Ezekieli 17:1-24

  • Fanizo la ziwombankhanga ziwiri ndi mtengo wa mpesa (1-21)

  • Nsonga yanthete idzakhala mtengo waukulu wa mkungudza (22-24)

17  Yehova analankhulanso nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, nena mawu ophiphiritsa komanso mwambi wokhudza nyumba ya Isiraeli.+  Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ku Lebanoni+ kunabwera chiwombankhanga chachikulu+ cha mapiko akuluakulu komanso ataliatali. Chiwombankhangacho chinali ndi nthenga zambiri zamitundu yosiyanasiyana. Chitafika kumeneko, chinathyola nsonga ya mtengo wa mkungudza.+  Chiwombankhangacho chinathyola nsonga yapamwamba penipeni pa nthambi za mtengowo nʼkupita nayo kudziko la anthu ochita malonda.* Kumeneko chinakadzala nsonga ya mkungudzayo mumzinda umene munali anthu ochita malonda.+  Kenako chinatenga mbewu imodzi mwa mbewu zamʼdzikomo+ nʼkuidzala mʼmunda wachonde. Chinadzala mbewuyo mʼmphepete mwa madzi ambiri kuti ikule ngati mtengo wa msondodzi.  Mbewuyo inamera nʼkukhala mtengo wa mpesa+ waufupi wamasamba ambiri. Nthambi za mtengowo sizinkakulira mʼmbali ndipo mizu yake inali pansi pa nthambizo. Choncho mbewuyo inakhala mtengo wa mpesa ndipo inaphuka nʼkuchita nthambi.+  Kenako kunabwera chiwombankhanga china chachikulu+ chamapiko akuluakulu komanso nthenga zikuluzikulu.+ Ndiyeno mwamsanga, mtengo wa mpesawo unatambasula mizu yake kupita kumene kunali chiwombankhangacho kutali ndi malo amene unadzalidwa. Mtengo wa mpesawo unatambasula nthambi zake kukafika pamene panali chiwombankhangacho kuti chiuthirire.+  Koma mtengowo anali ataudzala kale mʼmunda wabwino pafupi ndi madzi ambiri, kuti uchite nthambi, ubereke zipatso nʼkukhala mtengo waukulu wa mpesa.”’+  Ndiyeno unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi mtengo umenewu zinthu zidzauyendera bwino? Kodi munthu wina sadzadula mizu yake+ nʼkuchititsa kuti zipatso zake ziwole komanso kuchititsa kuti mphukira zake zinyale?+ Mtengowo udzauma kwambiri moti sipadzachita kufunika dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti auzule ndi mizu yomwe. 10  Ngakhale kuti mtengowo anautenga pamalo ena nʼkukaudzala pamalo ena, kodi zinthu zidzauyendera bwino? Kodi sudzaumiratu ukadzawombedwa ndi mphepo yakumʼmawa? Mtengowo udzauma pamalo amene unadzalidwapo.”’” 11  Yehova analankhulanso nane kuti: 12  “Chonde, uza anthu opandukawo kuti, ‘Kodi simukuzindikira tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Auze kuti, ‘Mfumu ya Babulo inabwera ku Yerusalemu nʼkudzatenga mfumu ndi akalonga amumzindawo nʼkupita nawo ku Babulo.+ 13  Kuwonjezera apo, inatenga mmodzi mwa ana* achifumu+ nʼkuchita naye pangano ndi kumulumbiritsa.+ Kenako mfumuyo inatenga anthu otchuka amʼdzikolo nʼkupita nawo kwawo+ 14  nʼcholinga choti ufumuwo ukhale waungʼono, usakhalenso wamphamvu, koma kuti ufumuwo udzapitirize kukhalapo ngati Aisiraeli atasunga pangano limene anachita.+ 15  Koma kenako mfumu ya Yuda inapandukira mfumu ya Babulo+ potumiza amithenga ku Iguputo kuti akatenge mahatchi+ ndi gulu lalikulu la asilikali.+ Kodi zinthu zidzaiyendera bwino? Kodi munthu amene akuchita zinthu zimenezi angapewe chilango? Kodi angaphwanye pangano nʼkupewabe chilango?’+ 16  ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, “Pali ine Mulungu wamoyo, munthu amene ananyoza lumbiro ndi kuphwanya pangano limene anachita ndi mfumu* imene inamulonga* ufumu, adzafera mʼdziko la Babulo, kumene mfumuyo imakhala.+ 17  Gulu lalikulu la asilikali komanso asilikali ambirimbiri a Farao sadzamuthandiza pankhondo,+ adani akadzamanga malo okwera omenyerapo nkhondo ndiponso mpanda womenyerapo nkhondo nʼcholinga chakuti aphe anthu ambiri. 18  Iye wanyoza lumbiro limenelo komanso waphwanya pangano. Ngakhale kuti analonjeza,* iye wachita zinthu zonsezi ndipo sadzapulumuka.”’ 19  ‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndidzamulanga chifukwa chonyoza lumbiro langa+ ndiponso chifukwa chophwanya pangano langa. 20  Ndidzamuponyera ukonde wanga ndipo adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Ndiyeno ndidzamubweretsa ku Babulo nʼkumuweruza chifukwa chondichitira zinthu mosakhulupirika.+ 21  Asilikali ake onse amene anathawa adzaphedwa ndi lupanga ndipo amene adzapulumuke adzabalalikira kumbali zonse.*+ Zikadzatero mudzadziwa kuti ine Yehova ndi amene ndanena zimenezi.”’+ 22  ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzathyola nsonga yapamwamba penipeni pa mtengo wa mkungudza+ nʼkuidzala. Ndidzabudula mphukira yanthete pamwamba pa nsonga zake+ ndipo ndidzaidzala pamwamba pa phiri lalitali kwambiri.+ 23  Ndidzaidzala pamwamba pa phiri lalitali la ku Isiraeli. Nthambi zake zidzakula ndipo udzabereka zipatso nʼkukhala mtengo waukulu wa mkungudza. Mbalame zamitundu yonse zizidzakhala pansi pa mtengowo ndi mumthunzi wa masamba ake. 24  Mitengo yonse yamʼthengo idzadziwa kuti ine Yehova ndatsitsa mtengo waukulu nʼkukweza mtengo wonyozeka.+ Idzadziwa kuti ndaumitsa mtengo wauwisi nʼkuchititsa maluwa mtengo umene unali wouma.+ Ine Yehova ndanena komanso kuchita zimenezi.”’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kudziko la Kanani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Ameneyu ndi Nebukadinezara.
Kutanthauza Zedekiya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anapereka dzanja lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumphepo zonse.”