Ezekieli 16:1-63

  • Mulungu ankakonda Yerusalemu (1-63)

    • Anamupeza ngati mwana wotayidwa patchire (1-7)

    • Mulungu anamukongoletsa nʼkupangana naye pangano la ukwati (8-14)

    • Anakhala wosakhulupirika (15-34)

    • Anapatsidwa chilango chifukwa anali mkazi wachigololo (35-43)

    • Anamuyerekezera ndi Samariya komanso Sodomu (44-58)

    • Mulungu anakumbukira pangano lake (59-63)

16  Yehova analankhulanso nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, uza Yerusalemu zinthu zake zonyansa zimene akuchita.+  Umuuze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akuuza iwe Yerusalemu kuti: “Iwe unachokera kudziko la Akanani ndipo unabadwira komweko. Bambo ako anali a Chiamori+ ndipo mayi ako anali Muhiti.+  Pa tsiku limene unabadwa, mchombo wako sunadulidwe. Sanakusambitse kuti ukhale woyera, sanakupake mchere ndipo sanakukulunge munsalu.  Palibe amene anakumvera chisoni kuti akuchitire chilichonse mwa zinthu zimenezi. Palibe amene anakuchitira chifundo. Mʼmalomwake anakutaya patchire chifukwa anthu anadana nawe pa tsiku limene unabadwa.  Ine ndikudutsa pafupi ndinakuona ukuponyaponya timiyendo tako mʼmwamba uli magazi okhaokha. Ndiyeno utagona pansi ndiponso uli ndi magazi okhaokha ndinakuuza kuti, ‘Ukhala ndi moyo!’ Ndithu ndinakuuza uli magazi okhaokha kuti, ‘Ukhala ndi moyo!’  Ndinakupangitsa kuti ukhale gulu lalikulu la anthu ngati mbewu zimene zaphuka mʼmunda. Unakula nʼkukhala mtsikana ndipo unkavala zodzikongoletsera zabwino kwambiri. Mabere ako anakula ndipo tsitsi lako linatalika, koma unali udakali wosavala ndiponso wamaliseche.”’  ‘Ndikudutsa pafupi ndinakuona ndipo ndinazindikira kuti wafika pamsinkhu woti utha kuyamba kukondana ndi munthu. Choncho ndinakuphimba ndi chovala changa+ ndipo ndinabisa maliseche ako. Ndinalumbira nʼkuchita nawe pangano ndipo unakhala wanga,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  ‘Komanso ndinakusambitsa ndipo ndinatsuka magazi ako nʼkukudzoza mafuta.+ 10  Kenako ndinakuveka chovala cha nsalu yopeta ndi nsapato za chikopa chabwino kwambiri.* Ndinakukulunga munsalu zabwino kwambiri nʼkukuveka zovala zamtengo wapatali. 11  Ndinakuvekanso zokongoletsera komanso ndinakuveka zibangili mʼmanja mwako ndi mkanda mʼkhosi mwako. 12  Ndinakuvekanso ndolo yapamphuno ndi ndolo zamʼmakutu ndiponso chisoti chokongola pamutu pako. 13  Unapitiriza kudzikongoletsa ndi zinthu zagolide ndi zasiliva. Zovala zako zinali za nsalu zabwino kwambiri, nsalu zamtengo wapatali komanso chovala cha nsalu yopeta. Unkadya ufa wosalala, uchi ndi mafuta ndipo unakhala wokongola kwambiri+ moti unali woyenera kukhala mfumukazi.* 14  Unatchuka* kwambiri pakati pa mitundu ya anthu+ chifukwa cha kukongola kwako. Zili choncho chifukwa kukongola kwako kunali kogometsa popeza ndinaika ulemerero wanga pa iwe,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 15  ‘Koma unayamba kudalira kukongola kwako+ ndipo unakhala hule chifukwa cha kutchuka kwako.+ Unayamba kuchita uhule mosadziletsa ndi munthu aliyense wodutsa mʼnjira+ ndipo unapereka kukongola kwako kwa anthu odutsawo. 16  Unatenga zovala zako zina za mitundu yosiyanasiyana nʼkukongoletsera malo okwezeka pamene unkachitirapo uhule.+ Zinthu zimene siziyenera kuchitika ndipo zisadzachitikenso. 17  Unatenganso zinthu zako zodzikongoletsera zagolide ndi zasiliva zimene ndinakupatsa ndipo unapangira zifaniziro za munthu wamwamuna nʼkumachita nazo uhule.+ 18  Unatenga zovala zako za nsalu yopeta nʼkuphimbira zifanizirozo ndipo unapereka mafuta anga ndi zonunkhiritsa zanga kwa zifanizirozo.+ 19  Komanso buledi amene ndinakupatsa kuti udye, wopangidwa ndi ufa wosalala, mafuta ndi uchi, unamuperekanso kwa zifanizirozo kuti zikhale kafungo kosangalatsa.*+ Izi ndi zimene zinachitikadi,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 20  ‘Unatenga ana ako aamuna ndi aakazi amene unandiberekera+ nʼkuwapereka nsembe kwa mafano.+ Kodi zochita zako zauhulezo sizinakukwanire? 21  Unapha ana anga ndipo unawapereka nsembe powaponya pamoto.+ 22  Pamene unkachita zinthu zako zonse zonyansa komanso zauhulezo, sunakumbukire zimene ndinakuchitira uli wakhanda pamene unali wamaliseche komanso wosavala, ukuponyaponya timiyendo tako mʼmwamba ndiponso uli magazi okhaokha. 23  Tsoka, tsoka kwa iwe chifukwa unachita zinthu zoipa zonsezi!’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 24  ‘Unamanga malo oti uzilambirirapo milungu yabodza ndipo unakonza malo okwera mʼbwalo lililonse la mzinda. 25  Unamanga malo ako okwerawo pamalo oonekera bwino kwambiri mumsewu uliwonse ndipo kukongola kwako unakusandutsa chinthu chonyansa podzipereka kwa munthu* aliyense wodutsa+ ndipo unachulukitsa zochita zako zauhulezo.+ 26  Unachita uhule ndi ana aamuna a Iguputo,+ anthu oyandikana nawo amene ali ndi chilakolako champhamvu chogonana,* ndipo unandikhumudwitsa ndi zochita zako zauhule zosawerengeka. 27  Tsopano ine nditambasula dzanja langa nʼkukulanga ndipo ndichepetsa chakudya chimene ndimakupatsa.+ Ndikupereka kwa akazi amene amadana nawe+ kuti achite nawe zimene akufuna. Ndikupereka kwa ana aakazi a Afilisiti, amene ankanyansidwa ndi khalidwe lako lonyansa.+ 28  Chifukwa chosakhutira, unachitanso uhule ndi ana aamuna a Asuri.+ Koma utachita uhule ndi amuna amenewa sunakhutirebe. 29  Choncho unawonjezera kuchita zauhule ndi dziko la anthu a malonda* ndiponso Akasidi.+ Koma ngakhale unachita zimenezo sunakhutirebe. 30  Mtima wako unali wofooka kwambiri pamene unkachita zinthu zonsezi.* Wakhala ukuchita zinthu ngati hule lopanda manyazi!’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 31  ‘Koma pamene unamanga malo oti uzilambirirapo milungu yabodza, pamalo oonekera bwino kwambiri mumsewu uliwonse komanso kukonza malo okwera mʼbwalo lililonse la mzinda, sunali ngati hule chifukwa unkakana kulipidwa. 32  Ndiwe mkazi wachigololo amene ukukonda amuna achilendo mʼmalo mwa mwamuna wako.+ 33  Anthu amapereka mphatso kwa mahule onse,+ koma iweyo ndi amene wapereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse.+ Umawapatsa ziphuphu kuti abwere kwa iwe kuchokera kumalo onse ozungulira kuti adzachite nawe zauhule.+ 34  Iweyo umachita zosiyana ndi akazi ena amene amachita uhule. Palibe amene amachita uhule ngati mmene iwe umachitira. Iweyo ndi amene umapereka malipiro kwa amuna koma iwowo sakulipira. Zimene umachita nʼzosiyana ndi zimene mahule ena amachita.’ 35  Choncho hule iwe,+ imva mawu a Yehova. 36  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa wasonyeza chilakolako mopitirira muyezo ndipo maliseche ako aonekera pamene umachita zauhule ndi zibwenzi zako ndiponso mafano ako onse onyansa,*+ amene unafika powapatsa nsembe za magazi a ana ako,+ 37  ine ndikusonkhanitsa pamodzi zibwenzi zako zonse zimene unkazisangalatsa, onse amene unkawakonda limodzi ndi onse amene unkadana nawo. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumadera onse ozungulira kuti akuukire ndipo ndidzakuvula kuti aone maliseche ako, moti adzakuona uli mbulanda.+ 38  Ndidzakupatsa chiweruzo chimene chimayenera kuperekedwa kwa akazi achigololo+ ndi kwa akazi okhetsa magazi+ ndipo magazi ako adzakhetsedwa mokwiya komanso mwansanje.+ 39  Ndidzakupereka mʼmanja mwa anthu okuukira ndipo iwo adzagwetsa malo ako olambirirako milungu yabodza ndi malo ako okwera.+ Iwo adzakuvula zovala+ ndipo adzatenga zinthu zako zodzikongoletsera zamtengo wapatali+ nʼkukusiya wosavala komanso wamaliseche. 40  Adzakubweretsera chigulu cha anthu+ kuti chikuukire. Iwo adzakugenda ndi miyala+ ndipo adzakupha ndi malupanga awo.+ 41  Iwo adzawotcha nyumba zako ndi moto+ ndipo adzakulanga pamaso pa akazi ambiri. Ndidzathetsa uhule wako+ ndipo udzasiya kupereka malipiro. 42  Mkwiyo wanga ndidzauthetsera pa iwe+ moti sindidzakukwiyiranso.+ Ndidzangokhala osachita kalikonse ndipo sindidzakhalanso wokwiya.’ 43  ‘Chifukwa sunakumbukire zimene ndinakuchitira uli wakhanda+ ndipo wandikwiyitsa pochita zinthu zonsezi, tsopano ndikubwezera mogwirizana ndi zochita zako. Ndipo sudzapitirizanso kuchita khalidwe lako lonyansa komanso zinthu zonse zonyansa zimene ukuchita,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 44  ‘Aliyense amene amanena miyambi adzakunenera mwambi wakuti, “Make mbuu, mwana mbuu!”+ 45  Iweyo uli ngati mayi ako, amene ankanyansidwa ndi mwamuna wawo komanso ana awo. Ulinso ngati azichemwali ako amene ankanyansidwa ndi amuna awo ndi ana awo. Mayi ako anali Muhiti ndipo bambo ako anali a Chiamori.+ 46  Mkulu wako ndi Samariya+ amene akukhala kumpoto kwako* limodzi ndi ana ake aakazi.*+ Ndipo mngʼono wako ndi Sodomu,+ amene akukhala kumʼmwera kwako* limodzi ndi ana ake aakazi.+ 47  Iwe sikuti unangoyenda mʼnjira zawo ndiponso sikuti unkangotsatira zinthu zawo zonyansa zimene ankachita basi, koma mʼkanthawi kochepa zochita zako zonse zinakhala zoipa kwambiri kuposa zimene iwowo ankachita.+ 48  Pali ine Mulungu wamoyo, mchemwali wako Sodomu ndi ana ake aakazi, sanachite zofanana ndi zimene iwe ndi ana ako aakazi mwachita,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 49  ‘Tamvera! Zolakwa za mchemwali wako Sodomu zinali izi: Iye ndi ana ake aakazi+ anali onyada,+ anali ndi chakudya chochuluka+ komanso ankakhala moyo wabata ndi wosatekeseka,+ koma sankathandiza anthu ovutika ndi osauka.+ 50  Iwo anapitiriza kudzikweza+ komanso kuchita zinthu zonyansa pamaso panga.+ Choncho ndinaona kuti nʼzoyenera kuti ndiwawononge.+ 51  Komanso Samariya+ sanachite machimo ofika ngakhale hafu ya machimo ako. Koma iwe unapitiriza kuchulukitsa zinthu zonyansa zimene unkachita kuposa abale ako, moti unachititsa kuti azichemwali ako aoneke ngati olungama chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene unkachita.+ 52  Tsopano iweyo ukuyenera kuchita manyazi chifukwa waikira kumbuyo makhalidwe a azichemwali ako. Iwowo ndi olungama kuposa iweyo chifukwa cha tchimo lako lochita zinthu zonyansa kwambiri kuposa zimene iwowo anachita. Choncho uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa chakuti wachititsa kuti azichemwali ako aoneke ngati olungama.’ 53  ‘Ine ndidzasonkhanitsa anthu awo amene anatengedwa kupita kudziko lina. Ndidzasonkhanitsa anthu a ku Sodomu ndi ana ake aakazi amene anagwidwa komanso anthu a ku Samariya ndi ana ake aakazi amene anagwidwa. Posonkhanitsa anthu amenewa ndidzasonkhanitsanso anthu ako amene anatengedwa kupita ku dziko lina,+ 54  kuti udzachite manyazi. Iwe udzachita manyazi chifukwa cha zimene wachita powatonthoza. 55  Azichemwali ako, omwe ndi Sodomu ndi ana ake aakazi ndiponso Samariya ndi ana ake aakazi, adzakhalanso ngati mmene analili kale. Komanso iweyo ndi ana ako aakazi mudzakhalanso ngati mmene munalili kale.+ 56  Mchemwali wako Sodomu sunkamuona kuti ndi woyenera kumutchula mʼmasiku amene unkanyada, 57  zoipa zako zisanaonekere.+ Koma pano ana aakazi a Siriya ndi anthu oyandikana naye akukunyoza komanso ana aakazi a Afilisiti+ ndi onse amene akuzungulira akukuchitira zachipongwe. 58  Udzakumana ndi zotsatira za khalidwe lako lonyansa ndiponso zinthu zonyansa zimene ukuchita,’ akutero Yehova. 59  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Tsopano ndikulanga mogwirizana ndi zochita zako,+ chifukwa unanyoza lumbiro pophwanya pangano langa.+ 60  Koma ine ndidzakumbukira pangano limene ndinapangana nawe uli wakhanda ndipo ndidzachita nawe pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale.+ 61  Udzakumbukira khalidwe lako ndipo udzachita manyazi+ ukadzalandira azichemwali ako omwe ndi akulu ako komanso angʼono ako. Ndidzawapereka kwa iwe kuti akhale ana ako aakazi, koma osati chifukwa cha pangano limene ndinachita ndi iwe. 62  Ineyo ndidzachita pangano ndi iwe ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova. 63  Kenako udzakumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri moti sudzatha kutsegula pakamwa pako chifukwa cha manyaziwo,+ ndikadzaphimba machimo ako ngakhale kuti unachita zonsezi,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “chikopa cha katumbu.”
Kapena kuti, “kukhala wolamulira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzina lako linatchuka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pokhanyulira munthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu oyandikana nawo a ziwalo zikuluzikulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dziko la Kanani.”
Mabaibulo ena amati, “Iweyo wandikwiyitsa koopsa chifukwa cha zonse zimene wakhala ukuchitazi.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanja kwako.”
Nʼkutheka kuti apa akunena za matauni ozungulira.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanzere kwako.”