Ekisodo 30:1-38
30 “Upange guwa lansembe zofukiza.+ Ulipange ndi matabwa amthethe.+
2 Mbali zake zonse 4 zikhale zofanana, mulitali mwake likhale masentimita 45,* mulifupi mwake masentimita 45. Ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka pamwamba likhale masentimita 90. Nyanga zake azipangire kumodzi ndi guwalo.*+
3 Ulikute ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi mʼmbali mwake kuzungulira guwalo komanso nyanga zake. Upange mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo.
4 Upangenso mphete ziwiri zagolide mʼmunsi mwa mkombero kumbali zake ziwiri zoyangʼanizana kuti muzilowa ndodo zonyamulira guwalo.
5 Upangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo uzikute ndi golide.
6 Guwalo uliike kutsogolo kwa katani imene ili pafupi ndi likasa la Umboni.+ Likhale patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa Umboni, pomwe ndidzaonekera kwa iwe.+
7 Aroni+ aziwotcha zofukiza zonunkhira+ kuti paguwapo+ pazikhala utsi mʼmawa uliwonse akamasamalira nyale.+
8 Komanso Aroni akamayatsa nyalezo madzulo, aziwotcha zofukizazo. Zimenezi ndi zofukiza zoyenera kuperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mʼmibadwo yanu yonse.
9 Paguwali usaperekerepo zofukiza zosavomerezeka,+ nsembe yopsereza kapena nsembe yambewu, ndipo usathirepo nsembe yachakumwa.
10 Aroni azipaka ena mwa magazi a nyama ya nsembe yamachimo panyanga za guwalo kuti aphimbe machimo+ a nyangazo. Azichita zimenezi kamodzi pa chaka+ mʼmibadwo yanu yonse. Kwa Yehova guwalo ndi lopatulika koposa.”
11 Kenako Yehova anauza Mose kuti:
12 “Ukamachita kalembera wa ana a Isiraeli,+ aliyense azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi imene ukuwawerengayo. Azichita zimenezi kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo.
13 Anthu onse amene awerengedwa azipereka zinthu izi: hafu ya sekeli* yofanana ndi sekeli yakumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli imodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+
14 Aliyense amene wawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita mʼtsogolo azipereka chopereka kwa Yehova.+
15 Mukamapereka kwa Yehova chopereka chophimba machimo kuti muwombole moyo wanu, anthu olemera asapereke zochuluka, ndipo osauka asapereke zosakwana hafu ya sekeli.*
16 Uzilandira ndalama zasiliva zophimbira machimo kwa Aisiraeli nʼkuzipereka kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wapachihema chokumanako. Ndalama zimenezi zidzathandiza kuti Yehova azikumbukira Aisiraeli komanso zidzaphimba machimo anu kuti muwombole moyo wanu.”
17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
18 “Upange beseni losambira lakopa+ ndi choikapo chake. Ukatero uliike pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe ndipo uthiremo madzi.+
19 Aroni ndi ana ake azisamba mʼmanja ndi mapazi awo pamenepo.+
20 Akamalowa mʼchihema chokumanako, kapena akamapita kukatumikira paguwa lansembe, kukapereka kwa Yehova nsembe yowotcha pamoto, azisamba kuti asafe.
21 Azisamba mʼmanja ndi mapazi awo kuti asafe. Limeneli ndi lamulo kwa iwo mpaka kalekale, likhale lamulo kwa Aroni ndi ana ake ku mibadwo yawo yonse.”+
22 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
23 “Kenako utenge mafuta onunkhira, abwino kwambiri awa: mule* woundana wokwana masekeli 500, sinamoni wonunkhira bwino hafu ya muyezo wa mule, kapena kuti masekeli 250, ndi kalamasi wonunkhira wokwana masekeli 250.
24 Utengenso kasiya* masekeli 500 ofanana ndi masekeli akumalo oyera*+ komanso hini* imodzi ya mafuta a maolivi.
25 Zinthu zimenezi upangire mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika, mafuta onunkhira osakanizidwa mwaluso.*+ Akhale mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika.
26 Mafuta amenewa udzozere chihema chokumanako,+ likasa la Umboni,
27 tebulo ndi ziwiya zake zonse, choikapo nyale ndi ziwiya zake zonse, guwa lansembe zofukiza,
28 guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, komanso beseni ndi choikapo chake.
29 Uziyeretse kuti zikhale zoyera koposa.+ Aliyense wogwira zinthu zimenezi azikhala woyera.+
30 Kenako udzoze Aroni+ ndi ana ake+ ndipo uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga.+
31 Uuze Aisiraeli kuti, ‘Mafuta awa akhale mafuta anga ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika mʼmibadwo yanu yonse.+
32 Musapake mafuta amenewa pakhungu la munthu aliyense, ndipo musapange mafuta ofanana nawo pogwiritsa ntchito zinthu zopangira mafutawa. Mafuta amenewa ndi opatulika. Apitirizebe kukhala opatulika kwa inu.
33 Aliyense wopanga mafuta ofanana ndi amenewa, ndiponso amene angapake munthu wamba mafutawa, ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’”+
34 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Utenge muyezo wofanana wa zinthu zonunkhira izi:+ madontho a sitakate,* onika, mafuta onunkhira a galibanamu ndi lubani* weniweni.
35 Zinthu zimenezi upangire zofukiza.+ Usakanize zonunkhiritsa zimenezi mwaluso,* uthire mchere,+ zikhale zoyera ndi zopatulika.
36 Kenako upere zina mwa zofukiza zimenezi kuti zikhale ufa wosalala kwambiri. Uike wina mwa ufawo patsogolo pa Umboni mʼchihema chokumanako, kumene ndidzaonekera kwa iwe. Zofukiza zimenezi zikhale zopatulika koposa kwa inu.
37 Musapange zofukiza zanuzanu pogwiritsa ntchito zinthu zopangira zofukiza zimenezi.+ Muziona kuti zofukiza zimenezi nʼzopatulika kwa Yehova.
38 Aliyense wopanga zofukiza zofanana ndi zimenezi pofuna kusangalala ndi kafungo kake, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mkono umodzi.” Onani Zakumapeto B14.
^ Kutanthauza kuti nyanga zimenezi sanazipangire padera nʼkuchita kuzilumikiza kuguwalo.
^ Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
^ Gera imodzi inali yofanana ndi magalamu 0.57. Onani Zakumapeto B14.
^ Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
^ Muyezo wa hini ndi wofanana ndi malita 3.67. Onani Zakumapeto B14
^ Kapena kuti, “mafuta onunkhira ngati opangidwa ndi anthu ogwira ntchito yosakaniza mafuta.”
^ “Sitakate” ndi utomoni wonunkhira wa mitengo.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ngati mmene amachitira anthu ogwira ntchito yosakaniza mafuta.”