼkuwakhazikitsa mʼphiri limene ndi cholowa chanu.+Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukhalemo, inu Yehova.Malo opatulika amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa.
18 Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale.+
19 Mahatchi a Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi atalowa mʼnyanja,+Yehova wabweza madzi amʼnyanjamo nʼkuwamiza.+Koma Aisiraeli ayenda panthaka youma pakati pa nyanja.”+
20 Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, yemwe anali mchemwali wake wa Aroni, anatenga maseche mʼmanja mwake ndipo akazi ena onse ankamutsatira akuimba maseche nʼkumavina.
21 Pamene amuna ankaimba, Miriamu ankathirira mangʼombe kuti:
“Imbirani Yehova chifukwa walemekezeka kwambiri.+
Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.”+
22 Kenako Mose anatsogolera Isiraeli kuchoka ku Nyanja Yofiira ndipo analowa mʼchipululu cha Shura. Iwo anayenda mʼchipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi.
23 Iwo anafika ku Mara,+ koma sanathe kumwa madzi a ku Mara chifukwa anali owawa. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Mara.*
24 Choncho anthu anayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose+ kuti: “Timwa chiyani?”
25 Zitatero Mose anafuulira Yehova+ ndipo Yehova anamusonyeza kamtengo. Mose anaponya kamtengoko mʼmadzi moti madziwo anakhala okoma.
Pamalo amenewo Mulungu anawapatsa lamulo ndi maziko operekera chiweruzo, ndipo kumeneko anawayesa.+
26 Iye anawauza kuti: “Mukadzamvera ndi mtima wonse mawu a Yehova Mulungu wanu, nʼkuchita zinthu zoyenera pamaso pake ndiponso kumvera malamulo ake ndi kusunga malangizo ake onse,+ sindidzakugwetserani matenda aliwonse amene ndinagwetsera Aiguputo,+ chifukwa ine Yehova ndi amene ndikukuchiritsani.”+
27 Kenako anafika ku Elimu kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza. Choncho iwo anamanga msasa pamenepo pafupi ndi madzi.