Ekisodo 34:1-35
34 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo ine ndidzalemba pamiyala yosemayo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija,+ imene iwe unaswa.+
2 Ndipo ukonzeke kuti mawa mʼmawa ukakwere phiri la Sinai nʼkukakhala pamaso panga kumeneko pamwamba pa phirilo.+
3 Koma usakwere mʼphirimo ndi wina aliyense, ndipo musapezeke wina aliyense mmenemo. Ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmunsi mwa phirilo.”+
4 Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo anadzuka mʼmamawa kwambiri nʼkukwera phiri la Sinai atanyamula miyala iwiriyo mʼmanja mwake, mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula.
5 Kenako Yehova anatsika+ mumtambo nʼkuima pafupi ndi Mose ndipo analengeza dzina lake lakuti Yehova.+
6 Ndiyeno Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wokoma mtima,*+ wosakwiya msanga+ ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka+ komanso choonadi.*+
7 Amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa mibadwo masauzande,+ amakhululuka zolakwa ndi machimo,+ koma sadzalekerera wolakwa osamʼpatsa chilango.+ Amalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+
8 Nthawi yomweyo Mose anagwada nʼkuweramira pansi.
9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde Yehova, muyende nafe ndipo mukhale pakati pathu,+ ngakhale kuti ndife anthu ouma khosi.+ Mutikhululukirenso zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndipo mutitenge kukhala chuma chanu.”
10 Poyankha Mulungu anati: “Ine ndikuchita nanu pangano ili: Ndidzachita zinthu zodabwitsa pamaso pa anthu ako onse, zimene sizinachitikepo padziko lonse lapansi kapena pakati pa mitundu yonse.+ Ndipo anthu onse okuzungulirani adzaonadi ntchito za Yehova, chifukwa ndidzakuchitirani chinthu chochititsa mantha.+
11 Koma inu mumvere mosamala zimene ndikukulamulani lero.+ Inetu ndikuthamangitsa pamaso panu Aamori, Akanani, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+
12 Samalani kuti musachite pangano ndi anthu amʼdziko limene mukupitako,+ kuopera kuti ungakhale msampha kwa inu.+
13 Koma maguwa awo ansembe mukawagwetse, zipilala zawo zopatulika mukaziphwanye ndipo mizati* yawo yopatulika mukaidule.+
14 Musagwadire mulungu wina,+ chifukwa Yehova amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.* Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.*+
15 Samalani kuti musachite pangano ndi anthu okhala mʼdzikomo, chifukwa akamachita uhule ndi milungu yawo komanso kupereka nsembe kwa milungu yawo,+ wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+
16 Kenako mudzatengadi ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna.+ Ndipo ana awo aakazi adzachita uhule ndi milungu yawo nʼkuchititsa ana anu aamuna kuchita uhule ndi milungu yawo.+
17 Musapange milungu ya chitsulo chosungunula.+
18 Muzichita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Mogwirizana ndi zimene ndinakulamulani, muzidya mikate yopanda zofufumitsa masiku 7 mʼmwezi wa Abibu* pa nthawi imene inaikidwa,+ chifukwa munatuluka mu Iguputo mʼmwezi wa Abibu.
19 Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa* ndi wanga,+ kuphatikizapo mwana woyamba kubadwa wa ziweto zanu zonse, kaya ndi mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena nkhosa.+
20 Mwana woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa. Koma ngati simungamuwombole, muzimuthyola khosi. Ndipo muziwombola mwana wanu wamwamuna aliyense woyamba kubadwa.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.
21 Muzigwira ntchito zanu kwa masiku 6, koma pa tsiku la 7 muzipuma.*+ Ngakhale pa nthawi yolima ndi yokolola muzipuma.
22 Muzichita Chikondwerero cha Masabata,* ndipo pochita chikondwerero chimenechi muzipereka tirigu woyamba kucha pa tirigu amene mwakolola. Kumapeto kwa chaka muzichita Chikondwerero cha Zokolola.*+
23 Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+
24 Mitundu ya anthu ndidzaithamangitsira kutali ndi inu,+ ndipo ndidzakulitsa dera lanu. Palibe aliyense amene adzasirire dziko lanu mukapita kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu katatu pa chaka.
25 Mukamapereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa.+ Musamasunge nsembe ya chikondwerero cha Pasika mpaka mʼmawa.+
26 Zipatso zoyamba kucha zabwino kwambiri zamʼmunda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+
Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.”+
27 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ulembe mawuwa+ chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe komanso Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”+
28 Choncho Mose anakhalabe mʼphirimo ndi Yehova masiku 40, masana ndi usiku. Iye sanadye mkate kapena kumwa madzi.+ Ndipo Mulungu analemba mawu a pangano, Malamulo Khumi,* pamiyala yosemayo.+
29 Ndiyeno Mose anatsika mʼphiri la Sinai atanyamula miyala iwiri ya Umboni ija mʼmanja mwake.+ Pamene ankatsika mʼphirimo, Mose sankadziwa kuti nkhope yake ikuwala chifukwa choti amalankhula ndi Mulungu.
30 Aroni ndi Aisiraeli onse ataona Mose, anaona kuti nkhope yake ikuwala ndipo anaopa kumuyandikira.+
31 Koma Mose anawaitana. Choncho Aroni ndi atsogoleri onse a gulu la Isiraeli anapita kwa iye, ndipo Mose analankhula nawo.
32 Kenako Aisiraeli onse anamuyandikira, ndipo iye anawapatsa malamulo onse amene Yehova anamupatsa mʼphiri la Sinai.+
33 Mose akamaliza kulankhula nawo ankaika chophimba pankhope yake.+
34 Koma Mose akamalowa mʼchihema chokumanako kukaonekera kwa Yehova kuti akalankhule naye, ankachotsa chophimbacho mpaka atatulukamo.+ Kenako ankapita kwa Aisiraeli nʼkuwauza zimene walamulidwa.+
35 Ndipo Aisiraeli anaona kuti nkhope ya Mose ikuwala. Choncho Mose anaphimbanso nkhope yake mpaka atabwerera kukalankhula ndi Mulungu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “wokhulupirika.”
^ Kapena kuti, “wachisomo.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “Yehova, dzina lake ndi amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.”
^ Kapena kuti, “amene salekerera opikisana naye.”
^ Onani Zakumapeto B15.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wotsegula mimba ya mayi ake.”
^ Kapena kuti, “muzisunga sabata.”
^ Kapena kuti, “Mawiki.”
^ Chimadziwikanso kuti Chikondwerero cha Misasa (Mahema).
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mawu Khumi.”