Ezara 10:1-44

  • Pangano loti achotse akazi a mitundu ina (1-14)

  • Akazi a mitundu ina anatumizidwa kwawo (15-44)

10  Pamene Ezara ankapemphera+ komanso kuvomereza machimo, zomwe ankachita akulira ndiponso atagona patsogolo pa nyumba ya Mulungu woona, gulu lalikulu la Aisiraeli linamuzungulira. Panali amuna, akazi ndi ana ndipo ankalira kwambiri.  Kenako Sekaniya mwana wa Yehiela+ wochokera mwa ana a Elamu+ anauza Ezara kuti: “Ifeyo tachita zosakhulupirika kwa Mulungu wathu chifukwa tinakwatira akazi achilendo kuchokera kwa anthu a mitundu ina.+ Ngakhale zili choncho, Aisiraeli ali ndi chiyembekezo.  Tsopano tiyeni tichite pangano ndi Mulungu wathu,+ kuti tisiya akazi onsewa komanso ana awo mogwirizana ndi lamulo la Yehova ndiponso anthu amene amalemekeza lamulo la Mulungu.+ Tiyeni tichite zinthu mogwirizana ndi Chilamulo.  Choncho dzuka, chifukwa nkhaniyi ili mʼmanja mwako ndipo ife tili nawe. Uchite zinthu mwamphamvu.”  Choncho Ezara ananyamuka nʼkuuza atsogoleri a ansembe, a Alevi ndi a Aisiraeli onse kuti alumbire kuti achita mogwirizana ndi zimene ananena+ ndipo analumbiradi.  Kenako Ezara anachoka panyumba ya Mulungu woona nʼkupita kuchipinda chodyera cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu. Ngakhale kuti anapita kumeneko, sanadye chakudya kapena kumwa madzi, popeza ankalira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu ochokera ku ukapolo aja.+  Ndiyeno analengeza ku Yuda ndi ku Yerusalemu konse kuti anthu onse amene anachokera ku ukapolo asonkhane ku Yerusalemu,  ndipo mogwirizana ndi lamulo la akalonga ndi akulu, aliyense amene sabwera pakapita masiku atatu, katundu wake yense alandidwa ndipo iyeyo achotsedwa pa gulu la anthu amene anachokera ku ukapolo.+  Choncho pasanathe masiku atatu, amuna onse a fuko la Yuda ndi la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu. Zimenezi zinachitika pa tsiku la 20 la mwezi wa 9. Anthu onsewo anakhala pabwalo la nyumba ya Mulungu woona, akunjenjemera chifukwa cha nkhaniyo komanso chifukwa kunkagwa mvula yambiri. 10  Kenako wansembe Ezara anaimirira nʼkuuza anthuwo kuti: “Inu mwachita zosakhulupirika chifukwa mwatenga akazi achilendo+ ndipo mwawonjezera machimo a Isiraeli. 11  Choncho vomerezani machimo anu kwa Yehova Mulungu wa makolo anu ndipo chitani zomusangalatsa. Musiyane ndi anthu a mitundu ina ndiponso akazi achilendowa.”+ 12  Gulu lonselo linayankha mokweza kuti: “Tichita ndendende mogwirizana ndi zimene mwanena. 13  Koma tilipo anthu ambiri ndipo ino ndi nyengo ya mvula, choncho nʼzosatheka kuima panja. Komanso nkhani imeneyi sitenga tsiku limodzi kapena masiku awiri chifukwa tachimwa kwambiri. 14  Choncho lolani kuti akalonga athu aimire anthu onse+ ndipo aliyense mʼmizinda yathu, amene wakwatira mkazi wachilendo, abwere pa nthawi imene ikhazikitsidwe. Abwere limodzi ndi akulu a mzinda uliwonse ndi oweruza ake, mpaka titabweza mkwiyo wa Mulungu wathu amene watikwiyira kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi.” 15  Koma Yonatani mwana wa Asaheli ndi Yahazeya mwana wa Tikiva anatsutsa zimenezi, ndipo Mesulamu ndi Sabetai,+ omwe anali Alevi, anawathandiza. 16  Anthu amene anachokera ku ukapolowo anachita zimene anagwirizanazo. Choncho wansembe Ezara ndi amuna onse amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, omwe anachita kuwatchula mayina awo, anachoka pakati pa anthuwo nʼkukakhala pansi kuti afufuze nkhaniyo. Anachita zimenezi pa tsiku loyamba la mwezi wa 10. 17  Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba, anathetsa nkhani zonse zokhudza amuna amene anatenga akazi achilendo. 18  Iwo anapeza kuti ana ena a ansembe anakwatira akazi achilendo.+ Kuchokera pa ana a Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ndi abale ake, panali Maaseya, Eliezere, Yaribi ndi Gedaliya. 19  Koma iwo analonjeza kuti asiya akazi awo komanso popeza anachimwa, apereka nkhosa yamphongo chifukwa cha tchimo lawolo.+ 20  Pa ana a Imeri+ panali Haneni ndi Zebadiya. 21  Pa ana a Harimu+ panali Maaseya, Eliya, Semaya, Yehiela ndi Uziya. 22  Pa ana a Pasuri+ panali Elioenai, Maaseya, Isimaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa. 23  Pa Alevi panali Yozabadi, Simeyi, Kelaya (kapena kuti Kelita), Petahiya, Yuda ndi Eliezere. 24  Pa oimba panali Eliyasibu. Pa alonda apageti panali Salumu, Telemu ndi Uri. 25  Kuchokera pa Aisiraeli, pa ana a Parosi+ panali Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eliezara, Malikiya ndi Benaya. 26  Pa ana a Elamu+ panali Mataniya, Zekariya, Yehiela,+ Abidi, Yeremoti ndi Eliya. 27  Pa ana a Zatu+ panali Elioenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza. 28  Pa ana a Bebai+ panali Yehohanani, Hananiya, Zabai ndi Atilai. 29  Pa ana a Bani panali Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubi, Seali ndi Yeremoti. 30  Pa ana a Pahati-mowabu+ panali Adena, Kelali, Benaya, Maaseya, Mataniya, Bezaleli, Binui ndi Manase. 31  Pa ana a Harimu+ panali Eliezere, Isihiya, Malikiya,+ Semaya, Simeoni, 32  Benjamini, Maluki ndi Semariya. 33  Pa ana a Hasumu+ panali Matenai, Mateta, Zabadi, Elifeleti, Yeremai, Manase ndi Simeyi. 34  Pa ana a Bani panali Maadai, Amuramu, Ueli, 35  Benaya, Bedeya, Kelui, 36  Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37  Mataniya, Matenai ndi Yaasu. 38  Pa ana a Binui panali Simeyi, 39  Selemiya, Natani, Adaya, 40  Makinadebai, Sasai, Sarayi, 41  Azareli, Selemiya, Semariya, 42  Salumu, Amariya ndi Yosefe. 43  Pa ana a Nebo panali Yeyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya. 44  Onsewa anatenga akazi achilendo+ ndipo akaziwo ndi ana awo anawatumiza kwawo.+

Mawu a M'munsi