Ezekieli 15:1-8

  • Yerusalemu ndi mtengo wa mpesa wopanda ntchito (1-8)

15  Yehova analankhulanso nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wa mpesa umasiyana bwanji ndi mitengo ina yonse kapena nthambi ya mitengo yamʼnkhalango?  Kodi anthu amadula nthambi yake kuti ikhale mtengo wogwiritsa ntchito inayake? Kapena kodi angatenge kamtengo kake nʼkukakhomerera pakhoma kuti azikolowekapo ziwiya zosiyanasiyana?  Mtengowo umaponyedwa pamoto kuti ukhale nkhuni ndipo motowo umanyeketsa kutsinde ndi kunsonga kwake. Pakati pa mtengowo pamapsanso. Ndiye kodi ungagwire ntchito iliyonse?  Ngakhale pamene mtengowo unali wathunthu sukanagwiritsidwa ntchito iliyonse. Ndiye kuli bwanji ukapsa ndi moto nʼkunyeka, kodi ungagwirenso ntchito iliyonse?”  “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Mofanana ndi mtengo wa mpesa womwe uli pakati pa mitengo yamʼnkhalango, umene ndaupereka kuti ukhale nkhuni, ndidzachitanso chimodzimodzi ndi anthu amene akukhala mu Yerusalemu.+  Anthuwo ndawayangʼana mokwiya. Iwo athawa moto, koma moto wina udzawapsereza. Ndipo ndikadzawayangʼana mokwiya, mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+  Dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja+ chifukwa chakuti iwo achita zosakhulupirika,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi