Ezekieli 1:1-28
1 Mʼchaka cha 30, mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 5 la mweziwo, pamene ndinali pakati pa anthu amene anali ku ukapolo+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara,+ kumwamba kunatseguka ndipo ndinayamba kuona masomphenya a Mulungu.
2 Pa tsiku la 5 la mweziwo, mʼchaka cha 5 kuchokera pamene Mfumu Yehoyakini anatengedwa ukapolo,+
3 Yehova analankhula ndi Ezekieli,* mwana wa wansembe Buzi, pamene anali mʼdziko la Akasidi+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Kumeneko mphamvu za Yehova zinayamba kugwira ntchito pa iye.*+
4 Ndinaona mphepo yamkuntho+ ikuchokera kumpoto. Ndinaonanso mtambo waukulu komanso moto walawilawi*+ utazunguliridwa ndi kuwala. Pakati pa motowo panali chinachake chooneka ngati siliva wosakanikirana ndi golide.+
5 Pakati pa motowo panali zinazake zooneka ngati angelo 4,*+ ndipo mngelo aliyense ankaoneka ngati munthu.
6 Mngelo aliyense anali ndi nkhope 4 komanso mapiko 4.+
7 Mapazi a angelowo anali owongoka ndipo anali ooneka ngati mapazi a mwana wa ngʼombe. Mapaziwo ankawala ngati kopa wopukutidwa bwino.+
8 Pansi pa mapiko 4 a angelowo panali manja a munthu ndipo manjawo anali mbali zonse 4. Angelowo anali ndi nkhope ndiponso mapiko.
9 Mapiko a angelowo ankagundana. Angelowo sankatembenuka akamayenda, mngelo aliyense ankangopita kutsogolo.+
10 Nkhope za angelowo zinkaoneka chonchi: Mngelo aliyense pa angelo 4 amenewo anali ndi nkhope ya munthu, nkhope ya mkango+ mbali yakumanja ndiponso nkhope ya ngʼombe+ yamphongo mbali yakumanzere. Mngelo aliyense pa angelo 4 amenewo analinso ndi nkhope+ ya chiwombankhanga.+
11 Umu ndi mmene nkhope zawo zinalili. Mapiko awo anali otambasukira mʼmwamba. Mngelo aliyense anali ndi mapiko awiri ogundana, ndipo mapiko ena awiri ankaphimba matupi awo.+
12 Mngelo aliyense ankapita kutsogolo, ankapita kulikonse kumene mzimu ukufuna kuti apite.+ Angelowo sankatembenuka akamayenda.
13 Angelowo ankaoneka ngati makala oyaka moto. Pakati pa angelowo panali zinazake zooneka ngati miyuni ya moto wowala imene inkayenda kuchokera kwa mngelo wina kupita kwa mngelo wina ndipo mʼmotowo munkatuluka mphezi.+
14 Angelowo akapita kwinakwake nʼkubwerako, mayendedwe awo ankaoneka ngati mphezi.
15 Pamene ndinkayangʼana angelowo, ndinangoona wilo limodzi lili pansi pambali pa mngelo wankhope 4 aliyense.+
16 Mawilowo ankawala ngati mwala wa kulusolito, ndipo mawilo 4 onsewo ankaoneka mofanana. Anapangidwa mooneka ngati wilo lina lili pakati pa linzake.*
17 Mawilowo ankalowera kumbali iliyonse pambali zonse 4 ndipo sankafunika kuchita kukhota akamayenda.
18 Malimu a mawilowo anali aatali kwambiri moti anali ochititsa mantha. Malimu 4 onsewo anali ndi maso paliponse.+
19 Angelo aja akamayenda, nawonso mawilowo ankayenda nawo limodzi. Angelowo akamakwera mʼmwamba kuchokera pansi, mawilowonso ankakwera mʼmwamba.+
20 Angelowo ankapita kulikonse kumene mzimu ukufuna kuti apite, kulikonse kumene mzimuwo wapita. Mawilowo ankakwera mʼmwamba limodzi ndi angelowo chifukwa mzimu womwe unkatsogolera angelowo unkatsogoleranso mawilowo.
21 Angelowo akamayenda, mawilowonso ankayenda. Angelowo akaima, mawilowonso ankaima. Angelowo akakwera mʼmwamba kuchokera pansi, mawilowonso ankakwera mʼmwamba chifukwa mzimu womwe unkatsogolera angelowo unkatsogoleranso mawilowo.
22 Pamwamba pa mitu ya angelowo panali chinachake chooneka ngati thambo chimene chinayalidwa pamwamba pa mitu yawo. Chinthucho chinali chonyezimira ngati madzi oundana ochititsa chidwi.+
23 Mapiko a angelo omwe anali pansi pa chinthu chooneka ngati thambocho, anali otambasukira mʼmwamba ndipo phiko lililonse linkagundana ndi linzake. Mngelo aliyense anali ndi mapiko awiri amene ankaphimba mbali imodzi ya thupi lake, ndipo mapiko ena awiri ankaphimba mbali ina yotsalayo.
24 Phokoso la mapiko awo linkamveka ngati phokoso la madzi omwe akuthamanga ndiponso ngati phokoso la Wamphamvuyonse.+ Angelowo akamayenda, ankamveka ngati phokoso la gulu la asilikali. Akaima, ankatsitsa mapiko awo pansi.
25 Pamwamba pa chinthu chooneka ngati thambo chimene chinali pamwamba pa mitu yawo pankamveka mawu. (Akaima, ankatsitsa mapiko awo pansi.)
26 Pamwamba pa chinthu chooneka ngati thambo chimene chinali pamwamba pa mitu yawo, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro+ ndipo chinkaonekanso ngati mpando wachifumu.+ Pachinthu chooneka ngati mpando wachifumucho, panakhala winawake wooneka ngati munthu.+
27 Ndinaona chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide,+ chimene chinkaoneka ngati moto umene ukuyaka kuchokera pa chimene chinkaoneka ngati chiuno chake kupita mʼmwamba. Komanso kuchokera mʼchiuno chake kupita mʼmunsi, ndinaona chinachake chooneka ngati moto.+ Pamalo onse omuzungulira panali powala
28 ngati utawaleza+ umene ukuoneka mumtambo pa tsiku la mvula. Umu ndi mmene kuwala kozungulira pamalopo kunkaonekera. Kunkaoneka ngati ulemerero wa Yehova.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi. Kenako ndinayamba kumva mawu a winawake akulankhula.