Ekisodo 2:1-25
2 Pa nthawiyo, mwamuna wina wa fuko la Levi anakwatira mkazi amene analinso wa fuko la Levi.+
2 Mkaziyo anakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu.+
3 Mwanayo atafika poti sangathenso kumubisa,+ anatenga kabasiketi* kagumbwa* nʼkukamata phula. Kenako anaikamo mwanayo nʼkukasiya kabasiketiko pakati pa mabango mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo.
4 Koma mchemwali wake+ anaima chapatali kuti aone zimene zingachitikire mwanayo.
5 Mwana wamkazi wa Farao atapita kukasamba mumtsinje wa Nailo, atsikana ake omutumikira ankayenda mʼmphepete mwa mtsinjewo. Kenako iye anaona kabasiketi kaja kali pakati pa mabango. Nthawi yomweyo anatuma kapolo wake wamkazi kuti akakatenge.+
6 Atakatsegula anaona kuti muli mwana wamwamuna, ndipo ankalira. Iye anamumvera chisoni, koma ananena kuti: “Uyu ndi mmodzi wa ana a Aheberi.”
7 Zitatero, mchemwali wake uja anauza mwana wa Farao kuti: “Kodi mungakonde kuti ndikakuitanireni mayi woyamwitsa wa Chiheberi kuti akulerereni mwanayu?”
8 Mwana wa Faraoyo anamuyankha kuti: “Inde pita!” Nthawi yomweyo mtsikanayo anapita kukaitana mayi ake+ a mwanayo.
9 Ndiyeno mwana wa Farao anauza mayiyo kuti: “Tenga mwanayu ukandilerere ndipo ine ndizikulipira.” Choncho mayiyo anatenga mwanayo ndipo anamulera.
10 Mwana uja atakula, anapita naye kwa mwana wa Farao, ndipo anakhala mwana wake.+ Zitatero anamʼpatsa dzina lakuti Mose* nʼkunena kuti: “Chifukwa chakuti ndinamuvuula mʼmadzi.”+
11 Tsopano mʼmasiku amenewo, Mose atakula* anapita kwa abale ake kuti akaone mmene ankavutikira ndi ntchito yaukapolo+ imene ankagwira. Kumeneko anaona mʼbale wake wa Chiheberi akumenyedwa ndi nzika ina ya ku Iguputo.
12 Choncho anayangʼana uku ndi uku ndipo ataona kuti palibe amene akumuona, anapha munthu wa ku Iguputoyo nʼkumubisa mumchenga.+
13 Koma tsiku lotsatira atapitanso, anapeza amuna awiri a Chiheberi akumenyana. Choncho anafunsa wolakwayo kuti: “Ukumʼmenyeranji mnzako?”+
14 Poyankha iye anati: “Ndi ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza? Kodi ukufuna kundipha ngati mmene unaphera nzika ya mu Iguputo ija?”+ Zitatero Mose anachita mantha ndipo mumtima mwake anati: “Apa nkhani ija yadziwika basi!”
15 Kenako Farao anamva za nkhaniyi ndipo ankafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa Farao nʼkupita kukakhala kudziko la Midiyani.+ Atafika kumeneko, anakhala pafupi ndi chitsime.
16 Ndiyeno wansembe wa ku Midiyani+ anali ndi ana aakazi 7. Iwo anafika pachitsimepo kuti atunge madzi ndi kuwathira momwera ziweto kuti ziweto za bambo awo zimwe.
17 Koma monga mwa masiku onse, kunafika abusa nʼkuthamangitsa atsikanawo. Zitatero Mose ananyamuka nʼkuthandiza* atsikanawo, ndipo iye anamwetsa ziweto zawo.
18 Ndiyeno atsikanawo atafika kunyumba, bambo awo a Reueli*+ anadabwa ndipo anati: “Bwanji mwabwerako mwamsanga chonchi lero?”
19 Iwo anayankha kuti: “Munthu wina wa ku Iguputo+ watilanditsa kwa abusa, komanso watitungira madzi nʼkutimwetsera ziweto.”
20 Iye anafunsa ana akewo kuti: “Nanga iyeyo ali kuti? Mwamusiyiranji? Pitani mukamuitane kuti tidzadye naye chakudya.”
21 Zitatero Mose anavomereza kukhala ndi Reueli, ndipo iye anapereka Zipora+ mwana wake wamkazi kwa Mose kuti akhale mkazi wake.
22 Kenako Zipora anabereka mwana wamwamuna ndipo Mose anamʼpatsa dzina lakuti Gerisomu,*+ chifukwa anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.”+
23 Patapita nthawi yaitali mfumu ya Iguputo inamwalira.+ Koma Aisiraeli anapitirizabe kuvutika chifukwa cha ukapolo ndipo ankalira modandaula. Iwo anapitirizabe kulirira Mulungu woona+ kuti awathandize chifukwa cha ukapolowo.
24 Patapita nthawi, Mulungu anamva kubuula+ kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+
25 Choncho Mulungu anayangʼana Aisiraeli ndipo anaona mmene ankavutikira.