Ekisodo 22:1-31

  • Zigamulo zoti Aisiraeli azitsatira (1-31)

    • Zokhudza kuba (1-4)

    • Zokhudza kuonongeka kwa mbewu (5, 6)

    • Zokhudza kulipira zinthu ndi katundu wamwini (7-15)

    • Zokhudza kunyengerera mkazi (16, 17)

    • Zokhudza kulambira komanso chilungamo (18-31)

22  “Munthu akaba ngʼombe kapena nkhosa nʼkuipha kapena kuigulitsa, azilipira ngʼombe 5 pa ngʼombe imodzi imene waba, ndi nkhosa 4 pa nkhosa imodzi imene waba.+  (Ngati wakuba+ wapezeka akuthyola nyumba kuti abe ndipo wamenyedwa nʼkufa, amene wamuphayo alibe mlandu wa magazi.  Koma ngati zachitika dzuwa litatuluka, amene wamuphayo ali ndi mlandu wa magazi.) Wakuba azilipira ndipo ngati alibe kalikonse, azigulitsidwa kuti alipire zinthu zimene anabazo.  Ngati zimene anabazo zapezeka ndi iyeyo zili zamoyo, kaya ndi ngʼombe, bulu kapena nkhosa, azilipira zowirikiza kawiri.  Ngati munthu waika ziweto zake kuti zidye mʼmunda wa mpesa kapena wa mbewu zina, ndipo wazilekerera kuti zikadye mʼmunda wa munthu wina, azilipira popereka zokolola zabwino koposa zamʼmunda wake wa mpesa kapena zamʼmunda wake wa mbewu zina.  Ngati munthu wayatsa moto, motowo nʼkugwirira zomera zaminga ndipo wafalikira mʼmunda wa munthu wina nʼkuwotcha mitolo yambewu, mbewu zosadula kapena munda wonse, amene anayatsa motowo azilipira mbewu zimene zapsazo.  Ngati munthu wapatsa mnzake ndalama kapena katundu wina kuti amusungire, zinthuzo nʼkubedwa mʼnyumba ya mnzakeyo, wakubayo akapezeka azilipira zowirikiza kawiri.+  Ngati wakubayo sanapezeke, azibweretsa mwininyumbayo pamaso pa Mulungu woona*+ kuti zidziwike ngati iyeyo ndi amene waba katundu wa mnzakeyo kapena ayi.  Pa milandu yonse yokhudza kutenga chinthu cha mwini popanda chilolezo, kaya ndi ngʼombe, bulu, nkhosa, chovala kapena chilichonse chimene chinasowa chomwe angachiloze kuti, ‘Ichi nʼchanga!’ awiri onsewo mlandu wawo uzifika pamaso pa Mulungu woona.+ Amene Mulungu adzamuweruze kuti ndi wolakwa, azilipira mnzakeyo zowirikiza kawiri.+ 10  Ngati munthu wapatsa mnzake bulu, ngʼombe, nkhosa kapena chiweto chilichonse kuti amusungire, ndipo chafa kapena chavulala kwambiri kapenanso chagwidwa popanda munthu kuona zimene zachitika, 11  amene anasunga zinthuzo azilumbira kwa mnzake pamaso pa Yehova kuti sanachite zimenezo pa katundu wa mnzake. Mwiniwake wa katunduyo azivomereza lumbirolo ndipo mnzakeyo asamalipire.+ 12  Koma ngati chiwetocho chinachita kubedwa,* azilipira kwa mwiniwake. 13  Ngati chiwetocho chinaphedwa ndi chilombo, azibweretsa chiweto chakufacho monga umboni. Iye sakuyenera kulipira ngati chiweto chaphedwa ndi chilombo. 14  Koma ngati munthu wabwereka chiweto kwa mnzake ndipo chavulala kwambiri kapena chafa mwiniwake wa chiwetocho palibe, wobwerekayo azilipira. 15  Ngati mwiniwake alipo, wobwerekayo asalipire. Ngati anafunika kupereka ndalama kuti abwereke, adzangopereka ndalama yobwerekera chiwetocho. 16  Mwamuna akanyengerera namwali wosalonjezedwa kukwatiwa nʼkugona naye, azimʼtenga ndithu kukhala mkazi wake atapereka malowolo.+ 17  Bambo a mtsikanayo akakaniratu kupatsa mwamunayo mwana wawo, iye azipereka ndalama zofanana ndi malowolo. 18  Mkazi wamatsenga musamulole kukhala ndi moyo.+ 19  Aliyense wogonana ndi nyama, aziphedwa ndithu.+ 20  Wopereka nsembe kwa milungu ina osati kwa Yehova yekha, aziphedwa ndithu.+ 21  Musamachitire nkhanza mlendo wokhala pakati panu kapena kumʼpondereza,+ chifukwa inunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+ 22  Musamazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye* aliyense.+ 23  Ngakhale mutamuzunza pangʼono, iye nʼkundilirira, ndidzamva ndithu kulira kwake.+ 24  Mkwiyo wanga udzakuyakirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga, moti akazi anu adzakhala akazi amasiye ndipo ana anu adzakhala ana amasiye. 25  Mukabwereketsa ndalama kwa munthu aliyense wosauka* pakati pa anthu anga, kwa munthu amene ali pafupi ndi inu, musakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira kwa iye. Musamuuze kuti apereke chiwongoladzanja.+ 26  Ukalanda mnzako chovala chake monga chikole cha ngongole,+ uzimubwezera dzuwa likamalowa. 27  Chifukwa chofunda chake nʼchomwecho. Ndi nsalu imene amafunda.+ Nanga afunda chiyani pogona? Ndiyeno akandilirira, ine ndidzamva ndithu, chifukwa ndine wachifundo.+ 28  Usatemberere* Mulungu+ kapena mtsogoleri* amene ali pakati pa anthu a mtundu wako.+ 29  Musamazengereze kundipatsa nsembe kuchokera pa zokolola zanu zomwe ndi zambiri komanso kuchokera ku vinyo ndi mafuta omwe ndi ochuluka.+ Mwana wanu wamwamuna woyamba kubadwa muzimupereka kwa ine.+ 30  Zimene muzichita ndi mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe ndi wa nkhosa yanu ndi izi:+ Azikhala ndi mayi ake masiku 7. Pa tsiku la 8 muzimupereka kwa ine.+ 31  Mukhale anthu oyera pamaso panga+ ndipo musadye nyama imene yaphedwa ndi chilombo kuthengo.+ Imeneyo muziponyera agalu.”

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti, kupita naye kwa oweruza oimira Mulungu woona.
Mwina chifukwa cha kusasamala kapena chifukwa cha zochitika zina zimene akanatha kuzipewa.
Kapena kuti, “mwana wopanda bambo.”
Kapena kuti, “wovutika.”
Kapena kuti, “wolamulira.”
Kapena kuti, “Usanyoze.”