Esitere 1:1-22

  • Phwando la Mfumu Ahasiwero ku Susani (1-9)

  • Mfumukazi Vasiti anakana kumvera mfumu (10-12)

  • Mfumu inafunsira malangizo kwa amuna anzeru (13-20)

  • Mfumu inatumiza makalata (21, 22)

1  Ahasiwero,* ankalamulira zigawo 127+ kuchokera ku Indiya mpaka ku Itiyopiya,* ndipo mʼmasiku ake,  mfumuyi inkakhala pampando wake mʼnyumba yachifumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.*+  Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wake, Ahasiwero anakonzera phwando akalonga ndi atumiki ake onse. Asilikali a Perisiya+ ndi Mediya,+ anthu olemekezeka ndiponso akalonga amʼzigawo za ufumu wake analinso pomwepo.  Ndipo kwa masiku ambiri, masiku okwana 180, iye anaonetsa anthuwo chuma chimene chinkachititsa kuti anthu azimulemekeza mu ufumu wake. Anawaonetsanso chuma ndi ulemerero wa ufumu wakewo.  Zimenezi zitatha, mfumu inakonza phwando la masiku 7 pabwalo la nyumba yake pomwe anadzalapo maluwa. Phwandoli inakonzera anthu onse, kaya olemekezeka kapena anthu wamba, amene ankakhala kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.*  Panali makatani a nsalu zoyera, makatani opangidwa ndi thonje labwino kwambiri ndi makatani abuluu. Makataniwo anawamanga ndi zingwe zopangidwa ndi nsalu zabwino kwambiri ndipo anawapachika mʼmikombero yasiliva yokulungidwa ndi ulusi wapepo. Mikomberoyo anaikoleka pa zipilala za miyala ya mabo. Panalinso mipando yagolide ndi siliva yokhala ngati mabedi imene inali pakhonde la miyala ya pofeli,* miyala yoyera ya mabo, ngale ndi miyala yakuda ya mabo.  Panali vinyo yemwe anthu ankamwera mʼmakapu agolide. Kapu iliyonse inali yosiyana ndi inzake, ndipo vinyo amene mfumu inapereka anali wambiri, mogwirizana ndi chuma cha mfumuyo.  Lamulo limene ankatsatira linali lakuti aliyense amwe mmene akufunira chifukwa mfumu ndi akuluakulu ogwira ntchito kunyumba yake anakonza zoti aliyense amwe mmene akufunira.  Nayenso Mfumukazi Vasiti+ anakonzera phwando azimayi kunyumba yachifumu ya Mfumu Ahasiwero. 10  Pa tsiku la 7, mtima wa mfumu utasangalala chifukwa chomwa vinyo, mfumuyo inauza Mehumani, Bizita, Haribona,+ Bigita, Abagata, Zetara ndi Karikasi, nduna 7 zomwe zinkatumikira Mfumu Ahasiwero, 11  kuti akatenge Mfumukazi Vasiti nʼkubwera naye kwa mfumu atavala duku lachifumu, kuti anthu onse ndi akalonga aone kukongola kwake, chifukwa analidi wokongola kwambiri. 12  Koma Mfumukazi Vasiti anakana atauzidwa ndi nduna zapanyumba ya mfumu kuti mfumu yalamula kuti apite. Zitatero mfumuyo inakwiya kwambiri ndipo inapsa mtima. 13  Ndiyeno mfumu inalankhula ndi amuna anzeru, odziwa miyambo ya masiku amenewo. (Zimenezi zinkathandiza kuti nkhani zokhudza mfumu zifike kwa anthu onse odziwa malamulo komanso milandu. 14  Alangizi amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali Karisena, Setara, Adimata, Tarisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, akalonga 7+ a Perisiya ndi Mediya, amene ankafika kwa mfumu komanso anali ndi maudindo akuluakulu mu ufumuwo.) 15  Mfumu inawafunsa kuti: “Mogwirizana ndi malamulo, kodi tichite chiyani ndi Mfumukazi Vasiti popeza sanamvere zimene Mfumu Ahasiwero yanena kudzera mwa nduna zake?” 16  Memukani anauza mfumu ndi akalonga kuti: “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha,+ koma walakwiranso akalonga onse ndi anthu onse amʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero. 17  Chifukwa zimene mfumukazi yachita zidziwika kwa akazi onse okwatiwa ndipo ayamba kunyoza amuna awo nʼkumanena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero anaitana Mfumukazi Vasiti, koma Vasiti anakana.’ 18  Lero akazi a akalonga a Perisiya ndi Mediya amene amva zimene mfumukazi yachita, alankhula za zimenezi ndi amuna awo ndipo zichititsa kuti ayambe kunyozana kwambiri ndiponso kukwiyitsana. 19  Ngati mungavomereze mfumu, mupereke lamulo ndipo lamuloli lilembedwe mʼmalamulo a Perisiya ndi Mediya omwe sasintha.+ Mulamule kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso panu, inu Mfumu Ahasiwero, ndipo mupereke udindo wake kwa mkazi wina, wabwino kuposa iyeyo. 20  Anthu akamva za lamulo limene muperekeli mu ufumu wanu wonse, womwe ndi waukulu, akazi onse okwatiwa azilemekeza amuna awo, kaya amunawo ndi olemekezeka kapena anthu wamba.” 21  Mawu amenewa anasangalatsa mfumu ndi akalonga, ndipo mfumuyo inachita zimene Memukani ananena. 22  Choncho mfumu inatumiza makalata mʼzigawo zonse za ufumu wake.+ Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu akumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Anachita izi kuti mwamuna aliyense azitsogolera banja lake ndiponso kuti banjalo lizilankhula chilankhulo cha mwamunayo.

Mawu a M'munsi

Anthu amati ameneyu anali Sasita Woyamba, mwana wa Dariyo Wamkulu (Dariyo Hisitasipi).
Kapena kuti, “Kusi.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
“Pofeli” ndi mtundu wa mwala wolimba kwambiri. Kawirikawiri mwala umenewu umaoneka wakuda mofiirira, wokhala ndi mawanga oyera ndipo ndi wamtengo wapatali kwambiri.