Ezara 9:1-15

  • Aisiraeli anakwatira akazi a mitundu ina (1-4)

  • Pemphero la Ezara lovomereza machimo (5-15)

9  Zimenezi zitangotha, akalonga anabwera kwa ine nʼkundiuza kuti: “Aisiraeli, ansembe ndiponso Alevi sanadzipatule kwa anthu a mitundu ina komanso ku zonyansa za mitunduyo.+ Anthu ake ndi Akanani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aiguputo+ ndi Aamori.+  Iwo atenga ena mwa ana aakazi a mitundu inayo kuti akhale akazi awo ndi akazi a ana awo aamuna.+ Anthuwa, omwe ndi ana* opatulika,+ asakanikirana ndi anthu a mitundu ina.+ Akalonga komanso atsogoleri ndi amene ali patsogolo kuchita zosakhulupirikazi.”  Nditangomva nkhaniyi, ndinangʼamba zovala zanga nʼkuzula tsitsi langa ndi ndevu zanga, ndipo ndinakhala pansi nditakhumudwa kwambiri.  Aliyense amene ankalemekeza mawu a Mulungu wa Isiraeli anabwera nʼkundizungulira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu amene anachokera ku ukapolo. Pa nthawiyi nʼkuti ndili wokhumudwa kwambiri ndipo ndinakhala pansi mpaka nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo.+  Pa nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo,+ ndinaimirira mwamanyazi, zovala zanga zili zongʼambika ndipo ndinagwada nʼkukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga.  Kenako ndinanena kuti: “Inu Mulungu wanga, ndikuchita manyazi kuti ndikweze nkhope yanga kuyangʼana kwa inu Mulungu wanga, chifukwa zolakwa zathu zachuluka kupitirira pamutu pathu ndipo machimo athu aunjikana mpaka kumwamba.+  Kuyambira masiku a makolo athu mpaka lero machimo athu achuluka.+ Chifukwa cha zolakwa zathu, ifeyo, mafumu athu ndi ansembe athu, taperekedwa mʼmanja mwa mafumu a mayiko ena, taphedwa ndi lupanga,+ tatengedwa kupita ku ukapolo,+ talandidwa katundu+ komanso takhala amanyazi ngati mmene tilili lero.+  Koma kwa nthawi yochepa, Yehova Mulungu wathu watikomera mtima polola anthu ena kuti apulumuke ndipo watipatsa malo otetezeka* mʼmalo ake oyera+ kuti maso athu awale. Mulungu wathu watitsitsimula pangʼono mu ukapolo wathu.  Ngakhale kuti ndife akapolo,+ Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathuwo, koma watisonyeza chikondi chokhulupirika pamaso pa mafumu a ku Perisiya.+ Wachita zimenezi kuti atitsitsimutse nʼcholinga choti tikamangenso nyumba ya Mulungu wathu+ komanso tikakonze malo ozungulira nyumbayo amene anawonongedwa, ndiponso kuti tikhale mu Yuda ndi mu Yerusalemu ngati kuti tili mumpanda wamiyala.* 10  Ndiyeno tinganene chiyani inu Mulungu wathu pambuyo pa zimene zachitikazi? Popeza tasiya malamulo anu 11  amene munatilamula kudzera mwa atumiki anu aneneri, akuti, ‘Dziko limene mukukalitenga kuti likhale lanu ndi lodetsedwa chifukwa anthu ake ndi odetsedwa ndi zonyansa zawo zimene adzaza nazo dziko lonselo.+ 12  Choncho musakapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna, kapena kutenga ana awo aakazi nʼkuwapereka kwa ana anu aamuna.+ Musakalole kuti akhale pamtendere ndiponso kuti atukuke.+ Mukachite zimenezi kuti mukakhale amphamvu, mukadye zabwino zamʼdzikolo ndiponso kuti mukalitenge kuti likhale la ana anu mpaka kalekale.’ 13  Pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha zochita zathu zoipa ndi machimo athu ochuluka, ndipo inu Mulungu wathu simunatilange mogwirizana ndi kulakwa kwathu+ komanso mwalola kuti enafe tipulumuke,+ 14  kodi zoona tiphwanyenso malamulo anu kachiwiri pokwatirana ndi anthu a mitundu ina omwe amachita zonyansawa?+ Kodi tikatero simutikwiyira koopsa nʼkupezeka kuti sipanatsalenso wina wopulumuka? 15  Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli ndinu wolungama+ chifukwa ife tidakali ndi moyo mpaka lero. Taima pamaso panu mʼmachimo athu, ngakhale kuti nʼzosatheka kuima pamaso panu chifukwa cha zimenezi.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhomo.”
Kapena kuti, “mumpanda wachitetezo.”