Esitere 3:1-15

  • Hamani anakwezedwa ndi mfumu (1-4)

  • Hamani anakonza chiwembu chopha Ayuda (5-15)

3  Kenako Mfumu Ahasiwero anakweza pa udindo Hamani+ mwana wa Hamedata mbadwa ya Agagi,+ ndipo anamupatsa mpando wapamwamba kuposa akalonga ena onse a mfumuyo.+  Choncho atumiki onse a mfumu amene ankakhala pageti la mfumu ankaweramira Hamani ndiponso kumugwadira chifukwa mfumu ndi imene inalamula kuti azimuchitira zimenezi. Koma Moredikayi ankakana kumuweramira kapena kumugwadira.  Choncho atumiki a mfumu amene ankakhala pagetiwo anafunsa Moredikayi kuti: “Nʼchifukwa chiyani sukutsatira lamulo la mfumu?”  Ankamufunsa zimenezi tsiku ndi tsiku koma iye sankawamvera. Kenako anthuwo anauza Hamani kuti aone ngati khalidwe la Moredikayi lingalekereredwe+ popeza iye anali atawauza kuti anali Myuda.+  Hamani ataona kuti Moredikayi sankamuweramira ndiponso kumugwadira, anakwiya kwambiri.+  Koma Hamani anaona kuti nʼzosakwanira kupha Moredikayi yekha chifukwa anthu anali atamuuza za anthu a mtundu wa Moredikayi. Choncho Hamani anaganiza zoti aphe Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredikayi mʼmadera onse amene Ahasiwero ankalamulira.  Ndiyeno mʼmwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani,* mʼchaka cha 12+ cha Mfumu Ahasiwero, anthu anachita Puri+ kapena kuti maere pamaso pa Hamani kuti adziwe tsiku ndi mwezi woyenerera. Maerewo anagwera mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+  Kenako Hamani anauza Mfumu Ahasiwero kuti: “Pali mtundu wina wa anthu+ umene ukupezeka paliponse mʼzigawo zonse za ufumu wanu.+ Malamulo awo ndi osiyana ndi malamulo a anthu ena onse ndipo sakutsatira malamulo anu. Choncho ngati mungawasiye anthu amenewa, zinthu sizikuyenderani bwino mfumu.  Ngati mungakonde mfumu, palembedwe lamulo loti anthu amenewa aphedwe. Ine ndidzapereka ndalama zokwana matalente* 10,000 asiliva kwa akuluakulu ogwira ntchito kunyumba ya mfumu kuti akaziike mosungiramo chuma cha mfumu.”* 10  Zitatero mfumu inavula mphete yake yodindira+ nʼkuipereka kwa Hamani+ mwana wa Hamedata, mbadwa ya Agagi,+ yemwe ankadana kwambiri ndi Ayuda. 11  Ndiyeno mfumu inauza Hamani kuti: “Siliva* komanso anthuwo ndakupatsa ndipo uchite nawo zilizonse zimene ukufuna.” 12  Kenako pa tsiku la 13 la mwezi woyamba, alembi a mfumu+ anaitanidwa. Ndipo alembiwo analemba+ zonse zimene Hamani analamula masatarapi* a mfumu, abwanamkubwa a mʼzigawo zosiyanasiyana ndiponso akalonga a anthu osiyanasiyana. Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu a kumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Makalatawa anawalemba mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndipo anawadinda ndi mphete yodindira ya mfumuyo.+ 13  Makalatawo anawatumiza kuzigawo zonse za mfumu kudzera mwa anthu operekera makalata. Anachita izi kuti tsiku limodzi, tsiku la 13 la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara,+ aphe Ayuda onse, kaya ndi achinyamata, amuna achikulire, ana ndiponso akazi nʼkutenga zinthu zawo.+ 14  Lamulo lopita kuzigawo zonse, limene analilemba mʼmakalatawo, linafalitsidwa kwa anthu a mitundu yonse kuti akonzekere tsiku limeneli. 15  Mfumu inalamula kuti operekera makalatawo apite mwamsanga.+ Lamuloli linaperekedwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Susani*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako mfumu ndi Hamani, anakhala pansi nʼkumamwa vinyo, koma mumzinda wa Susani munali chipwirikiti.

Mawu a M'munsi

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Mabaibulo ena amati, “Ine ndidzapereka ndalama zokwana matalente 10,000 asiliva kuti akaziike mosungiramo chuma cha mfumu zoti zipite kwa anthu amene adzagwire ntchitoyi.”
Nʼkutheka kuti amanena za siliva amene akatenge akakapha Ayuda.
Limeneli ndi dzina laudindo la anthu oteteza ufumu.
Kapena kuti, “Susa.”