Ezara 2:1-70

  • Anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo (1-67)

    • Atumiki a pakachisi (43-54)

    • Ana a atumiki a Solomo (55-57)

  • Zopereka zaufulu pakachisi (68-70)

2  Awa ndi anthu amʼchigawo* amene anatuluka mu ukapolo+ pa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+  Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,*+ Nehemiya, Seraya, Reelaya, Moredikayi, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Bana. Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:+  Ana a Parosi, 2,172.  Ana a Sefatiya, 372.  Ana a Ara,+ 775.  Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu, 2,812.  Ana a Elamu,+ 1,254.  Ana a Zatu,+ 945.  Ana a Zakai, 760. 10  Ana a Bani, 642. 11  Ana a Bebai, 623. 12  Ana a Azigadi, 1,222. 13  Ana a Adonikamu, 666. 14  Ana a Bigivai, 2,056. 15  Ana a Adini, 454. 16  Ana a Ateri, a mʼbanja la Hezekiya, 98. 17  Ana a Bezai, 323. 18  Ana a Yora, 112. 19  Ana a Hasumu,+ 223. 20  Ana a Gibara, 95. 21  Ana a Betelehemu, 123. 22  Amuna a ku Netofa, 56. 23  Amuna a ku Anatoti,+ 128. 24  Ana a Azimaveti, 42. 25  Ana a Kiriyati-yearimu, Kefira ndi Beeroti, 743. 26  Ana a Rama+ ndi Geba,+ 621. 27  Amuna a ku Mikemasi, 122. 28  Amuna a ku Beteli ndi a ku Ai,+ 223. 29  Ana a Nebo,+ 52. 30  Ana a Magabisi, 156. 31  Ana a Elamu wina, 1,254. 32  Ana a Harimu, 320. 33  Ana a Lodi, Hadidi ndi Ono, 725. 34  Ana a Yeriko, 345. 35  Ana a Senaya, 3,630. 36  Ansembe:+ Ana a Yedaya,+ a mʼbanja la Yesuwa,+ 973. 37  Ana a Imeri,+ 1,052. 38  Ana a Pasuri,+ 1,247. 39  Ana a Harimu,+ 1,017. 40  Alevi:+ Ana a Yesuwa, a mʼbanja la Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodaviya, 74. 41  Oimba,+ ana a Asafu,+ 128. 42  Ana a alonda apageti:+ ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita ndi ana a Sobai, onse analipo 139. 43  Atumiki apakachisi:*+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, 44  ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni, 45  ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu, 46  ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani, 47  ana a Gideli, ana a Gahara, ana a Reyaya, 48  ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu, 49  ana a Uziza, ana a Paseya, ana a Besai, 50  ana a Asena, ana a Meyuni, ana a Nefusimu, 51  ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, 52  ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa, 53  ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, 54  ana a Neziya ndi ana a Hatifa. 55  Ana a atumiki a Solomo: Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,+ 56  ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli, 57  ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu ndi ana a Ami. 58  Atumiki onse apakachisi* pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392. 59  Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi, ndi awa:+ 60  ana a Delaya, ana a Tobia ndi ana a Nekoda, 652. 61  Ana a ansembe anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi,+ ana a Barizilai amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ wa ku Giliyadi nʼkuyamba kutchedwa ndi dzina lawo. 62  Amenewa ndi amene mayina awo anawayangʼana mʼkaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Choncho anawaletsa kuti asatumikire ngati ansembe.*+ 63  Choncho, bwanamkubwa* anawauza kuti asamadye zinthu zopatulika koposa,+ mpaka patakhala wansembe amene angagwiritse ntchito Urimu ndi Tumimu.+ 64  Anthu onse analipo 42,360.+ 65  Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi aakazi amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi okwana 200. 66  Anali ndi mahatchi* 736 ndi nyulu* 245. 67  Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720. 68  Atsogoleri ena a nyumba za makolo awo atafika kunyumba ya Yehova imene inali ku Yerusalemu, anapereka zopereka zaufulu+ kunyumba ya Mulungu woona kuti imangidwenso pamalo ake.+ 69  Mogwirizana ndi chuma chawo, anapereka zinthu zoti zithandize pa ntchitoyo. Anapereka madalakima* agolide 61,000, ma mina*+ asiliva 5,000 ndi mikanjo 100 ya ansembe. 70  Ndiyeno ansembe, Alevi, anthu ena, oimba, alonda apageti, atumiki apakachisi* ndi Aisiraeli onse anayamba kukhala mʼmizinda yawo.+

Mawu a M'munsi

Nʼkutheka kuti chinali chigawo cha ku Babulo kapena cha ku Yuda.
Nʼkutheka kuti akunena za “Yoswa” yemwe akutchulidwa pa Hag 1:1 ndi Zek 3:1.
Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
Kapena kuti, “anawachotsa pa udindo wokhala ansembe chifukwa anali odetsedwa.”
Kapena kuti, “Tirisata.” Dzinali ndi la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.
Ena amati “mahosi.”
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
“Dalakima” imeneyi inali yofanana ndi ndalama yagolide ya ku Perisiya yotchedwa dariki, yomwe inkalemera magalamu 8.4. Koma si yofanana ndi dalakima yomwe imatchulidwa mʼMalemba a Chigiriki. Onani Zakumapeto B14.
“Mina” yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi inkalemera magalamu 570. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”