Esitere 4:1-17

  • Moredikayi analira (1-5)

  • Moredikayi anapempha Esitere kuti athandize (6-17)

4  Moredikayi+ atadziwa zonse zimene zinachitika,+ anangʼamba zovala zake nʼkuvala chiguduli ndipo anadzithira phulusa. Kenako anapita pakati pa mzinda nʼkuyamba kulira mofuula ndiponso mopwetekedwa mtima.  Koma anangofika pageti la mfumu chifukwa palibe amene ankaloledwa kulowa pageti la mfumu atavala chiguduli.  Ndipo mʼzigawo zonse+ kumene kunafika mawu a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali ndi chisoni kwambiri ndipo ankasala kudya+ komanso kulira mofuula. Ambiri ankagona paziguduli ndi paphulusa.+  Atsikana otumikira Mfumukazi Esitere ndiponso amuna ofulidwa amene ankamuyangʼanira atabwera nʼkudzamuuza zimenezi, zinamukhudza kwambiri. Choncho anatumiza zovala kuti Moredikayi akavale mʼmalo mwa zigudulizo, koma Moredikayi anakana.  Ndiyeno Esitere anaitana Hataki, mmodzi wa amuna ofulidwa a mfumu amene mfumuyo inamuika kuti azitumikira Esitere. Ndipo anamutuma kwa Moredikayi kuti akafufuze zimene zachitika.  Choncho Hataki anapita kwa Moredikayi kubwalo la mzinda limene linali kutsogolo kwa geti la mfumu.  Moredikayi anauza Hataki zonse zimene zinamuchitikira. Anamuuzanso zokhudza ndalama zonse+ zimene Hamani analonjeza kuti apereka mosungiramo chuma cha mfumu, nʼcholinga choti aphe Ayuda.+  Anamupatsanso kalata imene munali lamulo lochokera ku Susani*+ loti Ayuda onse aphedwe. Anamupatsa kalatayi kuti akaonetse Esitere ndiponso akamufotokozere mmene zinthu zilili. Moredikayi anauzanso Hataki kuti akauze Esitere+ kuti akaonekere kwa mfumu nʼkupempha kuti imuchitire chifundo ndiponso kuti akachonderere mfumuyo pamasomʼpamaso mʼmalo mwa anthu a mtundu wake.  Ndiyeno Hataki anapita kukauza Esitere zimene Moredikayi ananena. 10  Kenako Esitere anauza Hataki kuti akauze Moredikayi kuti:+ 11  “Atumiki onse a mfumu ndi anthu amʼzigawo zonse za mfumu akudziwa kuti, pali lamulo lakuti mwamuna kapena mkazi aliyense wopita mʼbwalo lamkati+ la mfumu asanaitanidwe, ayenera kuphedwa. Munthu saphedwa pokhapokha ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yake yagolide.+ Ndiye ine sindinaitanidwe kukaonekera kwa mfumu kwa masiku 30 tsopano.” 12  Moredikayi atauzidwa zimene Esitere ananena, 13  anayankha Esitere kuti: “Usaganize kuti chifukwa chakuti uli mʼnyumba ya mfumu, iweyo udzapulumuka Ayuda onse akamadzaphedwa. 14  Ngati iwe ungakhale chete panopa, thandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zichokera kwina.+ Koma iweyo ndi anthu a mʼnyumba ya bambo ako, nonse mudzaphedwa. Ndipo ndani akudziwa? Mwina iwe unakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.”+ 15  Esitere anayankha Moredikayi kuti: 16  “Pitani mukasonkhanitse Ayuda onse amene ali ku Susani* ndipo musale kudya+ mʼmalo mwa ine. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu,+ masana ndiponso usiku. Inenso ndi atsikana onditumikira tisala kudya. Ngakhale kuti ndi zosemphana ndi lamulo, ndidzapita kwa mfumu ndipo ngati nʼkufa, ndife.” 17  Choncho Moredikayi anapita kukachita zonse zimene Esitere anamuuza.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”