Esitere 6:1-14

  • Moredikayi analemekezedwa ndi mfumu (1-14)

6  Usiku wa tsiku limenelo mfumu inasowa tulo. Choncho inaitanitsa buku lomwe ankalembamo zochitika za masiku amenewo+ ndipo anayamba kuwerengera mfumu zimene zinalembedwa mʼbukulo.  Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zimene Moredikayi anaulula zokhudza Bigitana ndi Teresi, nduna ziwiri zapanyumba ya mfumu, alonda apakhomo, amene ankafuna kupha Mfumu Ahasiwero.+  Ndiyeno mfumu inafunsa kuti: “Kodi Moredikayi analandira ulemu wotani chifukwa cha zimene anachitazi?” Atumiki a mfumu anayankha kuti: “Palibe chilichonse chimene anachitiridwa.”  Kenako mfumu inati: “Kodi pabwalopo pali ndani?” Pa nthawiyi nʼkuti Hamani atafika pabwalo lakunja+ la nyumba ya mfumu kudzakambirana ndi mfumuyo zoti Moredikayi apachikidwe pamtengo umene anamukonzera.+  Atumiki a mfumu anati: “Pabwalo pali Hamani.”+ Ndiyeno mfumu inati: “Muuzeni alowe.”  Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti: “Kodi tingamuchitire chiyani munthu amene mfumu ikufuna kumupatsa ulemu?” Hamani atamva zimenezi anaganiza kuti: “Kodi winanso ndani amene mfumu ingafune kumupatsa ulemu kuposa ine?”+  Choncho Hamani anauza mfumu kuti: “Munthu amene mfumu ikufuna kumupatsa ulemu,  amubweretsere zovala zachifumu zimene mfumu imavala+ ndi hatchi* imene mfumu imakwera ndipo hatchiyo aiveke duku lachifumu.  Ndiyeno chovalacho ndi hatchiyo azipereke kwa mmodzi wa akalonga olemekezeka a mfumu. Kenako aveke chovalacho munthu amene mfumu ikufuna kumupatsa ulemuyo ndipo amukweze pahatchiyo nʼkumuyendetsa mʼbwalo la mzinda. Ndiye azifuula patsogolo pake kuti, ‘Izi ndi zimene timachitira munthu amene mfumu yafuna kumʼpatsa ulemu!’”+ 10  Nthawi yomweyo mfumu inauza Hamani kuti: “Fulumira, tenga chovala ndi hatchi ngati mmene wanenera, ndipo ukachitire zimenezi Moredikayi, Myuda, amene ali kugeti. Uonetsetse kuti wachita zonse zimene wanenazi.” 11  Choncho Hamani anatenga chovala ndi hatchi, ndipo anaveka Moredikayi+ chovalacho. Kenako anamʼkweza pahatchiyo nʼkumuyendetsa mʼbwalo la mzinda, akufuula patsogolo pake kuti: “Izi ndi zimene timachitira munthu amene mfumu yafuna kumʼpatsa ulemu!” 12  Kenako, Moredikayi anabwerera kugeti la mfumu. Koma Hamani anapita kunyumba kwake mofulumira, akulira ndiponso ataphimba kumutu. 13  Hamani atafotokozera mkazi wake Zeresi+ ndiponso anzake onse zonse zimene zinamuchitikira, amuna anzeru amene ankamutumikira komanso mkazi wakeyo anati: “Ngati wayamba kufooka pamaso pa Moredikayi, yemwe ndi Myuda, ndiye kuti supambana koma akugonjetsa ndithu.” 14  Ali mkati mokambirana nkhaniyi, nduna zakunyumba ya mfumu zinafika, ndipo nthawi yomweyo zinatenga Hamani nʼkupita naye kuphwando limene Esitere anakonza.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “hosi.”