Ezekieli 12:1-28

  • Zinthu zimene Ezekieli anachita polosera kuti anthu adzatengedwa kupita ku ukapolo (1-20)

    • Katundu wopita naye ku ukapolo (1-7)

    • Mtsogoleri adzachoka kuli mdima (8-16)

    • Adzadya chakudya ali ndi nkhawa ndipo adzamwa madzi ali ndi mantha aakulu (17-20)

  • Mawu achinyengo sadzakwaniritsidwa (21-28)

    • “Palibe mawu aliwonse omwe ndalankhula amene sadzachitika pa nthawi yake” (28)

12  Yehova analankhulanso nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu opanduka. Maso ali nawo koma saona, makutu ali nawo koma samva+ chifukwa ndi anthu opanduka.+  Koma iweyo mwana wa munthu, longedza katundu wako woti upite naye ku ukapolo. Ndiyeno upite ku ukapolo masana anthuwo akuona. Uchoke kwanu kupita ku ukapolo kumalo ena, iwo akuona. Mwina azindikira tanthauzo lake ngakhale kuti iwo ndi anthu opanduka.  Masana iwo akuona, utulutse katundu wako amene walongedza kuti upite naye ku ukapolo. Ndiyeno madzulo iwo akuona, unyamuke ngati munthu amene watengedwa kupita ku ukapolo.+  Ubowole khoma iwo akuona nʼkutulutsirapo katundu wako.+  Unyamule katunduyo paphewa iwo akuona ndipo umutulutse kuli mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone pansi chifukwa ndakuika kuti ukhale chizindikiro ku mtundu wa Isiraeli.”+  Ine ndinachita zonse zomwe anandilamula. Masana ndinatulutsa katundu wanga ngati katundu wopita naye ku ukapolo ndipo madzulo ndinabowola khoma ndi manja. Kutagwa mdima, ndinatulutsa katundu wanga ndipo ndinamunyamula paphewa iwo akuona.  Mʼmawa Yehova analankhulanso nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu opanduka a nyumba ya Isiraeli sanakufunse kuti, ‘Kodi ukuchita chiyani?’ 10  Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Uthenga uwu ndi wokhudza mtsogoleri+ amene ali mu Yerusalemu ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli amene ali mumzindawu.”’ 11  Uwauze kuti, iweyo ndi chizindikiro chawo.+ Zimene iwe wachitazi ndi zimenenso zidzawachitikire iwowo. Iwo adzapita ku ukapolo, kudziko lina.+ 12  Mtsogoleri amene ali pakati pawo adzanyamula katundu wake paphewa nʼkuchoka kuli mdima. Adzabowola khoma nʼkutulutsirapo katundu wake.+ Iye adzaphimba nkhope kuti asaone pansi. 13  Ine ndidzamuponyera ukonde wanga ndipo iye adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Kenako ndidzamupititsa ku Babulo, kudziko la Akasidi. Koma iye sadzaliona dzikolo ndipo adzafera komweko.+ 14  Anthu onse amene amuzungulira, amene amamuthandiza ndiponso asilikali ake, ndidzawabalalitsira kumbali zonse+ ndipo ndidzasolola lupanga kuti ndiwathamangitse.+ 15  Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova ndikadzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndi kumayiko ena. 16  Koma ndidzapulumutsa anthu ochepa pakati pawo kuti asaphedwe ndi lupanga, njala komanso mliri. Ndidzachita zimenezi kuti akafotokoze pakati pa anthu amitundu ina kumene adzapite zokhudza zinthu zonse zonyansa zimene ankachita ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.” 17  Ndiyeno Yehova analankhulanso nane kuti: 18  “Iwe mwana wa munthu, idya chakudya chako ukunjenjemera ndipo umwe madzi uli ndi mantha ndiponso nkhawa.+ 19  Anthu amʼdzikoli uwauze kuti, ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa anthu amene akukhala mu Yerusalemu, mʼdziko la Isiraeli: “Iwo adzadya chakudya chawo ali ndi nkhawa ndipo adzamwa madzi ali ndi mantha aakulu. Izi zidzachitika chifukwa dziko lawo lidzakhala bwinja lokhalokha+ chifukwa cha zinthu zachiwawa zimene anthu onse amene akukhala mmenemo akuchita.+ 20  Mizinda imene mukukhala anthu idzawonongedwa ndipo dzikolo lidzangokhala bwinja lokhalokha.+ Inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+ 21  Yehova analankhulanso nane kuti: 22  “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene anthu amʼdziko la Isiraeli mukunena wakuti, ‘Masiku akupita koma palibe masomphenya amene akwaniritsidwa,’+ umatanthauza chiyani? 23  Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzathetsa mwambi umenewu ndipo sadzaunenanso ngati mwambi mu Isiraeli.”’ Komano uwauze kuti, ‘Masiku ayandikira+ ndipo masomphenya onse adzakwaniritsidwa.’ 24  Chifukwa mʼnyumba ya Isiraeli simudzakhalanso masomphenya abodza kapena kulosera kwachiphamaso.*+ 25  ‘“Chifukwa ine Yehova ndidzalankhula ndipo mawu aliwonse amene ndidzalankhule adzachitikadi popanda kuzengereza.+ Mʼmasiku anu,+ inu a mʼnyumba yopanduka, ine ndidzanena mawu nʼkuwakwaniritsa,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’” 26  Yehova analankhulanso nane kuti: 27  “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Isiraeli akunena kuti, ‘Masomphenya amene ukuona adzachitika kutsogolo ndipo ukulosera zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo kwambiri.’+ 28  Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Palibe mawu aliwonse omwe ndalankhula amene sadzachitika pa nthawi yake. Zonse zimene ndanena zidzachitika,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kwachinyengo.”