Ezara 3:1-13

  • Anamanganso guwa nʼkuperekapo nsembe (1-6)

  • Ntchito yomanganso kachisi inayambika (7-9)

  • Anamanga maziko a kachisi (10-13)

3  Pofika mwezi wa 7,+ Aisiraeli omwe ankakhala mʼmizinda yawo anasonkhana limodzi mogwirizana ku Yerusalemu.  Kenako Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ndi ansembe anzake ndiponso Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi abale ake, anakamanga guwa lansembe la Mulungu wa Isiraeli. Anachita zimenezi kuti aziperekerapo nsembe zopsereza, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Mose,+ munthu wa Mulungu woona.  Iwo anamanga guwa lansembe pamalo ake akale ngakhale kuti ankaopa anthu a mitundu ina yowazungulira.+ Atatero anayamba kuperekerapo nsembe zopsereza kwa Yehova, zamʼmawa ndi zamadzulo.+  Kenako anachita Chikondwerero cha Misasa mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+ Tsiku ndi tsiku ankapereka nsembe zopsereza zomwe zinkayenera kuperekedwa tsiku lililonse.+  Ndiyeno anayamba kupereka nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku,+ nsembe ya masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi nsembe za pa zikondwerero zopatulika+ za Yehova. Anaperekanso nsembe za aliyense amene anapereka chopereka chaufulu+ kwa Yehova ndi mtima wonse.  Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wa 7+ kupita mʼtsogolo, anthuwo anayamba kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Pa nthawiyi nʼkuti maziko a kachisi wa Yehova asanamangidwe.  Kenako anthuwo anapereka ndalama kwa anthu osema miyala+ ndi amisiri.+ Anaperekanso chakudya, zakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi ku Turo chifukwa anabweretsa matabwa a mkungudza kudzera panyanja kuchokera ku Lebanoni kukafika ku Yopa.+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi chilolezo chimene Koresi mfumu ya ku Perisiya anawapatsa.+  Mʼchaka chachiwiri kuchokera pamene anabwera kunyumba ya Mulungu woona ku Yerusalemu, mʼmwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Salatiyeli, Yesuwa mwana wa Yehozadaki, abale awo onse, ansembe ndi Alevi ndiponso anthu ena onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo,+ anayamba kugwira ntchito. Anasankha Alevi oyambira zaka 20 kupita mʼtsogolo kuti akhale oyangʼanira ntchito yapanyumba ya Yehova.  Choncho Yesuwa, ana ake ndi abale ake, Kadimiyeli ndi ana ake, ndi ana a Yuda,* ananyamuka mogwirizana kuti akayangʼanire anthu ogwira ntchito mʼnyumba ya Mulungu woona. Panalinso ana a Henadadi,+ ana awo ndi abale awo, omwe anali Alevi. 10  Anthu amene ankamanga nyumbayo anamaliza kumanga maziko a kachisi wa Yehova.+ Atatero, ansembe ovala zovala zaunsembe omwe ananyamula malipenga+ ndiponso Alevi, ana a Asafu omwe ananyamula zinganga, anaimirira kuti atamande Yehova motsatira dongosolo limene Davide mfumu ya Isiraeli anakhazikitsa.+ 11  Iwo anayamba kuimba+ potamanda ndi kuyamika Yehova kuti, “iye ndi wabwino, chikondi chokhulupirika chimene amachisonyeza kwa Isiraeli chidzakhalapo mpaka kalekale.”+ Kenako anthu onse anafuula kwambiri potamanda Yehova chifukwa cha kumangidwa kwa maziko a nyumba ya Yehova. 12  Ansembe, Alevi ambiri ndi atsogoleri a nyumba za makolo awo, omwe anali amuna achikulire amene anaona nyumba yoyambirira,+ ankalira mokweza ataona maziko a nyumbayo pomwe ena ambiri ankafuula mosangalala.+ 13  Anthu ankalephera kusiyanitsa phokoso la chisangalalo ndi la kulira, chifukwa anthu osangalalawo ankafuula kwambiri, ndipo phokoso lawo linkamveka kutali kwambiri.

Mawu a M'munsi

Akutchulidwa kuti Hodaviya pa Eza 2:40 ndipo pa Ne 7:43 akutchedwa Hodeva.