Esitere 5:1-14

  • Esitere anaonekera kwa mfumu (1-8)

  • Hamani anasonyeza kukwiya komanso kudzikweza (9-14)

5  Pa tsiku lachitatu,+ Esitere anavala zovala zachifumu nʼkukaima mʼbwalo lamkati la nyumba ya mfumu kutsogolo kwa nyumba ya mfumuyo. Pa nthawiyi nʼkuti mfumu itakhala pampando wake wachifumu mʼnyumba yakeyo pafupi ndi khomo la nyumbayo.  Mfumuyo itangoona Mfumukazi Esitere ataima mʼbwalo la nyumba ya mfumu, inasangalala moti inamuloza ndi ndodo yachifumu yagolide+ imene inali mʼmanja mwake. Kenako Esitere anayandikira nʼkugwira kutsogolo kwa ndodoyo.  Kenako mfumu inamufunsa kuti: “Chavuta nʼchiyani Mfumukazi Esitere? Ukufuna kupempha chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumu wangawu, ndikupatsa.”  Esitere anati: “Ngati mungavomereze mfumu, inu ndi Hamani+ mubwere lero kuphwando limene ine ndakukonzerani.”  Ndiyeno mfumu inauza atumiki ake kuti: “Pitani mukamuuze Hamani kuti abwere mofulumira mogwirizana ndi zimene Esitere wapempha.” Choncho mfumu ndi Hamani anapita kuphwando limene Esitere anakonza.  Pa nthawi yomwe ankamwa vinyo paphwandolo, mfumu inafunsa Esitere kuti: “Ukufuna kupempha chiyani? Chimene ukufuna ndikupatsa. Ukufuna ndikupatse chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumu wangawu, ndikupatsa.”+  Esitere anayankha kuti: “Pempho langa ndi ili,  Ngati mungandikomere mtima mfumu ndiponso ngati mungakonde kundipatsa zimene ndapempha nʼkuchita zomwe ndikufuna, inu mfumu ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndidzakukonzereni mawa. Ndipo mawa ndidzakuuzani pempho langa ngati mmene inu mfumu mwanenera.”  Pa tsikuli Hamani anatuluka ali wosangalala kwambiri. Koma atangoona Moredikayi pageti la mfumu nʼkuonanso kuti sanaimirire ndi kumunjenjemerera, Hamani anamukwiyira kwambiri Moredikayi.+ 10  Koma Hamani anaugwira mtima ndipo anapita kunyumba kwake. Kenako anaitanitsa anzake ndi mkazi wake Zeresi.+ 11  Ndiyeno Hamani anayamba kudzitama kuti ali ndi chuma chambiri, ana aamuna ambiri+ ndiponso kuti mfumu inamukweza pa udindo kuposa akalonga ndi atumiki ena onse a mfumuyo.+ 12  Hamani ananenanso kuti: “Kuwonjezera pamenepo, Mfumukazi Esitere sanaitane wina aliyense kuphwando limene anakonza,+ koma anaitana ineyo kuti ndipite ndi mfumu, ndipo mawa wandiitananso pamodzi ndi mfumu.+ 13  Koma zonsezi sizikundikwanira ndikamaona Moredikayi, Myuda, atakhala pageti la mfumu.” 14  Choncho mkazi wake Zeresi ndiponso anzake onsewo anamuuza kuti: “Mukonzetse mtengo wautali mikono 50.* Ndiyeno mawa mʼmawa mukauze mfumu kuti Moredikayi apachikidwe pamtengowo.+ Mukatero mukapite ndi mfumu kuphwandoko kukasangalala.” Hamani anaona kuti maganizo amenewa ndi abwino, choncho anakonzetsa mtengowo.

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi mamita pafupifupi 22.3. Onani Zakumapeto B14.