Ekisodo 16:1-36
16 Atachoka ku Elimu, gulu lonse la Aisiraeli linafika mʼchipululu cha Sini chimene chili pakati pa Elimu ndi Sinai.+ Anafika kumeneko pa tsiku la 15 la mwezi wachiwiri atachoka mʼdziko la Iguputo.
2 Mʼchipululumo gulu lonse la Aisiraeli linayamba kungʼungʼudzira Mose ndi Aroni.+
3 Aisiraeliwo ankauza Mose ndi Aroni kuti: “Zikanakhala bwino dzanja la Yehova likanatiphera mʼdziko la Iguputo, kumene tinkadya nyama+ ndi mkate nʼkukhuta. Mʼmalomwake mwatibweretsa mʼchipululu muno kuti muphetse mpingo wonsewu ndi njala.”+
4 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Ndikugwetserani chakudya kuchokera kumwamba ngati mvula,+ ndipo aliyense azitola muyezo womukwanira pa tsikulo.+ Ndikuchita izi kuti ndiwayese kuti ndione ngati angatsatire chilamulo changa kapena ayi.+
5 Koma pa tsiku la 6,+ azitola muyezo wowirikiza kawiri zimene amatola tsiku ndi tsiku+ ndipo azikonzeratu zimene atolazo.”
6 Choncho Mose ndi Aroni anauza Aisiraeli onse kuti: “Madzulo ano mudziwa kuti Yehova ndi amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo.+
7 Mawa mʼmawa mudzaona ulemerero wa Yehova chifukwa wamva kungʼungʼudza kwanu kotsutsana ndi Yehovayo. Ife ndi ndani kuti muzitingʼungʼudzira?”
8 Ndiyeno Mose anapitiriza kuti: “Yehova akakupatsani nyama yoti mudye madzulo ano ndi mkate wokwanira mʼmawa, muona kuti Yehova wamva kungʼungʼudza kwanu kotsutsana naye. Ife ndi ndani? Kungʼungʼudza kwanu si kotsutsana ndi ife, koma nʼkotsutsana ndi Yehova.”+
9 Choncho Mose anauza Aroni kuti: “Uza gulu lonse la Aisiraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova, chifukwa wamva kungʼungʼudza kwanu.’”+
10 Ndiyeno Aroni atangomaliza kulankhula ndi gulu lonse la Aisiraeli, iwo anatembenuka nʼkuyangʼana kuchipululu. Ndipo kenako ulemerero wa Yehova unaonekera mumtambo.+
11 Yehova anauzanso Mose kuti:
12 “Ndamva kungʼungʼudza kwa Aisiraeli.+ Ndiye uwauze kuti, ‘Madzulo kuli kachisisira* mudzadya nyama ndipo mʼmawa mudzadya mkate nʼkukhuta.+ Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”+
13 Choncho madzulo amenewo kunabwera zinziri zimene zinakuta msasa wonse,+ ndipo mʼmawa kunachita mame kuzungulira msasa wonsewo.
14 Mame aja atauma, panthaka yamʼchipululumo panapezeka tinthu topyapyala ndi tolimba koma tosalala+ ngati madzi amene aundana panthaka.
15 Aisiraeli ataona tinthu timeneti anayamba kufunsana kuti: “Nʼchiyani ichi?” chifukwa sankadziwa kuti chinali chiyani. Mose anawauza kuti: “Ndi chakudya chimene Yehova wakupatsani.+
16 Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole chakudya chimenechi mogwirizana ndi mmene amadyera. Munthu aliyense muzimutolera muyezo wa omeri*+ imodzi mogwirizana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mutenti yanu.’”
17 Choncho Aisiraeli anayamba kutola chakudyacho, ena anatola chambiri koma ena anatola chochepa.
18 Akayeza chakudyacho pamuyezo wa omeri, munthu amene anatola chambiri sichinamutsalire ndipo amene anatola chochepa sichinamuperewere.+ Aliyense anatola mogwirizana ndi mmene amadyera.
19 Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Aliyense asasiye chakudyachi mpaka mʼmawa.”+
20 Koma iwo sanamvere Mose. Anthu ena atasiya chakudyacho mpaka mʼmawa, chinatuluka mphutsi nʼkuyamba kununkha, moti Mose anawakalipira kwambiri.
21 Mʼmawa uliwonse iwo ankatola chakudyacho, aliyense mogwirizana ndi mmene amadyera. Dzuwa likatentha, chakudyacho chinkasungunuka.
22 Pa tsiku la 6, anthuwo anatola muyezo wowirikiza kawiri,+ munthu aliyense maomeri awiri. Ndiyeno atsogoleri onse a gulu la Aisiraeli anabwera kwa Mose kudzanena.
23 Ndipo iye anawayankha kuti: “Ndi zimene Yehova wanena. Mawa ndi tsiku lopuma,* ndi sabata lopatulika la Yehova.+ Zimene mungaphike, phikani, ndipo zimene mungawiritse, wiritsani.+ Zotsala zonse muziike pambali nʼkuzisunga mpaka mʼmawa.”
24 Choncho anasungadi chakudyacho mpaka mʼmawa mogwirizana ndi zimene Mose anawalamula, ndipo sichinanunkhe kapena kuchita mphutsi.
25 Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Idyani chakudyachi lero, chifukwa lero ndi sabata la Yehova ndipo simukachipeza kunja kwa msasa.
26 Muzitola chakudyachi masiku 6, koma tsiku la 7 ndi Sabata.+ Pa tsiku limeneli sichidzapezeka kunja kwa msasa.”
27 Komabe, pa tsiku la 7 anthu ena anapita kuti akatole chakudyacho, koma sanachipeze.
28 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Kodi anthu inu mupitiriza kukana kusunga malamulo ndi malangizo anga mpaka liti?+
29 Dziwani kuti Yehova wakupatsani Sabata.+ Nʼchifukwa chake pa tsiku la 6 akukupatsani chakudya cha masiku awiri. Pa tsiku la 7 aliyense azikhala pamalo ake. Munthu asachoke pamalo ake.”
30 Choncho anthuwo anasunga sabata* tsiku la 7.+
31 Nyumba ya Isiraeli inapatsa chakudyacho dzina lakuti “mana.”* Chinali choyera ngati mapira,* ndipo kukoma kwake kunali ngati makeke opyapyala othira uchi.+
32 Kenako Mose anati: “Yehova walamula kuti, ‘Dzazani muyezo umodzi wa omeri ndi mana kuti asungidwe mʼmibadwo yanu yonse,+ nʼcholinga choti iwo adzaone chakudya chimene ndinakupatsani mʼchipululu nditakutulutsani mʼdziko la Iguputo.’”
33 Ndiyeno Mose anauza Aroni kuti: “Tenga mtsuko ndipo uthiremo mana okwana muyezo umodzi wa omeri nʼkuuika pamaso pa Yehova kuti asungidwe mʼmibadwo yanu yonse.”+
34 Aroni anaikadi mtsukowo patsogolo pa Umboni*+ kuti manawo asungidwe mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
35 Aisiraeli anadya mana kwa zaka 40+ mpaka pamene analowa mʼdziko limene munkakhala anthu.+ Iwo ankadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a dziko la Kanani.+
36 Miyezo 10 ya omeri inkakwana muyezo umodzi wa efa.*
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Pakati pa madzulo awiri.”
^ Malita pafupifupi 2.2. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “Mawa tidzasunga sabata.”
^ Kapena kuti, “anapuma pa.”
^ Zikuoneka kuti dzinali linachokera kumawu a Chiheberi amene amatanthauza kuti “Nʼchiyani ichi?”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “njere ya koriyanda.”
^ Kapena kuti, “Chikumbutso.” Zikuoneka kuti limeneli linali bokosi losungiramo zinthu zofunika zimene analemba.
^ Muyezo wa efa ndi wofanana ndi malita 22. Onani Zakumapeto B14.