Esitere 10:1-3

  • Moredikayi anakhala wamphamvu (1-3)

10  Mfumu Ahasiwero anayambitsa ntchito ya ukapolo mʼdzikomo ndiponso pazilumba zamʼnyanja.  Zinthu zonse zimene anachita chifukwa cha mphamvu zake, ndiponso mphamvu zonse za Moredikayi+ zimene anapatsidwa ndi mfumu,+ zinalembedwa mʼbuku la mbiri+ ya mafumu a Mediya ndi Perisiya.+  Moredikayi Myuda anali wachiwiri kwa Mfumu Ahasiwero. Iye anali wamkulu pakati pa Ayuda ndipo abale ake ambiri ankamulemekeza. Moredikayi ankachitira zabwino anthu a mtundu wake ndipo ankaonetsetsa kuti mbadwa zawo zinthu zidzawayendere bwino.

Mawu a M'munsi