Ekisodo 8:1-32
8 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao, ukamuuze kuti, ‘Yehova akuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+
2 Ukapitiriza kukana kuti apite, ndigwetsa mliri wa achule+ mʼdziko lako lonse.
3 Achulewo adzachuluka kwambiri mumtsinje wa Nailo ndipo adzatuluka mumtsinjemo nʼkulowa mʼnyumba yako, mʼchipinda chako chogona, pabedi pako ndiponso mʼnyumba za atumiki ako, za anthu ako, mʼmauvuni ako ndi mʼziwiya zako zokandiramo ufa.+
4 Ndipo achulewo adzabwera kwa iwe, anthu ako ndi atumiki ako onse.”’”
5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tambasula dzanja lako nʼkulozetsa ndodo yako kumitsinje, kungalande zochokera kumtsinje wa Nailo ndi kuzithaphwi, kuti achule atuluke mmenemo nʼkubwera pamtunda mʼdziko lonse la Iguputo.’”
6 Choncho Aroni anatambasula dzanja lake nʼkuloza madzi onse a mu Iguputo, ndipo achule anayamba kutuluka ndi kudzaza dziko lonse la Iguputo.
7 Komabe, ansembe ochita zamatsenga anachitanso zomwezo mwa matsenga awo, ndipo anachititsa achule kubwera pamtunda mʼdziko la Iguputo.+
8 Kenako Farao anaitana Mose ndi Aroni nʼkuwauza kuti: “Chondererani Yehova kuti achotse achule pa ine ndi anthu anga,+ chifukwa ndikufuna kulola anthu anu kuti apite kukapereka nsembe kwa Yehova.”
9 Ndiyeno Mose anauza Farao kuti: “Munene ndinu kuti ndikachonderere liti kwa Mulungu kuti achulewa achoke kwa inu, kwa atumiki anu, anthu anu ndi mʼnyumba zanu. Achulewa adzangotsala mumtsinje wa Nailo mokha.”
10 Pamenepo Farao anayankha kuti: “Mawa.” Ndiyeno Mose anati: “Zichitika mogwirizana ndi zimene mwanena kuti mudziwe kuti palibenso wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu.+
11 Achulewa adzachoka kwa inu, mʼnyumba zanu, kwa atumiki anu ndi kwa anthu anu. Adzangotsala mumtsinje wa Nailo mokha.”+
12 Choncho Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa Farao, ndipo Mose anachonderera Yehova kuti achotse achule amene Iye anagwetsera Farao.+
13 Zitatero Yehova anachita mogwirizana ndi zimene Mose anapempha, ndipo achule amene anali mʼnyumba, mʼmabwalo ndi mʼminda anayamba kufa.
14 Aiguputo anayamba kuunjika achulewo mʼmilu yosawerengeka ndipo dziko lonselo linayamba kununkha.
15 Farao ataona kuti mliri wa achulewo watha, anaumitsa mtima wake,+ ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.
16 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako nʼkumenya fumbi lapansi kuti likhale tizilombo toyamwa magazi* mʼdziko lonse la Iguputo.’”
17 Iwo anachitadi zomwezo. Aroni anatambasula dzanja lake nʼkumenya fumbi lapansi ndi ndodo yake, ndipo tizilomboto tinayamba kusowetsa mtendere anthu ndi nyama zomwe. Fumbi lonse lamʼdziko la Iguputo linasanduka tizilombo toyamwa magazi.+
18 Ansembe ochita zamatsenga anayesanso kuti apange tizilombo toyamwa magazi pogwiritsa ntchito matsenga awo,+ koma analephera. Ndipo tizilomboto tinkasowetsa mtendere anthu ndi nyama zomwe.
19 Ataona zimenezi ansembe ochita zamatsenga aja anauza Farao kuti: “Chimenechi ndi chala cha Mulungu!”+ Koma Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake ndipo sanawamvere, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.
20 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Mawa ulawirire mʼmamawa kwambiri kukakumana ndi Farao akamadzapita kumtsinje, ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.
21 Koma ngati sulola kuti anthu anga apite, nditumiza ntchentche zoluma kwa iweyo, atumiki ako, anthu ako ndi mʼnyumba zanu. Ndipo nyumba za mu Iguputo zidzangodzaziratu ndi ntchentche zimenezi komanso pena paliponse pamene pali anthu* moti adzasowa poponda.
22 Pa tsiku limenelo ndidzapatula dera la Goseni kumene kuli anthu anga. Kumeneko sikudzakhala ntchentche zoluma.+ Ndidzachita zimenezi kuti udziwe kuti ine Yehova, ndili mʼdziko lino.+
23 Ndipo zimene ndidzachitire anthu anga zidzakhala zosiyana ndi zimene ndidzachitire anthu ako. Mawa chizindikiro chimenechi chichitika.”’”
24 Yehova anachitadi zimenezi, moti ntchentche zoluma zinali paliponse mʼnyumba ya Farao, mʼnyumba za atumiki ake ndi mʼdziko lonse la Iguputo.+ Ntchentchezo+ zinabweretsa mavuto aakulu kwa anthu a ku Iguputo.
25 Zitatero, Farao anaitana Mose ndi Aroni nʼkuwauza kuti: “Pitani, kaperekeni nsembe kwa Mulungu wanu koma mʼdziko lomwe lino.”
26 Koma Mose anati: “Sizoyenera kuchita zimenezo, chifukwa nyama zomwe tingapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu zingakhale zonyansa kwa Aiguputo.+ Kodi Aiguputo sadzatiponya miyala akationa tikupereka nsembe nyama zimene amaziona kuti ndi zonyansa?
27 Ife tipita ulendo wamasiku atatu mʼchipululu, ndipo kumeneko tikapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wathu, mogwirizana ndi mmene watiuzira.”+
28 Ndiyeno Farao anati: “Ineyo ndikulolani kuti mupite, ndipo mukaperekadi nsembe kwa Yehova Mulungu wanu mʼchipululu, koma musapite kutali kwambiri. Ndichonderereni kwa Mulungu wanu.”+
29 Kenako Mose anati: “Ndikachoka pano, ndikupita kukakuchondererani kwa Yehova ndipo mawa ntchentchezi zichoka pa inu Farao, atumiki anu ndi anthu anu. Koma inu Farao musatipusitsenso posalola anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Yehova.”+
30 Zitatero Mose anachoka kwa Farao nʼkupita kukachonderera Yehova.+
31 Choncho Yehova anachita mogwirizana ndi zimene Mose anapempha, ndipo ntchentchezo zinachoka kwa Farao, atumiki ake ndi anthu ake. Sipanatsale ntchentche ngakhale imodzi.
32 Koma Farao anaumitsanso mtima wake, ndipo sanalole kuti anthuwo achoke.