Ekisodo 29:1-46

  • Kuikidwa kwa ansembe (1-37)

  • Nsembe ya tsiku ndi tsiku (38-46)

29  “Uchite izi kuti uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga: Utenge ngʼombe yaingʼono yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo zopanda chilema.+  Utengenso mkate wopanda zofufumitsa, mkate wozungulira woboola pakati wopanda zofufumitsa, wothira mafuta komanso timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta.+ Uzipange ndi ufa wa tirigu wosalala.  Zimenezi uziike mʼdengu nʼkuzipereka zili mʼdengu momwemo.+ Uchitenso chimodzimodzi ndi ngʼombe ndi nkhosa ziwiri zija.  Ubweretse Aroni ndi ana ake pakhomo la chihema chokumanako,+ ndipo uwasambitse* ndi madzi.+  Kenako utenge zovala+ zija nʼkuveka Aroni. Umuveke mkanjo ndi malaya odula manja a mkati mwa efodi. Umuvekenso efodi ndi chovala pachifuwa komanso umumange lamba* woluka wa efodi mʼchiuno mwake.+  Umuveke nduwira pamutu pake ndipo panduwirapo uikepo chizindikiro chopatulika cha kudzipereka.+  Kenako utenge mafuta odzozera+ nʼkuwathira pamutu pake kuti akhale wodzozedwa.+  Ukatero utenge ana ake nʼkuwaveka mikanjo.+  Aroni ndi ana akewo uwamange malamba pamimba. Ana akewo uwakulunge mipango kumutu kwawo ndipo adzakhala ansembe.+ Limeneli ndi lamulo langa mpaka kalekale. Uchite zimenezi kuti uike Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe.*+ 10  Kenako ubweretse ngʼombe patsogolo pa chihema chokumanako, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa ngʼombeyo.+ 11  Ndiyeno ngʼombeyo uiphe pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.+ 12  Ukatero utengeko magazi a ngʼombeyo ndi chala chako ndipo uwapake panyanga za guwa lansembe.+ Magazi otsalawo uwathire pansi pa guwa lansembe.+ 13  Kenako utenge mafuta onse+ okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake nʼkuzitentha kuti paguwa lansembe pakhale utsi.+ 14  Koma nyama ya ngʼombeyo, chikopa chake ndi ndowe zake uzitenthe ndi moto kunja kwa msasa. Ngʼombeyo ndi nsembe yamachimo. 15  Ndiyeno utenge nkhosa imodzi, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 16  Nkhosayo uiphe nʼkutenga magazi ake ndipo uwawaze mbali zonse za guwa lansembelo.+ 17  Nkhosayo uidule ziwaloziwalo. Kenako utsuke matumbo+ ndi ziboda zake nʼkuika chiwalo chilichonse pamodzi ndi chinzake, kuyambira kumiyendo mpaka kumutu. 18  Nkhosa yonseyo uiwotche kuti utsi wake ukwere mʼmwamba kuchokera paguwalo. Imeneyo ndi nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova, yakafungo kosangalatsa.*+ Ndi nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. 19  Kenako utenge nkhosa ina ija, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 20  Uphe nkhosayo nʼkutengako magazi ake ndipo uwapake mʼmunsi pakhutu lakumanja la Aroni, ndi mʼmunsi pamakutu akumanja a ana a Aroni. Uwapakenso pazala zawo za manthu kudzanja lamanja ndi pazala zawo zazikulu za mwendo wakumanja, ndipo uwaze magaziwo mbali zonse za guwa lansembe. 21  Ndiyeno utengeko magazi amene ali paguwa lansembe ndi mafuta pangʼono odzozera+ nʼkuwadontheza pa Aroni ndi pazovala zake. Uwadonthezenso pa ana ake ndi zovala zawo kuti Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake ndi zovala zawo akhale oyera.+ 22  Ndiyeno pankhosayo utengepo mafuta ndi mchira wa mafuta ndi mafuta okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake+ ndi mwendo wakumbuyo wakumanja, chifukwa nkhosayo ndi yowaikira kuti akhale ansembe.+ 23  Mʼdengu la mikate yosafufumitsa limene lili pamaso pa Yehova utengemo mkate wobulungira, mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta ndi mkate wopyapyala. 24  Zonsezi uziike mʼmanja mwa Aroni ndi mʼmanja mwa ana ake, ndipo uziyendetse uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova. 25  Kenako uzitenge mʼmanja mwawo nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza, kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. 26  Kenako utenge chidale cha nkhosa yoikira+ Aroni kuti akhale wansembe ndipo uchiyendetse uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyo idzakhale yako. 27  Pankhosa yoikira Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe, upatule chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku, ndi mwendo wa gawo lopatulika umene anapereka.+ 28  Zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake mwa lamulo mpaka kalekale. Aisiraeli ayenera kutsatira lamulo limeneli chifukwa ndi gawo lopatulika. Lidzakhala gawo lopatulika loyenera kuperekedwa ndi Aisiraeli.+ Limeneli ndi gawo lawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova kuchokera pansembe zawo zamgwirizano.+ 29  Zovala zopatulika+ za Aroni zidzagwiritsidwa ntchito ndi ana ake+ obwera mʼmbuyo mwake akadzawadzoza nʼkuwaika kuti akhale ansembe. 30  Wansembe amene adzalowe mʼmalo mwake kuchokera pakati pa ana ake, amene adzalowe mʼchihema chokumanako kukatumikira mʼmalo oyera, azidzavala zovalazo kwa masiku 7.+ 31  Kenako udzatenge nkhosa yowaikira kuti akhale ansembe nʼkuwiritsa nyama yake mʼmalo oyera.+ 32  Aroni ndi ana ake adye+ nyama ya nkhosayo ndi mkate umene uli mʼdengu, adyere pakhomo la chihema chokumanako. 33  Adye zinthu zimene aphimbira machimo kuti awaike* kukhala ansembe nʼkuwayeretsa. Koma munthu wamba* asadye nawo, chifukwa ndi zinthu zopatulika.+ 34  Nyama ya nkhosa yowaikira kuti akhale ansembe ndi mkatewo, zikatsala mpaka mʼmawa, uziwotche ndi moto.+ Siziyenera kudyedwa chifukwa ndi zinthu zopatulika. 35  Uchite zimenezi kwa Aroni ndi ana ake malinga ndi zonse zimene ndakulamula. Udzatenga masiku 7 kuti uwaike* kukhala ansembe.+ 36  Uzipereka ngʼombe ya nsembe yamachimo tsiku lililonse kuti iphimbe machimo. Uziyeretsa guwa lansembe ku machimo poliperekera nsembe yophimba machimo, ndipo uzilidzoza kuti likhale loyera.+ 37  Udzatenga masiku 7 poperekera guwa lansembelo nsembe yophimba machimo. Udzaliyeretse kuti likhale guwa lansembe loyera koposa.+ Aliyense wogwira guwa lansembe azikhala woyera. 38  Zimene uzipereka paguwa lansembelo ndi izi: ana a nkhosa a chaka chimodzi, awiri pa tsiku ndipo uzichita zimenezi nthawi zonse.+ 39  Uzipereka mwana wa nkhosa mmodzi mʼmawa, ndipo mwana wa nkhosa winayo madzulo kuli kachisisira.*+ 40  Popereka mwana wa nkhosa woyamba, uzipereka limodzi ndi ufa wosalala, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* wothira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini,* ndi gawo limodzi mwa magawo 4 a vinyo wa nsembe yachakumwa. 41  Uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira.* Uzimupereka pamodzi ndi nsembe yambewu komanso nsembe yachakumwa ngati mmene unachitira mʼmawa. Uzipereke kuti zikhale kafungo kosangalatsa,* nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. 42  Mʼmibadwo yanu yonse, muzipereka nsembe yopsereza imeneyi nthawi zonse pakhomo la chihema chokumanako pamaso pa Yehova, kumene ndidzaonekera kwa inu kuti ndilankhule nanu.+ 43  Ndidzaonekera pamenepo kwa Aisiraeli, ndipo malo amenewa adzayeretsedwa ndi ulemerero wanga.+ 44  Ndidzayeretsa chihema chokumanako ndi guwa lansembe. Ndidzayeretsanso Aroni ndi ana ake+ kuti atumikire monga ansembe anga. 45  Ndidzakhala pakati pa Aisiraeli ndipo ndidzakhala Mulungu wawo.+ 46  Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo, amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo kuti ndikhale pakati pawo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wawo.”

Mawu a M'munsi

Nʼkuthekanso kuti Mose anawauza kuti asambe.
Kapena kuti, “lamba wamʼchiuno.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “udzaze dzanja la Aroni ndi manja a ana ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “udzaze manja awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlendo,” kutanthauza munthu amene si wa mʼbanja la Aroni.
Mʼchilankhulo choyambirira, “udzaze manja awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”
Muyezo wa efa ndi wofanana ndi malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Muyezo wa hini ndi wofanana ndi malita 3.67. Onani Zakumapeto B14
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”