Ezekieli 13:1-23

  • Anadzudzula aneneri abodza (1-16)

    • Makoma opakidwa laimu adzagwa (10-12)

  • Anadzudzula aneneri aakazi (17-23)

13  Yehova anandiuzanso kuti: 2  “Iwe mwana wa munthu, losera zokhudza aneneri a mu Isiraeli+ ndipo anthu amene akulosera zamʼmutu mwawo+ uwauze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova. 3  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka kwa aneneri opusa, amene akungolosera zamʼmutu mwawo pamene sanaone chilichonse.+ 4  Iwe Isiraeli, aneneri ako akhala ngati nkhandwe zamʼmabwinja. 5  Simudzapita mʼmalo ogumuka a mipanda yamiyala kuti mukamangirenso nyumba ya Isiraeli+ malo amene anagumukawo, nʼcholinga choti Aisiraeli adzapulumuke pa nkhondo pa tsiku la Yehova.”+ 6  “Iwo aona masomphenya abodza ndipo alosera zonama. Akunena kuti, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene Yehova sanawatume, ndipo akuyembekeza kuti zimene anenazo zichitika.+ 7  Kodi masomphenya amene mwaonawa si abodza ndipo zimene mwaloserazi si zonama pamene mukunena kuti, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene ine sindinanene chilichonse?”’ 8  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Chifukwa choti mwalankhula zabodza ndipo masomphenya anu ndi onama, ine ndithana nanu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+ 9  Dzanja langa likulimbana ndi aneneri amene masomphenya awo ndi abodza ndiponso amene akulosera zonama.+ Iwo sadzakhala mʼgulu la anthu amene ndimawakonda ndipo sadzalembedwa mʼbuku la mayina a anthu a nyumba ya Isiraeli. Komanso sadzabwerera kudziko la Isiraeli ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 10  Zonsezi zidzachitika chifukwa chakuti iwo asocheretsa anthu anga ponena kuti, “Tili pa mtendere!” koma palibe mtendere.+ Munthu akamanga khoma lachipinda losalimba, iwo akumalipaka laimu.’*+ 11  Uza anthu amene akupaka laimuwo kuti khomalo lidzagwa. Kudzagwa mvula yamphamvu, kudzagwanso matalala akuluakulu* ndipo mphepo yamkuntho idzagwetsa khomalo.+ 12  Ndiyeno khomalo likadzagwa, anthu adzakufunsani kuti, ‘Kodi laimu amene munapaka uja ali kuti?’+ 13  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzatumiza mphepo yamkuntho yamphamvu komanso mvula yambiri posonyeza mkwiyo wanga. Ndidzatumiza matalala akuluakulu kuti awononge khomalo chifukwa ndakwiya kwambiri. 14  Khoma limene mwalipaka laimulo, ndidzaligwetsa pansi ndipo maziko ake adzaonekera. Mzindawo ukamadzawonongedwa, inuyo mudzafera momwemo. Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova. 15  Ndikadzasonyeza mkwiyo wanga wonse pakhomalo ndiponso pa anthu amene analipaka laimuwo, ndidzakuuzani kuti: “Khoma lija kulibe komanso anthu amene analipaka laimu aja kulibenso.+ 16  Aneneri a mu Isiraeli adzakhala atawonongedwa. Aneneri amenewa ndi omwe akulosera zokhudza Yerusalemu nʼkumaona masomphenya oti mumzindawo muli mtendere, pamene mulibe mtendere,”’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 17  Koma iwe mwana wa munthu, yangʼana ana aakazi a anthu a mtundu wako, amene akulosera zamʼmutu mwawo ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire. 18  Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka akazi amene akusoka zinthu zovala mʼmikono* yonse ndi kupanga nsalu zophimba kumutu za mitu ya masaizi osiyanasiyana nʼcholinga choti akole anthuwo mumsampha nʼkuwapha. Kodi mukusaka miyoyo ya anthu anga nʼkumayesetsa kuti mupulumutse miyoyo yanu? 19  Inu mukundinyozetsa pamaso pa anthu anga chifukwa cha balere wongodzaza mʼmanja ndi nyenyeswa za mkate.+ Inu mukupha anthu amene sakuyenera kufa, ndipo mukusiya anthu amene sakuyenera kukhala ndi moyo. Mukuchita zimenezi ponamiza anthu anga amene akumvetsera mabodza anuwo.”’+ 20  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Akazi inu, ine ndikudana ndi zinthu zanu zovala mʼmikono, zimene mukuzigwiritsa ntchito potchera anthu msampha ngati kuti ndi mbalame. Ndizichotsa mʼmikono mwanu nʼkumasula anthu amene mwawatchera msampha ngati mbalame. 21  Ndingʼamba nsalu zanu zophimba kumutu ndi kulanditsa anthu anga mʼmanja mwanu. Iwo sadzakhalanso ngati zinthu zoti muzidzazisaka nʼkuzigwira ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 22  Inu mwakhumudwitsa munthu wolungama chifukwa cha chinyengo chanu,+ pamene ineyo sindinafune kuti azivutika.* Ndipo mwalimbitsa manja a munthu woipa+ kuti asasiye njira zake zoipazo. Chifukwa cha zimenezi iye sadzapitiriza kukhala ndi moyo.+ 23  Choncho akazi inu simudzaonanso masomphenya abodza ndipo simudzaloseranso zamʼtsogolo.+ Ine ndidzapulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

Mawu a M'munsi

Iwo ankachita zimenezi kuti khomalo lizioneka ngati lolimba.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo inu matalala akuluakulu, mudzagwanso.”
Kutanthauza zithumwa zovala mʼmanja kapena mʼzigongono.
Kapena kuti, “azimva ululu.”