Esitere 9:1-32

  • Ayuda anapambana (1-19)

  • Anakhazikitsa chikondwerero cha Purimu (20-32)

9  Tsiku la 13 la mwezi wa 12, umene ndi mwezi wa Adara,*+ linali tsiku limene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinayenera kuchitika.+ Limeneli linali tsiku limene adani a Ayuda ankayembekezera kugonjetsa Ayudawo. Koma pa tsikuli zinthu zinasintha, moti Ayuda ndi amene anagonjetsa adani awowo.+  Ayuda anasonkhana mʼmizinda yawo mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero+ kuti amenyane ndi adani awo amene ankafuna kuwapha. Ndipo palibe munthu amene anakwanitsa kulimbana nawo chifukwa anthu a mitundu yonse ankaopa Ayudawo.+  Akalonga onse a mʼzigawo, masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi onse ogwira ntchito za mfumu ankathandiza Ayudawo chifukwa ankaopa Moredikayi.  Moredikayi anali ndi mphamvu zambiri+ mʼnyumba ya mfumu ndipo anatchuka mʼzigawo zonse chifukwa anapitiriza kukhala ndi mphamvu.  Ndiyeno Ayuda anapha adani awo onse ndi lupanga. Ayudawo anachita zonse zimene ankafuna kwa adani awo.+  Kunyumba ya mfumu ya ku Susani,*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, Ayudawo anapha amuna 500.  Anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata,  Porata, Adaliya, Aridata,  Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaizata, 10  omwe anali ana aamuna 10 a Hamani mwana wa Hamedata yemwe ankadana ndi Ayuda.+ Koma atawapha, sanatenge zinthu zawo.+ 11  Pa tsikuli mfumu inauzidwa chiwerengero cha anthu amene anaphedwa kunyumba ya mfumu ya ku Susani* yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. 12  Ndiyeno mfumu inauza Mfumukazi Esitere kuti: “Kunyumba ya mfumu ya ku Susani* yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, Ayuda apha amuna 500 komanso ana 10 a Hamani. Ndiye kuli bwanji mʼzigawo zina zonse za mfumu?+ Panopa ukufuna kupempha chiyani? Ndikupatsa. Pali zinanso zimene ukufuna kupempha? Zimene ukufuna zichitika.” 13  Esitere anayankha kuti: “Ngati mungavomereze mfumu,+ bwanji mawa Ayuda amene ali ku Susani* achitenso zimene lamulo laleroli likunena?+ Ndikupemphanso kuti ana aamuna 10 a Hamani apachikidwe pamtengo.”+ 14  Choncho mfumu inalamula kuti achite zimenezo ndipo lamulo linaperekedwa ku Susani.* Komanso ana aamuna 10 a Hamani anapachikidwa. 15  Ndiyeno Ayuda amene anali ku Susani* anasonkhananso pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara,+ ndipo anapha amuna 300 ku Susani, koma sanatenge zinthu zawo. 16  Nawonso Ayuda ena onse amene anali mʼzigawo za mfumu anasonkhana kuti adziteteze.+ Ndipo anapha adani awo+ okwana 75,000 koma sanatenge zinthu zawo. 17  Limeneli linali tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Ndiyeno pa tsiku la 14 anapuma nʼkuchita phwando ndipo anasangalala kwambiri. 18  Ayuda amene anali ku Susani* anasonkhana pa tsiku la 13+ ndi la 14+ la mweziwo. Iwo anapuma pa tsiku la 15 ndipo anachita phwando komanso chikondwerero. 19  Nʼchifukwa chake Ayuda akumidzi amene ankakhala mʼmadera akutali ndi mzinda, anasankha kuti tsiku la 14 la mwezi wa Adara likhale tsiku lachikondwerero, lochita phwando, losangalala+ ndiponso lotumizirana chakudya.+ 20  Ndiyeno Moredikayi+ analemba zimene zinachitikazi nʼkutumiza makalata kwa Ayuda onse amene anali mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero, zakutali ndiponso zapafupi. 21  Mʼmakalatawo anawauza kuti pa tsiku la 14 ndi la 15 la mwezi wa Adara azichita chikondwerero chimenechi chaka chilichonse. 22  Anawauza zimenezi chifukwa masiku amenewa Ayuda anasiya kuvutitsidwa ndi adani awo, komanso mʼmwezi umenewu chisoni chawo chinasintha nʼkukhala chikondwerero ndipo tsiku lolira+ linasintha nʼkukhala tsiku losangalala. Masiku amenewa ankayenera kukhala ochita phwando, kusangalala, kutumizirana chakudya ndiponso kupereka mphatso kwa anthu osauka. 23  Ndipo Ayuda anavomereza kuti apitiriza chikondwerero chimene anali atayamba kale komanso achita zimene Moredikayi anawalembera. 24  Izi zinali choncho chifukwa Hamani+ mwana wa Hamedata, mbadwa ya Agagi,+ amene ankadana ndi Ayuda onse, anawakonzera Ayudawo chiwembu kuti awaphe.+ Ndiponso iye anachita Puri+ kapena kuti maere, nʼcholinga choti awasokoneze maganizo nʼkuwapha. 25  Koma Esitere atakaonekera kwa mfumu, mfumuyo inalemba+ lamulo lakuti: “Chiwembu chimene anakonzera Ayuda+ chimubwerere iyeyo.” Choncho Hamani komanso ana ake anawapachika pamtengo.+ 26  Nʼchifukwa chake masiku amenewa anawapatsa dzina lakuti Purimu, kutengera dzina lakuti Puri.*+ Choncho chifukwa cha zonse zomwe zinalembedwa mʼkalatayi, zimene anaona pa nkhani imeneyi komanso zimene zinawachitikira, 27  Ayudawo analonjeza kuti iwo, mbadwa zawo ndiponso anthu onse amene anakhala kumbali yawo,+ azichita chikondwerero masiku awiri amenewa komanso azichita zimene zinalembedwa zokhudza masikuwa pa nthawi yake chaka chilichonse. 28  Mʼbadwo uliwonse uyenera kukumbukira masiku amenewa ndipo zizichitika mʼbanja lililonse, chigawo chilichonse ndiponso mzinda uliwonse. Ayuda sayenera kusiya kukumbukira masiku a Purimu ndipo mbadwa zawo siziyenera kusiya kukumbukira masiku amenewa. 29  Ndiyeno Mfumukazi Esitere, mwana wa Abihaili, komanso Moredikayi Myuda, analemba kalata yachiwiri ndi ulamuliro wonse, kutsimikizira za Purimu. 30  Kenako anatumiza makalata okhala ndi mawu amtendere ndiponso oona kwa Ayuda onse mʼzigawo 127+ zimene Ahasiwero ankalamulira.+ 31  Anatumiza makalatawo kuti atsimikizire kuti azichita chikondwerero cha Purimu pa nthawi yake, mogwirizana ndi zimene Moredikayi Myuda ndi Mfumukazi Esitere anawalamulira kuti azichita.+ Komanso mogwirizana ndi zimene analonjeza kuti Ayudawo ndi mbadwa zawo azichita,+ kuphatikizapo kusala kudya+ komanso kupemphera mochonderera.+ 32  Choncho lamulo la Esitere linatsimikizira nkhani zimenezi zokhudza Purimu+ ndipo zinalembedwa mʼbuku.

Mawu a M'munsi

Limeneli ndi dzina laudindo la anthu oteteza ufumu.
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Mawu akuti “Puri” amatanthauza “Maere.” Koma kenako mawu akuti “Purimu,” komwe ndi kuchulukitsa, anayamba kuwagwiritsa ntchito ponena za chikondwerero cha Ayuda cha mwezi wa 12 pakalendala yopatulika. Onani Zakumapeto B15.